< 1 Mbiri 6 >
1 Ana a Levi anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
Fils de Lévi: Gersom, Caath et Mérari.
2 Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
Fils de Caath: Amram, Isaar et Oziel.
3 Ana a Amramu anali awa: Aaroni, Mose ndi Miriamu. Ana a Aaroni anali awa: Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara
Fils d'Amram: Aaron, Moïse et Marie. — Fils d'Aaron: Nadab, Abiu, Eléazar et Ithamar. —
4 Eliezara anabereka Finehasi, Finehasi anabereka Abisuwa,
Eléazar engendra Phinées; Phinées engendra Abisué;
5 Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi.
Abisué engendra Bocci; Bocci engendra Ozi;
6 Uzi anabereka Zerahiya, Zerahiya anabereka Merayoti,
Ozi engendra Zaraïas; Zaraïas engendra Méraïoth;
7 Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi.
Méraïoth engendra Amarias; Amarias engendra Achitob;
8 Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Ahimaazi.
Achitob engendra Sadoc; Sadoc engendra Achimaas;
9 Ahimaazi anabereka Azariya, Azariya anabereka Yohanani,
Achimaas engendra Azarias; Azarias engendra Johanan;
10 Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),
Johanan engendra Azarias: c'est lui qui exerça le sacerdoce dans la maison que Salomon bâtit à Jérusalem;
11 Azariya anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi,
Azarias engendra Amarias; Amarias engendra Achitob;
12 Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Salumu,
Achitob engendra Sadoc; Sadoc engendra Sellum;
13 Salumu anabereka Hilikiya, Hilikiya anabereka Azariya,
Sellum engendra Helcias; Helcias engendra Azarias;
14 Azariya anabereka Seraya, ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.
Azarias engendra Saraïas; Saraïas engendra Josédec.
15 Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.
Josédec partit pour l'exil quand Yahweh fil emmener en captivité Juda et Jérusalem par l'intermédiaire de Nabuchodonosor.
16 Ana a Levi anali awa: Geresomu, Kohati ndi Merari.
Fils de Lévi: Gersom, Caath et Mérari. —
17 Mayina a ana a Geresomu ndi awa: Libini ndi Simei.
Voici les noms des fils de Gersom: Lobni et Séméï. —
18 Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
Fils de Caath: Amram, Isaar, Hébron et Oziel. —
19 Ana a Merari anali awa: Mahili ndi Musi. Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:
Fils de Mérari: Moholi et Musi. Voici les familles de Lévi selon leurs pères:
20 Ana a Geresomu ndi awa: Libini, Yehati, Zima,
De Gersom: Lobni, son fils; Jahath, son fils; Zamma, son fils;
21 Yowa, Ido, Zera ndi Yeaterai.
Joah, son fils; Addo, son fils; Zara, son fils; Jethraï, son fils. —
22 Zidzukulu za Kohati ndi izi: Aminadabu, Kora, Asiri,
Fils de Caath: Aminadab, son fils; Coré, son fils; Asir, son fils;
23 Elikana, Ebiyasafu, Asiri,
Elcana, son fils; Abiasaph, son fils; Asir, son fils;
24 Tahati, Urieli, Uziya ndi Sauli.
Thahath, son fils; Uriel, son fils; Ozias, son fils; Saül, son fils.
25 Zidzukulu za Elikana ndi izi: Amasai, Ahimoti,
Fils d'Elcana: Amasaï et Achimoth;
26 Elikana, Zofai, Nahati,
Elcana, son fils; Sophaï, son fils; Nahath, son fils;
27 Eliabu, Yerohamu, Elikana ndi Samueli.
Eliab, son fils; Jéroham, son fils; Elcana, son fils.
28 Ana a Samueli ndi awa: Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya.
Fils de Samuel: le premier-né Vasséni, et Abia. —
29 Zidzukulu za Merari ndi izi: Mahili, Libini, Simei, Uza,
Fils de Mérari: Moholi; Lobni, son fils; Séméï, son fils; Oza, son fils;
30 Simea, Hagiya ndi Asaya.
Sammaa, son fils; Haggia, son fils; Asaïa, son fils.
31 Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo.
Voici ceux que David établit pour diriger le chant dans la maison de Yahweh, depuis que l'arche eut un lieu de repos:
32 Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.
ils remplirent les fonctions de chantres devant la Demeure de la tente de réunion, jusqu'à ce que Salomon eût bâti la maison de Yahweh à Jérusalem, et ils se tenaient à leur service selon leur règlement. —
33 Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa: Ochokera ku banja la Kohati: Hemani, katswiri woyimba, anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,
Voici ceux qui officiaient avec leurs fils: — D'entre les fils des Caathites: Héman, le chantre, fils de Joël, fils de Samuel,
34 mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Elieli, mwana wa Towa,
fils d'Elcana, fils de Jéroham, fils d'Eliel, fils de Thohu,
35 mwana wa Zufi, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,
fils de Suph, fils d'Elcana, fils de Mahath, fils d'Amasaï,
36 mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,
fils d'Elcana, fils de Joël, fils d'Azarias, fils de Sophonias,
37 mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,
fils de Thahath, fils d'Asir, fils d'Abiasaph, fils de Coré,
38 mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israeli;
fils d'Isaar, fils de Caath, fils de Lévi, fils d'Israël.
39 ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja: Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,
— Son frère Asaph, qui se tenait à sa droite: Asaph, fils de Barachias, fils de Samaa,
40 mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya, mwana wa Malikiya,
fils de Michaël, fils de Basaïas, fils de Melchias,
41 mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya,
fils d'Athanaï, fils de Zara, fils d'Adaïa,
42 mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana Simei,
fils d'Ethan, fils de Zamma, fils de Séméï,
43 mwana wa Yahati, mwana wa Geresomu, mwana wa Levi;
fils de Jeth, fils de Gersom, fils de Lévi.
