< 1 Mbiri 18 >
1 Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Iye analanda Gati ndi midzi yake yozungulira mʼmanja mwa Afilistiwo.
2 Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye.
3 Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
4 Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.
5 Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000.
6 Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.
7 Davide anatenga zishango zagolide zimene ankanyamula akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu.
8 Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa.
9 Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri mfumu ya Zoba,
10 anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa.
11 Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki.
12 Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere.
13 Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.
14 Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse.
15 Yowabu, mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika;
16 Zadoki, mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Savisa anali mlembi;
17 Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali alangizi a mfumu.