< 1 Mbiri 4 >

1 Ana a Yuda anali awa: Perezi, Hezironi, Karimi, Huri ndi Sobali.
בני יהודה פרץ חצרון וכרמי וחור ושובל׃
2 Reaya mwana wa Sobala anabereka Yahati, ndipo Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Awa anali mabanja a Azorati.
וראיה בן שובל הוליד את יחת ויחת הליד את אחומי ואת להד אלה משפחות הצרעתי׃
3 Ana a Etamu anali awa: Yezireeli, Isima ndi Idibasi. Dzina la mlongo wawo linali Hazeleliponi.
ואלה אבי עיטם יזרעאל וישמא וידבש ושם אחותם הצללפוני׃
4 Penueli anabereka Gedori, ndipo Ezeri anabereka Husa. Awa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi abambo a Betelehemu.
ופנואל אבי גדר ועזר אבי חושה אלה בני חור בכור אפרתה אבי בית לחם׃
5 Asihuri abambo a Tekowa anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara.
ולאשחור אבי תקוע היו שתי נשים חלאה ונערה׃
6 Naara anamuberekera Ahuzamu, Heferi, Temani ndi Haahasitari. Awa ndiwo anali ana a Naara.
ותלד לו נערה את אחזם ואת חפר ואת תימני ואת האחשתרי אלה בני נערה׃
7 Ana a Hela: Zereti, Zohari, Etinani,
ובני חלאה צרת יצחר ואתנן׃
8 ndi Kozi, amene anali abambo ake a Anubi ndi Hazo-Beba ndi mabanja a Ahariheli mwana wa Harumi.
וקוץ הוליד את ענוב ואת הצבבה ומשפחות אחרחל בן הרום׃
9 Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, “Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri.”
ויהי יעבץ נכבד מאחיו ואמו קראה שמו יעבץ לאמר כי ילדתי בעצב׃
10 Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.
ויקרא יעבץ לאלהי ישראל לאמר אם ברך תברכני והרבית את גבולי והיתה ידך עמי ועשית מרעה לבלתי עצבי ויבא אלהים את אשר שאל׃
11 Kelubi, mʼbale wa Suha, anabereka Mehiri, amene anabereka Esitoni.
וכלוב אחי שוחה הוליד את מחיר הוא אבי אשתון׃
12 Esitoni anabereka Beti-Rafa, Paseya ndi Tehina amene anabereka Iri Nahasi. Amenewa ndiwo anthu a ku Reka.
ואשתון הוליד את בית רפא ואת פסח ואת תחנה אבי עיר נחש אלה אנשי רכה׃
13 Ana a Kenazi anali awa: Otanieli ndi Seraya. Ana a Otanieli anali awa: Hatati ndi Meonotai.
ובני קנז עתניאל ושריה ובני עתניאל חתת׃
14 Meonotai anabereka Ofura. Seraya anabereka Yowabu, amene anabereka Ge-Harasimu. Anawatcha dzina ili chifukwa anthu ake anali amisiri.
ומעונתי הוליד את עפרה ושריה הוליד את יואב אבי גיא חרשים כי חרשים היו׃
15 Ana a Kalebe mwana wa Yefune anali awa: Iru, Ela ndi Naama. Mwana wa Ela anali Kenazi.
ובני כלב בן יפנה עירו אלה ונעם ובני אלה וקנז׃
16 Ana a Yehaleleli anali awa: Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asareli.
ובני יהללאל זיף וזיפה תיריא ואשראל׃
17 Ana a Ezara anali awa: Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mmodzi mwa akazi a Meredi anabereka Miriamu, Samai ndi Isiba abambo ake a Esitemowa.
ובן עזרה יתר ומרד ועפר וילון ותהר את מרים ואת שמי ואת ישבח אבי אשתמע׃
18 (Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira.
ואשתו היהדיה ילדה את ירד אבי גדור ואת חבר אבי שוכו ואת יקותיאל אבי זנוח ואלה בני בתיה בת פרעה אשר לקח מרד׃
19 Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wa Nahamu anali awa: abambo ake a Keila wa ku Garimi ndi Esitemowa wa ku Maaka.
