< 1 Mbiri 19 >

1 Patapita nthawi Nahasi mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Algún tiempo después, Nahas, rey de los amonitas, murió y su hijo lo sucedió.
2 Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake. Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni kudzamupepesa,
Entonces David dijo: “Seré bondadoso con Hanún, hijo de Nahas, porque su padre fue bondadoso conmigo”. Así que David envió mensajeros para consolarle por la muerte de su padre. Los embajadores de David llegaron a la tierra de los amonitas y fueron a consolar a Hanún.
3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?”
Pero los príncipes amonitas le dijeron a Hanún: “¿De verdad crees que David honra a tu padre enviándote a estos hombres para consolarte? ¿Acaso no crees que han venido sólo a espiar la tierra para encontrar la manera de conquistarla?”
4 Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anawameta ndi kudula zovala zawo pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera ndipo anawabweza kwawo.
Entonces Hanún detuvo a los embajadores de David y los mandó a afeitar, y además les cortó la túnica a la altura de las nalgas. Entonces los envió de vuelta.
5 Munthu wina atafika ndi kufotokozera Davide za anthuwo, iye anatuma amithenga kukakumana nawo, chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”
Luego informaron a David de lo que había sucedido con estos hombres. Entonces David envió mensajeros a los hombres para decirles: “Quédense en Jericó hasta que les crezca la barba, y entonces podrán regresar”.
6 Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, Hanuni ndi Aamoni anatumiza siliva wolemera makilogalamu 34,000 kuti akalipirire magaleta ndi okwerapo ake a ku Mesopotamiya; Aramu-Maaka ndi Zoba.
Entonces los amonitas se dieron cuenta de que realmente habían sido ofensivos con David. Así que Hanún y los amonitas enviaron mil talentos de plata para contratar carros y sus conductores de Harán-naharaim, Harán-maaca y Soba.
7 Iwo analipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi ankhondo ake. Amenewa anabwera ndi kudzamanga misasa yawo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni anabwera kuchokera ku mizinda yawo ndipo anapita kukachita nkhondo.
También contrataron 32.000 carros y al rey de Maaca con su ejército. Vinieron a acampar cerca de Medeba. Los amonitas también fueron llamados desde sus ciudades y se prepararon para la batalla.
8 Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu.
Cuando David se enteró de esto, envió a Joab y a todo el ejército a enfrentarlos.
9 Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene mafumu amene anabwera nawo anali kwa wokha, ku malo wopanda mitengo.
Los amonitas establecieron sus líneas de batalla cerca de la entrada de la ciudad, mientras que los otros reyes que se les habían unido tomaron posiciones en los campos abiertos.
10 Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake; iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu.
Joab se dio cuenta de que tendría que luchar tanto delante como detrás de él, así que escogió algunas de las mejores tropas de Israel y se puso al frente de ellas para dirigir el ataque a los arameos.
11 Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni.
Puso al resto del ejército bajo el mando de Abisai, su hermano. Debían atacar a los amonitas.
12 Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse; koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa.
Joab le dijo: “Si los arameos son más fuertes que yo, ven a ayudarme. Si los amonitas son más fuertes que tú, yo vendré a ayudarte.
13 Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.”
Sé valiente y lucha lo mejor que puedas por nuestro pueblo y las ciudades de nuestro Dios. Que el Señor haga lo que considere bueno”.
14 Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake.
Joab atacó con sus fuerzas a los arameos y éstos huyeron de él.
15 Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai mʼbale wake ndi kulowa mu mzinda. Motero Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.
Cuando los amonitas vieron que los arameos habían huido, también huyeron de Abisai, el hermano de Joab, y se retiraron a la ciudad. Entonces Joab regresó a Jerusalén.
16 Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, pamodzi ndi mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezeri, Sofaki akuwatsogolera.
En cuanto los arameos vieron que habían sido derrotados por los israelitas, enviaron a buscar refuerzos del otro lado del río Éufrates, bajo el mando de Sobac, comandante del ejército de Hadad-Ezer.
17 Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani. Iyeyo anapita kukakumana nawo ndipo anakhala mʼmizere yankhondo moyangʼanana ndipo iwo anamenyana naye.
Cuando le informaron de esto a David, reunió a todo Israel. Atravesó el Jordán y se acercó al ejército arameo, poniendo sus fuerzas en línea de batalla contra ellos. Cuando David entró en combate con ellos, ellos lucharon con él.
18 Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 7,000 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Iye anaphanso Sofaki, mtsogoleri wawo wankhondo.
Pero el ejército arameo huyó de los israelitas, y David mató a 7.000 aurigas y 40.000 soldados de infantería, así como a Sobac, su comandante.
19 Mafumu amene ali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anachita mtendere ndi Davide ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.
Cuando los aliados de Hadad-Ezer se dieron cuenta de que habían sido derrotados por Israel, hicieron la paz con David y se sometieron a él. Como resultado, los arameos no quisieron ayudar más a los amonitas.

< 1 Mbiri 19 >