< 1 Mbiri 7 >

1 Ana a Isakara anali awa: Tola, Puwa, Yasubu ndi Simironi ndipo onse analipo anayi.
以薩迦的兒子是陀拉、普瓦、雅述、伸崙,共四人。
2 Ana a Tola ndi awa: Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600.
陀拉的兒子是烏西、利法雅、耶勒、雅買、易伯散、示母利,都是陀拉的族長,是大能的勇士。到大衛年間,他們的人數共有二萬二千六百名。
3 Mwana wa Uzi anali Izirahiya. Ana a Izirahiya anali: Mikayeli, Obadiya, Yoweli ndi Isiya. Onse asanu anali atsogoleri a mabanja.
烏西的兒子是伊斯拉希;伊斯拉希的兒子是米迦勒、俄巴底亞、約珥、伊示雅,共五人,都是族長。
4 Monga mwa chiwerengero cha mabanja awo, panali anthu 36,000 odziwa kumenya nkhondo, pakuti iwo anali ndi akazi ndi ana ambiri.
他們所率領的,按着宗族出戰的軍隊,共有三萬六千人,因為他們的妻和子眾多。
5 Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo.
他們的族弟兄在以薩迦各族中都是大能的勇士,按着家譜計算共有八萬七千人。
6 Ana atatu a Benjamini anali awa: Bela, Bekeri ndi Yediaeli.
便雅憫的兒子是比拉、比結、耶疊,共三人。
7 Ana a Bela anali awa: Eziboni, Uzi, Uzieli, Yerimoti ndi Iri. Iwowa anali atsogoleri a mabanja awo ndipo onse pamodzi analipo asanu. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali anthu 22,034 odziwa kumenya nkhondo.
比拉的兒子是以斯本、烏西、烏薛、耶利摩、以利,共五人,都是族長,是大能的勇士。按着家譜計算,他們的子孫共有二萬二千零三十四人。
8 Ana a Bekeri anali awa: Zemira, Yowasi, Eliezara, Eliyoenai, Omiri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri.
比結的兒子是細米拉、約阿施、以利以謝、以利約乃、暗利、耶利摩、亞比雅、亞拿突、亞拉篾。這都是比結的兒子。
9 Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali atsogoleri a mabanja ndi anthu 20,200 odziwa kumenya nkhondo.
他們都是族長,是大能的勇士。按着家譜計算,他們的子孫共有二萬零二百人。
10 Mwana wa Yediaeli anali Bilihani. Ana a Bilihani anali awa: Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara.
耶疊的兒子是比勒罕;比勒罕的兒子是耶烏施、便雅憫、以忽、基拿拿、細坦、他施、亞希沙哈。
11 Ana onsewa a Yediaeli anali atsogoleri a mabanja. Analipo anthu 17,200 amene anali okonzeka kupita ku nkhondo.
這都是耶疊的兒子,都是族長,是大能的勇士;他們的子孫能上陣打仗的,共有一萬七千二百人。
12 Asupi ndi Ahupi anali zidzukulu za Iri, ndipo Ahusimu anali zidzukulu za Aheri.
還有以珥的兒子書品、戶品,並亞黑的兒子戶伸。
13 Ana a Nafutali anali awa: Yahazieli, Guni, Yezeri ndi Salumu, zidzukulu za Biliha.
拿弗他利的兒子是雅薛、沽尼、耶色、沙龍。這都是辟拉的子孫。
14 Ana a Manase anali awa: Asirieli ndi mwana amene anabereka kwa mzikazi wake wa ku Aramu. Mzikazi yemweyo anaberekanso Makiri abambo ake a Giliyadi.
瑪拿西的兒子亞斯列是他妾亞蘭人所生的,又生了基列之父瑪吉。
15 Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka. Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha.
瑪吉娶的妻是戶品、書品的妹子,名叫瑪迦。瑪拿西的次子名叫西羅非哈;西羅非哈但有幾個女兒。
16 Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Perezi. Mʼbale wake anamutcha Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rakemu.
