< 1 Mbiri 9 >
1 Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli. Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.
2 Tsono anthu oyamba kukhala mʼmadera awo anali Aisraeli wamba, ansembe, Alevi ndi otumikira ku Nyumba ya Yehova.
3 Anthu a ku Yuda, Benjamini ndi Efereimu ndiponso Manase amene anakhala mu Yerusalemu anali awa:
4 Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi mwana wa Yuda.
5 A banja la Siloni: Asaya mwana wake woyamba pamodzi ndi ana ake.
6 A banja la Zera: Yeueli. Anthu ochokera ku Yuda analipo 690.
7 A fuko la Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuya;
8 Ibineya mwana wa Yerohamu; Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri; ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli mwana wa Ibiniya.
9 Anthu ochokera ku Benjamini monga analembedwera mwa mibado yawo, analipo 956. Anthu onsewa anali atsogoleri a mabanja awo.
10 Ansembe: Yedaya, Yehoyaribu; Yakini;
11 Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi, wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu;
12 Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya; ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yahizera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri.
13 Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja awo analipo 1,760. Anali anthu amphamvu ndi odziwa kutumikira mʼnyumba ya Mulungu.
14 Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa mʼbanja la Merari;
15 Bakibakara, Heresi, Galali ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu;
16 Obadiya mwana wa Semaya mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi ya Anetofati.
17 Alonda a pa makomo: Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani ndi abale awo. Mtsogoleri wawo anali Salumu.
18 Amenewa amakhala pa chipata cha mfumu kummawa mpaka lero lino. Alonda a gulu la Alevi anali awa:
19 Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova.
20 Masiku oyamba Finehasi mwana wa Eliezara anali woyangʼanira alonda apakhomo ndipo Yehova anali naye.
21 Zekariya mwana wa Meselemiya anali mlonda woyangʼanira pa chipata cha tenti ya msonkhano.
22 Onse amene anasankhidwa kukhala alonda pa khonde analipo 212. Iwo analembedwa mwa mibado yawo ku midzi yawo. Davide ndi mneneri Samueli ndiwo anawayika mʼmalo awo antchito chifukwa cha kukhulupirika kwawo.
23 Iwo ndi zidzukulu zawo anali oyangʼanira zipata za nyumba ya Yehova imene imatchedwa Tenti.
24 Alonda apakhomowa anali mbali zonse zinayi: kummawa, kumadzulo, kumpoto ndi kummwera.
25 Abale awo a ku midzi yawo amabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito yawo kwa masiku asanu ndi awiri.
26 Koma atsogoleri akuluakulu anayi a alonda, amene anali Alevi, anapatsidwa udindo woyangʼanira zipinda ndi chuma cha nyumba ya Mulungu.
27 Iwo amakhala usiku wonse atayima mozungulira Nyumba ya Mulungu, chifukwa anayenera kuyilondera. Ndipo anali ndi kiyi wotsekulira mmawa uliwonse.
28 Ena amayangʼanira zipangizo zimene amagwiritsa ntchito pa ntchito mʼNyumba ya Mulungu. Iwo amaziwerenga zikamalowetsedwa ndi potulutsidwa.
29 Ena anapatsidwa udindo wosamalira zipangizo ndi zinthu zina zonse za ku malo opatulika, pamodzi ndi ufa, vinyo, mafuta, lubani ndi zonunkhira.
30 Koma ansembe ena amasakaniza zonunkhirazo.
31 Mlevi wotchedwa Matitiya mwana woyamba wa Salumu wa mʼbanja la Kora, anapatsidwa udindo woyangʼanira zophikidwa mʼziwaya.
32 Abale ake ena a mʼbanja la Akohati amaphika buledi wa pa Sabata lililonse amene amayikidwa pa tebulo.
33 Atsogoleri a mabanja a Alevi, amene anali ndi luso loyimba, amakhala mʼzipinda za Nyumba ya Mulungu ndipo samagwira ntchito zina chifukwa ankatumikira usana ndi usiku.
34 Onsewa anali atsogoleri a mabanja a Alevi, akuluakulu monga analembedwera pa mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.
35 Yeiyeli abambo a Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni. Dzina la akazi awo linali Maaka,
36 ndipo mwana wawo woyamba kubadwa anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu,
37 Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti.
38 Mikiloti anabereka Simeamu. Iwonso ankakhala ndi abale awo ku Yerusalemu.
39 Neri anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.
40 Mwana wa Yonatani anali Meri-Baala, amene anabereka Mika.
41 Ana a Mika anali: Pitoni, Meleki, Tahireya ndi Ahazi.
42 Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimiri anabereka Moza.
43 Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Refaya, Eleasa ndi Azeli.
44 Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo mayina awo anali awa: Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Awa anali ana a Azeli.