< 1 Mbiri 27 >

1 Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.
Y LOS hijos de Israel según su número, [á saber], príncipes de familias, tribunos, centuriones y oficiales de los que servían al rey en todos los negocios de las divisiones que entraban y salían cada mes en todos los meses del año, eran en cada división veinte y cuatro mil.
2 Amene amalamulira gulu loyamba pa mwezi woyamba anali Yasobeamu mwana wa Zabidieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
Sobre la primera división del primer mes estaba Jasobam hijo de Zabdiel; y había en su división veinte y cuatro mil.
3 Iyeyu anali chidzukulu cha Perezi ndipo anali mkulu wa atsogoleri onse a ankhondo mwezi woyamba.
De los hijos de Phares [fué] él jefe de todos los capitanes de las compañías del primer mes.
4 Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
Sobre la división del segundo mes estaba Dodai Ahohita: y Micloth [era] mayor general en su división, en la que también había veinte y cuatro mil.
5 Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000.
El jefe de la tercera división para el tercer mes era Benaías, hijo de Joiada sumo sacerdote; y en su división había veinte y cuatro mil.
6 Uyu ndi Benaya uja amene anali wamphamvu pa gulu la anthu makumi atatu ndipo ndiye amatsogolera anthu makumi atatu aja. Mwana wake Amizabadi ndiye amatsogolera gulu lake.
Este Benaías era valiente entre los treinta y sobre los treinta; y en su división estaba Amisabad su hijo.
7 Wachinayi pa mwezi wachinayi anali Asaheli mʼbale wake wa Yowabu; ndipo mwana wake Zebadiya ndiye analowa mʼmalo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El cuarto [jefe] para el cuarto mes era Asael hermano de Joab, y después de él Zebadías su hijo; y en su división había veinte y cuatro mil.
8 Wachisanu pa mwezi wachisanu anali Samihuti, mdzukulu wa Izira. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El quinto jefe para el quinto mes era Sambuth Izrita: y en su división había veinte y cuatro mil.
9 Wa 6 pa mwezi wa 6 anali Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El sexto para el sexto mes era Hira hijo de Icces, de Tecoa; y en su división veinte y cuatro mil.
10 Wa 7 pa mwezi wa 7 anali Helezi Mpeloni wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El séptimo para el séptimo mes era Helles Pelonita, de los hijos de Ephraim; y en su división veinte y cuatro mil.
11 Wa 8 pa mwezi wa 8 anali Sibekai Mhusati, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000
El octavo para el octavo mes era Sibbecai Husatita, de Zarahi; y en su división veinte y cuatro mil.
12 Wa 9 pa mwezi wa 9 anali Abiezeri wa banja la Anatoti, wa fuko la Benjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El noveno para el noveno mes era Abiezer Anathothita, de los Benjamitas; y en su división veinte y cuatro mil.
13 Wa khumi pa mwezi wa khumi anali Mahazayi wa ku Netofa, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El décimo para el décimo mes era Maharai Nethophathita, de Zarahi; y en su división veinte y cuatro mil.
14 Mtsogoleri wa 11, pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El undécimo para el undécimo mes era Benaías Piratonita, de los hijos de Ephraim; y en su división veinte y cuatro mil.
15 Mtsogoleri wa 12, pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, wa banja la Otanieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
El duodécimo para el duodécimo mes era Heldai Nethophathita, de Othniel; y en su división veinte y cuatro mil.
