< 1 Mbiri 2 >
1 Ana a Israeli anali awa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni,
Вот сыновья Израиля: Рувим, Симеон, Левий, Иуда, Иссахар, Завулон,
2 Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri.
Дан, Иосиф, Вениамин, Неффалим, Гад и Асир.
3 Ana a Yuda anali awa: Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha.
Сыновья Иуды: Ир, Онан и Силом, - трое родились у него от дочери Шуевой, Хананеянки. И был Ир, первенец Иудин, не благоугоден в очах Господа, и Он умертвил его.
4 Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.
И Фамарь, невестка его, родила ему Фареса и Зару. Всех сыновей у Иуды было пятеро.
5 Ana a Perezi anali awa: Hezironi ndi Hamuli.
Сыновья Фареса: Есром и Хамул.
6 Ana a Zera anali awa: Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu.
Сыновья Зары: Зимри, Ефан, Еман, Халкол и Дара; всех их пятеро.
7 Mwana wa Karimi anali Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.
Сыновья Харми: Ахар, наведший беду на Израиля, нарушив заклятие.
8 Mwana wa Etani anali Azariya.
Сын Ефана: Азария.
9 Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali: Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai.
Сыновья Есрома, которые родились у него: Иерахмеил, Арам и Хелувай.
10 Ramu anabereka Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda.
Арам же родил Аминадава; Аминадав родил Наассона, князя сынов Иудиных;
11 Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi,
Наассон родил Салмона, Салмон родил Вооза;
12 Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese.
Вооз родил Овида, Овид родил Иессея;
13 Yese anabereka Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea,
Иессей родил первенца своего Елиава, второго - Аминадава, третьего - Самму,
14 wachinayi Netaneli, wachisanu Radai,
четвертого - Нафанаила, пятого - Раддая,
15 wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide.
шестого - Оцема, седьмого - Давида.
16 Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli.
Сестры их: Саруия и Авигея. Сыновья Саруии: Авесса, Иоав и Азаил, трое.
17 Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli.
Авигея родила Амессу; отец же Амессы - Иефер, Измаильтянин.
18 Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni.
Халев, сын Есрома, родил от Азувы, жены своей, и от Иериофы, и вот сыновья его: Иешер, Шовав и Ардон.
19 Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri.
И умерла Азува; и взял себе Халев жену Ефрафу, и она родила ему Хура.
20 Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli.
Хур родил Урия, Урий родил Веселиила.
21 Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu.
После Есром вошел к дочери Махира, отца Галаадова, и взял ее, будучи шестидесяти лет, и она родила ему Сегува.
22 Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi.
Сегув родил Иаира, и было у него двадцать три города в земле Галаадской.
23 (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.
Но Гессуряне и Сирияне взяли у них селения Иаира, Кенаф и зависящие от него города, - шестьдесят городов. Все эти города сыновей Махира, отца Галаадова.
24 Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa.
По смерти Есрома в Халев-Ефрафе, жена Есромова, Авия, родила ему Ашхура, отца Фекои.
25 Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali: Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya.
Сыновья Иерахмеила, первенца Есромова, были: первенец Рам, за ним Вуна, Орен, Оцем и Ахия.
26 Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu.
Была у Иерахмеила и другая жена, имя ее Афара; она мать Онама.
27 Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa: Maazi, Yamini ndi Ekeri.
Сыновья Рама, первенца Иерахмеилова, были: Маац, Иамин и Екер.
28 Ana a Onamu anali awa: Shamai ndi Yada. Ana a Shamai anali awa: Nadabu ndi Abisuri.
Сыновья Онама были: Шаммай и Иада. Сыновья Шаммая: Надав и Авишур.
29 Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi.
Имя жене Авишуровой Авихаиль, и она родила ему Ахбана и Молида.
30 Ana a Nadabu anali awa: Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana.
Сыновья Надава: Селед и Афаим. И умер Селед бездетным.
31 Ana a Apaimu anali awa: Isi, amene anabereka Sesani. Sesani anabereka Ahilai.
Сын Афаима: Иший. Сын Ишия: Шешан. Сын Шешана: Ахлай.
32 Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa: Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana.
Сыновья Иады, брата Шаммаева: Иефер и Ионафан. Иефер умер бездетным.
33 Ana a Yonatani anali awa: Peleti ndi Zaza. Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli.
Сыновья Ионафана: Пелеф и Заза. Это сыновья Иерахмеила.
34 Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha. Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha.
У Шешана не было сыновей, а только дочери. У Шешана был раб, Египтянин, имя его Иарха;
35 Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi.
Шешан отдал дочь свою Иархе рабу своему в жену: и она родила ему Аттая.
36 Atayi anali abambo ake a Natani, Natani anali abambo ake a Zabadi,
Аттай родил Нафана, Нафан родил Завада;
37 Zabadi anali abambo a Efilali, Efilali anali abambo a Obedi,
Завад родил Ефлала, Ефлал родил Овида;
38 Obedi anali abambo a Yehu, Yehu anali abambo a Azariya,
Овид родил Иеуя, Иеуй родил Азарию;
39 Azariya anali abambo a Helezi, Helezi anali abambo a Eleasa,
Азария родил Хелеца, Хелец родил Елеасу;
40 Eleasa anali abambo ake a Sisimai, Sisimai anali abambo a Salumu,
Елеаса родил Сисмая, Сисмай родил Саллума;
41 Salumu anali abambo a Yekamiya, Yekamiya anali abambo a Elisama.
Саллум родил Иекамию, Иекамия родил Елишаму.
42 Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa: Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni.
Сыновья Халева, брата Иерахмеилова: Меша, первенец его, - он отец Зифа; и сыновья Мареши, отца Хеврона.
43 Ana a Hebroni anali awa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema.
Сыновья Хеврона: Корей и Таппуах, и Рекем и Шема.
44 Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai.
Шема родил Рахама, отца Иоркеамова, а Рекем родил Шаммая.
45 Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri.
Сын Шаммая Маон, а Маон - отец Беф-Цура.
46 Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi.
И Ефа, наложница Халевова, родила Харана, Моцу и Газеза. И Харан родил Газеза.
47 Ana a Yahidai anali awa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi.
Сыновья Иегдая: Регем, Иофам, Гешан, Пелет, Ефа и Шааф.
48 Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana.
Наложница Халевова, Мааха, родила Шевера и Фирхану;
49 Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa.
она же родила Шаафа, отца Мадманны, Шеву, отца Махбены и отца Гивеи. Дочь же Халева - Ахса.
50 Izi zinali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa: Sobala abambo a Kiriati Yearimu,
Вот сыновья Халева: сын Хур, первенец Ефрафы; Шовал, отец Кириаф-Иарима;
51 Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera.
Салма, отец Вифлеема; Хареф, отец Бефгадера.
52 Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi: Harowe, theka la banja la Manahati,
У Шовала, отца Кириаф-Иарима, были сыновья: Гарое, Хаци, Галменюхот.
53 ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa.
Племена Кириаф-Иарима: Ифрияне, Футияне, Шумафане и Мидраитяне. От сих произошли Цоряне и Ештаоляне.
54 Zidzukulu za Salima zinali izi: Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori,
Сыновья Салмы: Вифлеемляне и Нетофафяне, венец дома Иоавова и половина Менухотян - Цоряне,
55 ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.
и племена Соферийцев, живших в Иабеце, Тирейцы, Шимейцы, Сухайцы: это Кинеяне, происшедшие от Хамафа, отца Бетрехава.