< 1 Mbiri 28 >
1 Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima.
Und David versammelte gen Jerusalem alle Obersten Israels, nämlich die Fürsten der Stämme, die Fürsten der Ordnungen, die dem König dienten, die Fürsten über tausend und über hundert, die Fürsten über die Güter und das Vieh des Königs und seiner Söhne mit den Kämmerern, die Kriegsmänner und alle ansehnlichen Männer.
2 Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.”
Und David, der König, stand auf und sprach: Höret mir zu, meine Brüder und mein Volk! Ich hatte mir vorgenommen, ein Haus zu bauen, da ruhen sollte die Lade des Bundes des HERRN und der Schemel seiner Füße unsres Gottes, und hatte mich geschickt, zu bauen.
3 Koma Mulungu anati kwa ine, “Usandimangire nyumba chifukwa ndiwe munthu wankhondo ndipo wakhala ukukhetsa magazi.”
Aber Gott ließ mir sagen: Du sollst meinem Namen kein Haus bauen; denn du bist ein Kriegsmann und hast Blut vergossen.
4 “Komabe Yehova Mulungu wa Israeli anasankha ine pakati pa onse a banja langa kukhala mfumu ya Israeli kwamuyaya. Iye anasankha Yuda kukhala mtsogoleri, ndipo pa banja la Yuda anasankha banja langa. Pakati pa ana aamuna a abambo anga, kunamukomera Iye kundikhazika mfumu ya Aisraeli onse.
Nun hat der HERR, der Gott Israel, mich erwählt aus meines Vaters ganzem Hause, daß ich König über Israel sein sollte ewiglich. Denn er hat Juda erwählt zum Fürstentum, und im Hause Juda meines Vaters Haus, und unter meines Vaters Kindern hat er Gefallen gehabt an mir, daß er mich über ganz Israel zum König machte.
5 Pa ana anga ambiri onse amene Yehova wandipatsa, Iye wasankha mwana wanga Solomoni kuti akhale pa mpando waufumu wa ufumu wa Yehova kuti alamulire Israeli.”
Und unter allen seinen Söhnen (denn der HERR hat mir viele Söhne gegeben) hat er meinen Sohn Salomo erwählt, daß er sitzen soll auf dem Stuhl des Königreichs des Herrn über Israel,
6 Yehova anati kwa ine, “Solomoni mwana wako ndiye amene adzamanga nyumba yanga ndi mabwalo anga, pakuti Ine ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake.
und hat zu mir geredet: Dein Sohn Salomo soll mein Haus und meine Vorhöfe bauen; denn ich habe ihn erwählt zum Sohn, und ich will sein Vater sein
7 Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya ngati iye saleka kutsatira malamulo ndi malangizo anga, monga momwe zikuchitikira leromu.”
und will sein Königreich bestätigen ewiglich, so er wird anhalten, daß er tue nach meinen Geboten und Rechten, wie es heute steht.
8 “Tsono lero ine ndikulamula inu pamaso pa Aisraeli onse ndi pa msonkhano wa Yehova, ndipo Mulungu wathu akumva: Mutsatire mosamala malamulo a Yehova Mulungu wathu, kuti dziko labwinoli likhale lanu ndi kuti mudzalipereke kwa zidzukulu zanu kukhala cholowa chawo kwamuyaya.”
Nun vor dem ganzen Israel, der Gemeinde des HERRN, und vor den Ohren unseres Gottes: So haltet und sucht alle die Gebote des HERRN, eures Gottes, auf daß ihr besitzet das gute Land und es vererbt auf eure Kinder nach euch ewiglich.
9 “Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya.
Und du, mein Sohn Salomo, erkenne den Gott deines Vaters und diene ihm mit ganzem Herzen und mit williger Seele. Denn der HERR sucht alle Herzen und versteht aller Gedanken Dichten. Wirst du ihn suchen, so wirst du ihn finden; wirst du ihn aber verlassen, so wird er dich verwerfen ewiglich.
10 Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.”
So siehe nun zu; denn der HERR hat dich erwählt, daß du sein Haus baust zum Heiligtum. Sei getrost und mache es!
11 Kotero Davide anapatsa Solomoni mwana wake mapulani a khonde la Nyumba ya Mulungu, nyumba zake, mosungiramo katundu, zipinda zake zamʼmwamba, zipinda zamʼkati ndi malo a nsembe zopepesera machimo.