16 Akuluakulu amene amatsogolera mafuko a Israeli ndi awa: Mtsogoleri wa fuko la Rubeni: Eliezara mwana wa Zikiri; mtsogoleri wa fuko la Simeoni: Sefatiya mwana wa Maaka;
Asimismo sobre las tribus de Israel: el jefe de los Rubenitas era Eliezer hijo de Zichri; de los Simeonitas, Sephatías, hijo de Maachâ:
17 mtsogoleri wa fuko la Levi: Hasabiya mwana wa Kemueli, mtsogoleri wa banja la Aaroni: Zadoki;
De los Levitas, Hasabías hijo de Camuel; de los Aaronitas, Sadoc;
18 mtsogoleri wa fuko la Yuda: Elihu, mʼbale wake wa Davide; mtsogoleri wa fuko la Isakara: Omuri mwana wa Mikayeli;
De Judá, Eliú, uno de los hermanos de David; de los de Issachâr, Omri hijo de Michâel;
19 mtsogoleri wa fuko la Zebuloni: Isimaiya mwana wa Obadiya; mtsogoleri wa fuko la Nafutali: Yerimoti mwana wa Azirieli;
De los de Zabulón, Ismaías hijo de Abdías; de los de Nephtalí, Jerimoth hijo de Azriel;
20 mtsogoleri wa fuko la Efereimu: Hoseya mwana wa Azaziya; mtsogoleri wa fuko la theka la Manase: Yoweli mwana wa Pedaya;
De los hijos de Ephraim, Oseas hijo de Azazía; de la media tribu de Manasés, Joel hijo de Pedaía;
21 mtsogoleri wa fuko la theka la Manase limene linali ku Giliyadi: Ido mwana wa Zekariya; mtsogoleri wa fuko la Benjamini: Yaasieli mwana wa Abineri;
De la otra media tribu de Manasés en Galaad, Iddo hijo de Zachârías; de los de Benjamín, Jaaciel hijo de Abner;
22 mtsogoleri wa fuko la Dani: Azareli mwana wa Yerohamu. Awa anali akuluakulu a mafuko a Israeli.
Y de Dan, Azarael hijo de Jeroam. Estos fueron los jefes de las tribus de Israel.
23 Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga.
Y no tomó David el número de los que eran de veinte años abajo, por cuanto Jehová había dicho que él había de multiplicar á Israel como las estrellas del cielo.
24 Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide.
Joab hijo de Sarvia había comenzado á contar, mas no acabó, pues por esto vino la ira sobre Israel: y [así] el número no fué puesto en el registro de las crónicas del rey David.
25 Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera.
Y Azmaveth hijo de Adiel tenía cargo de los tesoros del rey; y de los tesoros de los campos, y de las ciudades, y de las aldeas y castillos, Jonathán hijo de Uzzías;
26 Eziri mwana wa Kelubi ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima ku munda.
Y de los que trabajaban en la labranza de las tierras, Ezri hijo de Chêlud;
27 Simei wa ku Rama ankayangʼanira minda ya mpesa. Zabidi wa ku Sifamu ankayangʼanira mphesa ndi mosungiramo mwake.
Y de las viñas Simi Ramathita; y del fruto de las viñas para las bodegas, Zabdías Siphmita;
28 Baala-Hanani wa ku Gederi ankayangʼanira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ya ku Sefela. Yowasi ankayangʼanira mafuta a Olivi.
Y de los olivares é higuerales que había en las campiñas, Baal-hanan Gederita; y de los almacenes del aceite, Joas;
29 Sitirayi wa ku Saroni ankayangʼanira ziweto zimene amaweta ku Saroni. Safati mwana wa Adilayi ankayangʼanira ngʼombe zakuzigwa.
De las vacas que pastaban en Sarón, Sitrai Saronita; y de las vacas que estaban en los valles, Saphat hijo de Adlai;
30 Obili Mwismaeli ankayangʼanira ngamira. Yehideya Mmerenoti ankayangʼanira abulu.
Y de los camellos, Obil Ismaelita; y de las asnas, Jedías Meronothita;
31 Yazizi Mhagiri akayangʼanira nkhosa ndi mbuzi. Onsewa anali akuluakulu oyangʼanira chuma cha mfumu Davide.
Y de las ovejas, Jaziz Agareno. Todos estos eran superintendentes de la hacienda del rey David.
32 Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu.
Y Jonathán, tío de David, era consejero, varón prudente y escriba; y Jehiel hijo de Hacmoni estaba con los hijos del rey.
33 Ahitofele anali phungu wa mfumu. Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu.
Y también Achitophel era consejero del rey; y Husai Arachîta amigo del rey.
34 Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara. Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.
Después de Achitophel era Joiada hijo de Benaías, y Abiathar. Y Joab era el general del ejército del rey.

< 1 Mbiri 27 >