瑪吉的妻瑪迦生了一個兒子,起名叫毗利施。毗利施的兄弟名叫示利施;示利施的兒子是烏蘭和利金。
17 Mwana wa Ulamu anali Bedani. Awa anali ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase.
烏蘭的兒子是比但。這都是基列的子孫。基列是瑪吉的兒子,瑪吉是瑪拿西的兒子。
18 Mlongo wake Hamoleketi anabereka Isihodi, Abiezeri ndi Mahila.
基列的妹子哈摩利吉生了伊施荷、亞比以謝、瑪拉。(
19 Ana a Semida anali: Ahiyani, Sekemu, Likihi ndi Aniyamu.
示米大的兒子是亞現、示劍、利克希、阿尼安。)
20 Ana a Efereimu anali awa: Sutela, Beredi, Tahati, Eliada, Tahati,
以法蓮的兒子是書提拉;書提拉的兒子是比列;比列的兒子是他哈;他哈的兒子是以拉大;以拉大的兒子是他哈;
21 Zabadi, Sutela. Ezeri ndi Eladi anaphedwa ndi anthu a ku Gati, pamene anabwera kudzalanda zoweta zawo.
他哈的兒子是撒拔;撒拔的兒子是書提拉。以法蓮又生以謝、以列;這二人因為下去奪取迦特人的牲畜,被本地的迦特人殺了。
22 Efereimu, abambo awo, anawalira masiku ambiri, ndipo abale ake anabwera kudzamutonthoza.
他們的父親以法蓮為他們悲哀了多日,他的弟兄都來安慰他。
23 Kenaka anagona ndi mkazi wake, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Beriya, chifukwa tsoka linagwera banja lake.
以法蓮與妻同房,他妻就懷孕生了一子,以法蓮因為家裏遭禍,就給這兒子起名叫比利亞。
24 Mwana wake wamkazi anali Seera, amene anamanga mzinda wa Beti-Horoni Wakumunsi, Wakumtunda kudzanso Uzeni-Seera.
他的女兒名叫舍伊拉,就是建築上伯‧和崙、下伯‧和崙與烏羨‧舍伊拉的。
25 Mwana wina wa Efereimu anali Refa amene zidzukulu zake zinali Resefu, Tela, Tahani,
比利亞的兒子是利法和利悉。利悉的兒子是他拉;他拉的兒子是他罕;
26 Ladani, Amihudi, Elisama,
他罕的兒子是拉但;拉但的兒子是亞米忽;亞米忽的兒子是以利沙瑪;
27 Nuni ndi Yoswa.
以利沙瑪的兒子是嫩;嫩的兒子是約書亞。
28 Malo amene ankakhala anali Beteli ndi midzi yozungulira, cha kummawa kunali Naarani, Gezeri ndi midzi yake ya kumadzulo ndi Sekemu ndi midzi yake mpaka ku Aya ndi midzi yake.
以法蓮人的地業和住處是伯特利與其村莊;東邊拿蘭,西邊基色與其村莊;示劍與其村莊,直到迦薩與其村莊;
29 Mʼmbali mwa malire a Manase munali Beti-Seani, Taanaki, Megido ndi Dori, pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Yosefe mwana wa Israeli zimakhala mʼmizinda imeneyi.
還有靠近瑪拿西人的境界,伯‧善與其村莊;他納與其村莊;米吉多與其村莊;多珥與其村莊。以色列兒子約瑟的子孫住在這些地方。
30 Ana a Aseri anali awa: Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya. Mlongo wawo anali Sera.
亞設的兒子是音拿、亦施瓦、亦施韋、比利亞,還有他們的妹子西拉。
31 Ana a Beriya anali awa: Heberi ndi Malikieli amene anabereka Birizaiti.
比利亞的兒子是希別、瑪結;瑪結是比撒威的父親。
32 Heberi anabereka Yafuleti, Someri, Hotamu ndi Suwa, mlongo wawo.
希別生雅弗勒、朔默、何坦,和他們的妹子書雅。
33 Ana a Yafuleti anali awa: Pasaki, Bimuhali ndi Asivati. Awa anali ana a Yafuleti.
雅弗勒的兒子是巴薩、賓哈、亞施法。這都是雅弗勒的兒子。
34 Ana a Someri anali awa: Ahi, Rohiga, Yehuba ndi Aramu.
朔默的兒子是亞希、羅迦、耶戶巴、亞蘭。
35 Ana a mʼbale wake Helemu anali awa: Zofa, Imuna, Selesi ndi Amali.
朔默兄弟希連的兒子是瑣法、音那、示利斯、亞抹。
36 Ana a Zofa anali awa: Suwa, Harineferi, Suwali, Beri, Imula,
瑣法的兒子是書亞、哈尼弗、書阿勒、比利、音拉、
37 Bezeri, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Bera.
比悉、河得、珊瑪、施沙、益蘭、比拉。
38 Ana a Yeteri anali awa: Yefune, Pisipa ndi Ara.
益帖的兒子是耶孚尼、毗斯巴、亞拉。
39 Ana a Ula anali awa: Ara, Hanieli ndi Riziya.
烏拉的兒子是亞拉、漢尼業、利寫。
40 Onsewa anali zidzukulu za Aseri, atsogoleri a mabanja, anthu omveka, ankhondo olimba mtima, ndi akuluakulu pakati pa atsogoleri anzawo. Chiwerengero cha anthu odziwa kumenya nkhondo chomwe chinalembedwa chinali 26,000.
這都是亞設的子孫,都是族長,是精壯大能的勇士,也是首領中的頭目,按着家譜計算,他們的子孫能出戰的共有二萬六千人。

< 1 Mbiri 7 >