Und David gab seinem Sohn Salomo ein Vorbild der Halle des Tempels und seiner Häuser und der Gemächer und Söller und Kammern inwendig und des Hauses Gnadenstuhls,
12 Iye anapatsa Solomoni mapulani a zonse zimene ankaziganizira za bwalo la Nyumba ya Yehova ndi zipinda zonse zozungulira, zipinda zosungiramo chuma cha Nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Yehova.
dazu Vorbilder alles dessen, was bei ihm in seinem Gemüt war, nämlich die Vorhöfe am Hause des HERRN und aller Gemächer umher für die Schätze im Hause Gottes und für die Schätze des Geheiligten,
13 Davide anamulangiza za magulu a ansembe ndi Alevi ndi ntchito yonse yotumikira mʼNyumba ya Yehova, komanso za zinthu zonse zogwirira ntchito potumikira.
und der Ordnungen der Priester und Leviten, und aller Geschäfte und Geräte der Ämter im Hause des HERRN,
14 Iye anakonzeratu za kulemera kwa golide wopangira zida zonse zagolide zogwirira ntchito zosiyanasiyana, ndiponso kulemera kwa siliva wopangira zida zonse zasiliva zogwirira ntchito zosiyanasiyana:
und des goldenen Zeuges nach dem Goldgewicht zu allerlei Geräte eines jeglichen Amts, und alles silbernen Zeuges nach dem Gewicht zu allerlei Geräte eines jeglichen Amts,
15 kulemera kwa golide wopangira choyikapo nyale chagolide ndi nyale zake; ndiponso kulemera kwa siliva wa choyikapo nyale chilichonse ndi nyale zake, molingana ndi kagwiritsidwe ka choyikapo nyale chilichonse;
und das Gewicht für den goldenen Leuchter und die goldenen Lampen, für jeglichen Leuchter und seine Lampen sein Gewicht, also auch für die silbernen Leuchter, für den Leuchter und seine Lampen, nach dem Amt eines jeglichen Leuchters;
16 kulemera kwa golide wa tebulo iliyonse yoyikapo buledi wopatulika; kulemera kwa siliva wopangira matebulo asiliva;
auch gab er das Gewicht des Goldes für die Tische der Schaubrote, für jeglichen Tisch sein Gewicht, also auch des Silbers für die silbernen Tische,
17 muyeso wa golide woyengeka bwino wopangira mafoloko, mbale ndi zotungira; muyeso wa golide wa beseni lililonse la siliva;
und für die Gabeln, Becken und Kannen von lauterem Golde und für die goldenen Becher, für jeglichen Becher sein Gewicht, und für die silbernen Becher, für jeglichen Becher sein Gewicht,
18 ndiponso muyeso wa golide wabwino wopangira guwa la zofukiza. Davide anamupatsanso ndondomeko ya mapangidwe a galeta, akerubi agolide atatambasula mapiko awo kuphimba Bokosi la Chipangano la Yehova.
und für den Räucheraltar vom allerlautersten Golde sein Gewicht, auch ein Vorbild des Wagens, nämlich der goldenen Cherubim, daß sie sich ausbreiteten und bedeckten oben die Lade des Bundes des HERRN.
19 Davide anati, “Zonsezi ndalemba kuchokera kwa Yehova, ndipo Iye wachita kuti ndimvetsetse zonse za mapulaniwa.”
“Das alles ist mir beschrieben gegeben von der Hand des HERRN, daß es mich unterwiese über alle Werke des Vorbildes.”
20 Davide anatinso kwa mwana wake Solomoni, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndipo uchite ntchitoyi. Usachite mantha kapena kutaya mtima pakuti Yehova Mulungu wanga ali nawe. Iye sadzakukhumudwitsa kapena kukusiya mpaka ntchito yonse ya Nyumba ya Mulungu itatha.
Und David sprach zu seinem Sohn Salomo: Sei getrost und unverzagt und mache es; fürchte dich nicht und zage nicht! Gott der HERR, mein Gott, wird mit dir sein und wird die Hand nicht abziehen noch dich verlassen, bis du alle Werke zum Amt im Hause des HERRN vollendest.
21 Magulu a ansembe ndi Alevi ndi okonzeka kugwira ntchito ya Nyumba ya Mulungu, ndipo munthu waluso aliyense wodzipereka adzakuthandiza pa ntchito yonse. Akuluakulu ndi anthu onse adzamvera chilichonse chomwe udzalamula.”
Siehe da, die Ordnungen der Priester und Leviten zu allen Ämtern im Hause Gottes sind mit dir zu allem Geschäft und sind willig und weise zu allen Ämtern, dazu die Fürsten und alles Volk zu allen deinen Händeln.