ובני אשת הודיה אחות נחם אבי קעילה הגרמי ואשתמע המעכתי׃
20 Ana a Simeoni anali awa: Amnoni, Rina, Beni-Hanani ndi Tiloni. Ana a Isi anali awa: Zoheti ndi Beni-Zoheti.
ובני שימון אמנון ורנה בן חנן ותולון ובני ישעי זוחת ובן זוחת׃
21 Ana a Sela mwana wa Yuda anali awa: Eri amene anabereka Leka, Laada amene anabereka Maresa ndi mabanja a anthu owomba nsalu zofewa ndi zosalala a ku Beti-Asibeya,
בני שלה בן יהודה ער אבי לכה ולעדה אבי מרשה ומשפחות בית עבדת הבץ לבית אשבע׃
22 Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale).
ויוקים ואנשי כזבא ויואש ושרף אשר בעלו למואב וישבי לחם והדברים עתיקים׃
23 Iwo anali owumba mbiya amene ankakhala ku Netaimu ndi Gederi. Ankakhala kumeneko ndi kumatumikira mfumu.
המה היוצרים וישבי נטעים וגדרה עם המלך במלאכתו ישבו שם׃
24 Ana a Simeoni anali awa: Nemueli, Yamini, Yaribu, Zera ndi Sauli;
בני שמעון נמואל וימין יריב זרח שאול׃
25 Salumu anali mwana wa Sauli, Mibisamu anali mwana wa Salumu ndipo Misima anali mwana wa Mibisamu.
שלם בנו מבשם בנו משמע בנו׃
26 Zidzukulu za Misima zinali izi: Hamueli, Zakuri ndi Simei.
ובני משמע חמואל בנו זכור בנו שמעי בנו׃
27 Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda.
ולשמעי בנים ששה עשר ובנות שש ולאחיו אין בנים רבים וכל משפחתם לא הרבו עד בני יהודה׃
28 Iwo amakhala ku Beeriseba, Molada, Hazari-Suwali,
וישבו בבאר שבע ומולדה וחצר שועל׃
29 Biliha, Ezemu, Toladi,
ובבלהה ובעצם ובתולד׃
30 Betueli, Horima, Zikilagi,
ובבתואל ובחרמה ובציקלג׃
31 Beti-Marikaboti, Hazari-Susimu, Beti-Biri ndi Saaraimu. Iyi inali mizinda yawo mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Davide.
ובבית מרכבות ובחצר סוסים ובבית בראי ובשערים אלה עריהם עד מלך דויד׃
32 Midzi yowazungulira inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, midzi isanu
וחצריהם עיטם ועין רמון ותכן ועשן ערים חמש׃
33 ndi midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baala. Awa anali malo awo okhalapo. Ndipo anasunga mbiri ya makolo awo.
וכל חצריהם אשר סביבות הערים האלה עד בעל זאת מושבתם והתיחשם להם׃
34 Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya,
ומשובב וימלך ויושה בן אמציה׃
35 Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli,
ויואל ויהוא בן יושביה בן שריה בן עשיאל׃
36 komanso Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya,
ואליועיני ויעקבה וישוחיה ועשיה ועדיאל וישימאל ובניה׃
37 ndiponso Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya.
וזיזא בן שפעי בן אלון בן ידיה בן שמרי בן שמעיה׃
38 Anthu amene atchulidwawa anali atsogoleri a mabanja awo. Mabanja awo anakula kwambiri
אלה הבאים בשמות נשיאים במשפחותם ובית אבותיהם פרצו לרוב׃
39 ndipo anakafika ku malire a Gedori ku chigwa cha kummawa kufuna msipu wodyetsa ziweto zawo.
וילכו למבוא גדר עד למזרח הגיא לבקש מרעה לצאנם׃
40 Anapeza msipu wobiriwira ndi wabwino ndipo dziko linali lalikulu, la mtendere ndi bata. Kumeneko kunkakhala fuko la Hamu poyamba.
וימצאו מרעה שמן וטוב והארץ רחבת ידים ושקטת ושלוה כי מן חם הישבים שם לפנים׃
41 Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo.
ויבאו אלה הכתובים בשמות בימי יחזקיהו מלך יהודה ויכו את אהליהם ואת המעינים אשר נמצאו שמה ויחרימם עד היום הזה וישבו תחתיהם כי מרעה לצאנם שם׃
42 Ndipo anthu 500 a fuko la Simeoni, motsogozedwa ndi Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uzieli, ana a Isi, analanda dziko lamapiri la Seiri.
ומהם מן בני שמעון הלכו להר שעיר אנשים חמש מאות ופלטיה ונעריה ורפיה ועזיאל בני ישעי בראשם׃
43 Iwo anapha Aamaleki otsala amene anali atapulumuka ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.
ויכו את שארית הפלטה לעמלק וישבו שם עד היום הזה׃

< 1 Mbiri 4 >