< 1 Mbiri 25 >

1 Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:
Moreover David and the captains of the army set apart for the service certain of the sons of Asaph, and of Heman, and of Jeduthun, who should prophesy with harps, with psalteries, and with cymbals. And the number of those who did the work according to their service was:
2 Kuchokera kwa ana a Asafu: Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu.
of the sons of Asaph: Zaccur, and Joseph, and Nethaniah, and Asharelah, the sons of Asaph, under the hand of Asaph, who prophesied after the order of the king.
3 Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.
Of Jeduthun, the sons of Jeduthun: Gedaliah, and Zeri, and Jeshaiah, Hashabiah, and Mattithiah, six, under the hands of their father Jeduthun with the harp, who prophesied in giving thanks and praising Jehovah.
4 Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake: Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti.
Of Heman, the sons of Heman: Bukkiah, Mattaniah, Uzziel, Shebuel, and Jerimoth, Hananiah, Hanani, Eliathah, Giddalti, and Romamtiezer, Joshbekashah, Mallothi, Hothir, Mahazioth.
5 Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.
All these were the sons of Heman the king's seer in the words of God, to lift up the horn. And God gave to Heman fourteen sons and three daughters.
6 Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.
All these were under the hands of their father for song in the house of Jehovah, with cymbals, psalteries, and harps, for the service of the house of God; Asaph, Jeduthun, and Heman being under the order of the king.
7 Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.
And the number of them, with their brothers who were instructed in singing to Jehovah, even all who were skilful, was two hundred eighty-eight.
8 Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.
And they cast lots for their offices, all alike, as well the small as the great, the teacher as the scholar.
9 Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe, ana ndi abale ake. 12 Maere achiwiri anagwera Gedaliya, ndi abale ake ndi ana ake. 12
Now the first lot came forth for Asaph to Joseph, the second to Gedaliah (he and his brothers and sons were twelve),
10 Maere achitatu anagwera Zakuri, ana ake ndi abale ake. 12
the third to Zaccur, his sons and his brothers, twelve;
11 Maere achinayi anagwera Iziri, ana ake ndi abale ake. 12
the fourth to Izri, his sons and his brothers, twelve;
12 Maere achisanu anagwera Netaniya, ana ake ndi abale ake. 12
the fifth to Nethaniah, his sons and his brothers, twelve;
13 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya, ana ake ndi abale ake. 12
the sixth to Bukkiah, his sons and his brothers, twelve;
14 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela, ana ake ndi abale ake. 12
the seventh to Jesharelah, his sons and his brothers, twelve;
15 Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya, ana ake ndi abale ake. 12
the eighth to Jeshaiah, his sons and his brothers, twelve;
16 Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya, ana ake ndi abale ake. 12
the ninth to Mattaniah, his sons and his brothers, twelve;
17 Maere a khumi anagwera Simei, ana ake ndi abale ake. 12
the tenth to Shimei, his sons and his brothers, twelve;
18 Maere a 11 anagwera Azareli, ana ake ndi abale ake. 12
the eleventh to Azarel, his sons and his brothers, twelve;
19 Maere a 12 anagwera Hasabiya, ana ake ndi abale ake. 12
the twelfth to Hashabiah, his sons and his brothers, twelve;
20 Maere a 13 anagwera Subaeli, ana ake ndi abale ake. 12
for the thirteenth, Shubael, his sons and his brothers, twelve;
21 Maere a 14 anagwera Matitiya, ana ake ndi abale ake. 12
for the fourteenth, Mattithiah, his sons and his brothers, twelve;
22 Maere a 15 anagwera Yeremoti, ana ake ndi abale ake. 12
for the fifteenth to Jeremoth, his sons and his brothers, twelve;
23 Maere a 16 anagwera Hananiya, ana ake ndi abale ake. 12
for the sixteenth to Hananiah, his sons and his brothers, twelve;
24 Maere a 17 anagwera Yosibakasa, ana ake ndi abale ake. 12
for the seventeenth to Joshbekashah, his sons and his brothers, twelve;
25 Maere a 18 anagwera Hanani, ana ake ndi abale ake. 12
for the eighteenth to Hanani, his sons and his brothers, twelve;
26 Maere a 19 anagwera Maloti, ana ake ndi abale ake. 12
for the nineteenth to Mallothi, his sons and his brothers, twelve;
27 Maere a 20 anagwera Eliyata, ana ake ndi abale ake. 12
for the twentieth to Eliathah, his sons and his brothers, twelve;
28 Maere a 21 anagwera Hotiri, ana ake ndi abale ake. 12
for the twenty-first to Hothir, his sons and his brothers, twelve;
29 Maere a 22 anagwera Gidaliti, ana ake ndi abale ake. 12
for the twenty-second to Giddalti, his sons and his brothers, twelve;
30 Maere a 23 anagwera Mahazioti, ana ake ndi abale ake. 12
for the twenty-third to Mahazioth, his sons and his brothers, twelve;
31 Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri, ana ake ndi abale ake 12.
for the twenty-fourth to Romamtiezer, his sons and his brothers, twelve.

< 1 Mbiri 25 >