44 ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere: Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki,
— Fils de Mérari, leurs frères, à la gauche: Ethan, fils de Cusi, fils d'Abdi, fils de Maloch,
45 mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
fils de Hasabias, fils d'Amasias, fils de Helcias,
46 mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri,
fils d'Amasaï, fils de Boni, fils de Somer,
47 mwana wa Mahili, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.
fils de Moholi, fils de Musi, fils de Mérari, fils de Lévi.
48 Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu.
Leurs frères, les lévites, étaient chargés de tout le service du tabernacle de la maison de Yahweh.
49 Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.
Mais Aaron et ses fils brûlaient les victimes sur l'autel des holocaustes et l'encens sur l'autel des parfums; ils avaient à remplir tout le ministère du saint des saints, et à faire l'expiation pour Israël, selon tout ce qu'avait ordonné Moïse, serviteur de Dieu.
50 Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa: Eliezara, Finehasi, Abisuwa,
Voici les fils d'Aaron: Eléazar, son fils; Phinées, son fils; Abisué, son fils;
Bocci, son fils; Ozi, son fils; Zaraïas, son fils;
52 Merayoti, Amariya, Ahitubi,
Méraïoth, son fils; Amarias, son fils; Achitob, son fils;
Sadoc, son fils; Achimaas, son fils.
54 Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo).
Voici leurs habitations, selon leurs enceintes, dans leurs territoires: — Aux fils d'Aaron, de la famille des Caathites, désignés les premiers par le sort,
55 Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
on donna Hébron, dans le pays de Juda, et les pâturages qui l'entourent;
56 Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune.
mais on donna le territoire de la ville et ses villages à Caleb, fils de Jéphoné.
57 Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa,
On donna donc aux fils d'Aaron la ville de refuge Hébron, Lobna et ses pâturages,
Jéther, Esthémo et ses pâturages, Hélon et ses pâturages, Dabir et ses pâturages,
59 Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
Asan et ses pâturages, Bethsémès et ses pâturages;
60 Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13.
de la tribu de Benjamin, Gabée et ses pâturages, Almath et ses pâturages, Anathoth et ses pâturages. Total de leurs villes: treize villes, d'après leurs familles.
61 Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase.
— Les autres fils de Caath eurent par le sort dix villes des familles de la tribu, de la demi-tribu de Manassé.
62 Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani.
Les fils de Gersom, d'après leurs familles, eurent treize villes de la tribu d'Issachar, de la tribu d'Aser, de la tribu de Nephthali et de la tribu de Manassé, en Basan.
63 Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
Les fils de Mérari, d'après leurs familles, eurent par le sort douze villes de la tribu de Ruben, de la tribu de Gad et de la tribu de Zabulon.
64 Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa.
Les enfants d'Israël donnèrent aux Lévites les villes et leurs pâturages.
65 Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina.
Ils donnèrent par le sort, de la tribu des enfants de Juda, de la tribu des enfants de Siméon et de la tribu des enfants de Benjamin, ces villes qu'ils désignèrent par leurs noms.
66 Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu.
Pour les autres familles des fils de Caath, les villes qui leur échurent furent de la tribu d'Ephraïm.
67 Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri,
On leur donna: la ville de refuge Sichem et ses pâturages, dans la montagne d'Ephraïm, Gazer et ses pâturages,
68 Yokineamu, Beti-Horoni,
Jecmaam et ses pâturages, Bethoron et ses pâturages,
69 Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira.
Hélon et ses pâturages, Geth-Remmon et ses pâturages;
70 Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati.
et de la demi-tribu de Manassé, Aner et ses pâturages, Balaam et ses pâturages: pour les familles des autres fils de Caath.
71 Ageresomu analandira malo awa: Kuchokera ku theka la fuko la Manase, analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;
On donna aux fils de Gersom: de la famille de la demi-tribu de Manassé, Gaulon en Basan et ses pâturages, Astharoth et ses pâturages;
72 Kuchokera ku fuko la Isakara analandira Kedesi, Daberati,
de la tribu d'Issachar, Cédès et ses pâturages, Dabéreth et ses pâturages,
73 Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
Ramoth et ses pâturages, Anem et ses pâturages;
74 kuchokera ku fuko la Aseri analandira Masala, Abidoni,
de la tribu d'Aser, Masal et ses pâturages, Abdon et ses pâturages,
75 Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
Hucac et ses pâturages, Rohob et ses pâturages;
76 ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.
et de la tribu de Nephthali, Cédès en Galilée et ses pâturages, Hamon et ses pâturages, et Cariathaïm et ses pâturages.
77 Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa: kuchokera ku fuko la Zebuloni, iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
On donna au reste des Lévites, aux fils de Mérari: de la tribu de Zabulon, Remmono et ses pâturages, Thabor et ses pâturages;
78 Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko, analandira Bezeri ku chipululu, Yaza,
de l'autre côté du Jourdain, vis-à-vis de Jéricho, à l'orient du Jourdain: de la tribu de Ruben, Bosor, au désert, et ses pâturages, Jassa et ses pâturages,
79 Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
Cadémoth et ses pâturages, Méphaat et ses pâturages;
80 ndipo kuchokera ku fuko la Gadi analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu,
et de la tribu de Gad, Ramoth en Galaad et ses pâturages, Manaïm, et ses pâturages,
81 Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.
Hésebon et ses pâturages, Jézer et ses pâturages.