< 1 Mbiri 21 >
1 Satana anafuna kuvutitsa Aisraeli choncho anawutsa mtima wa Davide kuti awerenge Aisraeli.
2 Choncho Davide anati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, “Pitani mukawerenge Aisraeli kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani. Ndipo mudzandiwuze kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”
3 Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?”
4 Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu, kotero Yowabu anapita mu Israeli monse ndipo kenaka anabwera ku Yerusalemu.
5 Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda.
6 Koma Yowabu sanaphatikizepo fuko la Levi ndi fuko la Benjamini pa chiwerengerochi, pakuti lamulo la mfumu linamuyipira.
7 Lamulo limeneli silinakomerenso Mulungu. Kotero Iye analanga Israeli.
8 Choncho Davide anati kwa Mulungu, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”
9 Yehova anati kwa Gadi, mlosi wa Davide,
10 “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’”
11 Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa Iye, “Yehova akuti, ‘Musankhepo chimene mungakonde kuti chichitike:
12 mʼdziko mukhale njala zaka zitatu, mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu, akukukanthani ndi lupanga la Yehova, kapena mʼdziko mukhale mliri kwa masiku atatu, mngelo wa Yehova akuwononga Israeli yense.’ Ndipo tsono ganizirani bwino chomwe ndikamuyankhe amene wandituma.”
13 Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ine andilange ndi Yehova, pakuti chifundo chake ndi chachikulu kwambiri; koma ndisalangidwe ndi anthu.”
14 Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000.
15 Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
16 Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba.
17 Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.”
18 Pamenepo mngelo wa Yehova analamula Gadi kuti awuze Davide kuti akamange guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
19 Ndipo Davide anapita pomvera mawu amene Gadi ananena mʼdzina la Yehova.
20 Pamene Arauna ankapuntha tirigu, anatembenuka ndipo anaona mngelo ndipo ana ake anayi aamuna amene anali naye anabisala.
21 Davide anayandikira, ndipo Arauna atayangʼana ndi kumuona, anachoka popunthira tirigupo ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi pamaso pa Davide.
22 Davide anati kwa Arauna, “Undipatse malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe, kuti mliri uli pa anthuwa usiye. Undigulitse ine pa mtengo woyenera ndithu.”
23 Arauna anati kwa Davide, “Tengani! Mbuye wanga mfumu achite chomukomera. Taonani ine ndidzapereka ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, zopunthira tirigu zidzakhala nkhuni ndipo tiriguyu adzakhala chopereka chachakudya. Ndidzapereka zonsezi.”
24 Koma mfumu Davide inayankha Arauna kuti, “Ayi, ine ndikuti ndipereka mtengo wathunthu. Sindingatenge chinthu chako ndi kuchipereka kwa Yehova, kapena kupereka nsembe imene sindinayigule.”
25 Choncho Davide analipira Arauna masekeli agolide 600 chifukwa cha malowo.
26 Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Iye anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anayankha potumiza moto pa guwa lansembe zopsereza kuchokera kumwamba.
27 Tsono Yehova anayankhula kwa mngelo, ndipo analowetsa lupanga lake mʼchimake.
28 Pa nthawi imeneyo, Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi, anapereka nsembe pamenepo.
29 Tenti ya Yehova imene Mose anapanga mʼchipululu, ndi guwa lansembe zopsereza pa nthawi imeneyi zinali pa phiri ku Gibiyoni.
30 Koma Davide sanathe kupita kumeneko kuti akapemphere pamaso pa Yehova, chifukwa amaopa lupanga la mngelo wa Yehova.