< 1 Mbiri 3 >

1 Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli; wachiwiri anali Danieli, amayi ake anali Abigayeli wa ku Karimeli;
Tito jsou pak synové Davidovi, kteříž se jemu zrodili v Hebronu: Prvorozený Amnon z Achinoam Jezreelské, druhý Daniel z Abigail Karmelské;
2 wachitatu anali Abisalomu, mwana wa Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri; wachinayi anali Adoniya amayi ake anali Hagiti;
Třetí Absolon syn Maachy, dcery Tolmai, krále Gessur, čtvrtý Adoniáš, syn Haggit;
3 wachisanu anali Sefatiya, amayi ake anali Abitali; wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila.
Pátý Sefatiáš z Abitál, šestý Jetram, z Egly manželky jeho.
4 Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi. Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33,
Šest se mu jich zrodilo v Hebronu, kdež kraloval sedm let a šest měsíců; třidceti pak a tři kraloval v Jeruzalémě.
5 ndipo ana amene anabadwira ku Yerusalemuko anali awa: Samua, Sobabu, Natani ndi Solomoni. Ana anayi awa anali a Batisuwa mwana wa Amieli.
Potom tito se jemu zrodili v Jeruzalémě: Sammua, Sobab, Nátan a Šalomoun, čtyři, z Betsabé, dcery Amielovy;
6 Anaberekanso Ibihari, Elisua, Elipeleti,
Též Ibchar, Elisama a Elifelet;
7 Noga, Nefegi, Yafiya,
A Noga, Nefeg a Jafia;
8 Elisama, Eliada ndi Elifeleti, onse analipo asanu ndi anayi.
A Elisama, Eliada a Elifelet, těch devět.
9 Onsewa anali ana a Davide, osawerengera ana a azikazi. Ndipo mlongo wawo anali Tamara.
Všickni ti synové Davidovi krom synů ženin, a Támar sestra jejich.
10 Mwana wa Solomoni anali Rehabiamu, Rehabiamu anabereka Abiya, Abiya anabereka Asa, Asa anabereka Yehosafati,
Syn pak Šalomounův Roboám, Abiam syn jeho, Aza syn jeho, Jozafat syn jeho,
11 Yehosafati anabereka Yehoramu, Yehoramu anabereka Ahaziya, Ahaziya anabereka Yowasi,
Joram syn jeho, Ochoziáš syn jeho, Joas syn jeho,
12 Yowasi anabereka Amaziya, Amaziya anabereka Azariya, Azariya anabereka Yotamu,
Amaziáš syn jeho, Azariáš syn jeho, Jotam syn jeho,
13 Yotamu anabereka Ahazi, Ahazi anabereka Hezekiya, Hezekiya anabereka Manase,
Achas syn jeho, Ezechiáš syn jeho, Manasses syn jeho,
14 Manase anabereka Amoni, Amoni anabereka Yosiya.
Amon syn jeho, Joziáš syn jeho.
15 Ana a Yosiya anali awa: Yohanani mwana wake woyamba, Yehoyakimu mwana wake wachiwiri, Zedekiya mwana wake wachitatu, Salumu mwana wake wachinayi.
Synové pak Joziášovi: Prvorozený Jochanan, druhý Joakim, třetí Sedechiáš, čtvrtý Sallum.
16 Ana a Yehoyakimu: Yekoniya ndi Zedekiya mwana wake.
Synové pak Joakimovi: Jekoniáš syn jeho, Sedechiáš syn jeho.
17 Zidzukulu za Yekoniya wa mʼndende zinali izi: mwana wake Silatieli,
Synové pak Jekoniáše vězně: Salatiel syn jeho.
18 Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama ndi Nedabiya.
Toho pak Malkiram, Pedai, Senazar, Jekamia, Hosama a Nedabia.
19 Ana a Pedaya anali awa: Zerubabeli ndi Simei. Ana a Zerubabeli anali awa: Mesulamu ndi Hananiya. Mlongo wawo anali Selomiti.
Synové pak Pedaiovi: Zorobábel a Semei. A syn Zorobábelův: Mesullam, Chananiáš, a Selomit sestra jejich.
20 Panalinso ana ena asanu awa: Hasubu, Oheli, Berekiya, Hasabiya ndi Yusabu-Hesedi.
Toho pak Chasuba, Ohel, Berechiáš, Chasadiáš a Jusabchesed, těch pět.
21 Zidzukulu za Hananiya zinali izi: Pelatiya ndi Yesaiya, ndiponso ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya ndi ana a Sekaniya.
Syn pak Chananiášův: Pelatia a Izaiáš. Synové Refaie, synové Arnanovi, synové Abdiášovi, synové Sechaniovi.
22 Zidzukulu za Sekaniya zinali izi: Semaya ndi ana ake: Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati. Onse anali asanu ndi mmodzi.
A synové Sechaniovi: Semaiáš. A synové Semaiášovi: Chattus, Igal, Bariach, Neariáš a Safat, šest.
23 Ana a Neariya anali awa: Eliyoenai, Hezekiya ndi Azirikamu. Onse anali atatu.
A syn Neariáše: Elioenai, Ezechiáš a Azrikam, ti tři.
24 Ana a Eliyoenai: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya ndi Anani, onse anali asanu ndi awiri.
Též synové Elioenai: Hodaviáš, Eliasib, Pelaiáš, Akkub, Jochanan, Delaiáš a Anani, těch sedm.

< 1 Mbiri 3 >