< 1 Mbiri 15 >
1 Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti.
fecit quoque sibi domos in civitate David et aedificavit locum arcae Dei tetenditque ei tabernaculum
2 Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.”
tunc dixit David inlicitum est ut a quocumque portetur arca Dei nisi a Levitis quos elegit Dominus ad portandum eam et ad ministrandum sibi usque in aeternum
3 Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse mu Yerusalemu kuti abweretse Bokosi la Yehova ku malo amene analikonzera.
congregavitque universum Israhel in Hierusalem ut adferretur arca Dei in locum suum quem praeparaverat ei
4 Iye anayitanitsa pamodzi zidzukulu za Aaroni ndi Alevi:
necnon et filios Aaron et Levitas
5 kuchokera ku banja la Kohati, mtsogoleri Urieli ndi abale ake 120.
de filiis Caath Urihel princeps fuit et fratres eius centum viginti
6 Kuchokera ku banja la Merari, mtsogoleri Asaya ndi abale ake 220;
de filiis Merari Asaia princeps et fratres eius ducenti viginti
7 kuchokera ku banja la Geresomu, mtsogoleri Yoweli ndi abale ake 130;
de filiis Gersom Iohel princeps et fratres eius centum triginta
8 kuchokera ku banja la Elizafani, mtsogoleri Semaya ndi abale ake 200;
de filiis Elisaphan Semeias princeps et fratres eius ducenti
9 kuchokera ku banja la Hebroni, mtsogoleri Elieli ndi abale ake 80;
de filiis Hebron Elihel princeps et fratres eius octoginta
10 kuchokera ku banja la Uzieli, mtsogoleri Aminadabu ndi abale ake 112.
de filiis Ozihel Aminadab princeps et fratres eius centum duodecim
11 Kenaka Davide anayitanitsa ansembe Zadoki ndi Abiatara, ndi Alevi awa, Urieli, Asaya, Yoweli, Semaya, Elieli ndi Aminadabu.
vocavitque David Sadoc et Abiathar sacerdotes et Levitas Urihel Asaiam Iohel Semeiam Elihel et Aminadab
12 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu atsogoleri a mabanja a Alevi ndipo inu ndi abale anu Alevi mudziyeretse nokha ndi kubweretsa Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli ku malo amene ine ndalikonzera.
et dixit ad eos vos qui estis principes familiarum leviticarum sanctificamini cum fratribus vestris et adferte arcam Domini Dei Israhel ad locum qui ei praeparatus est
13 Popeza kuti inu Alevi simunalinyamule poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anatikantha. Sitinafunse momwe tikanachitira monga mmene Iyeyo anafotokozera.”
ne ut a principio quia non eratis praesentes percussit nos Dominus sic et nunc fiat inlicitum quid nobis agentibus
14 Kotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa ndi cholinga chakuti akatenge Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli.
sanctificati sunt ergo sacerdotes et Levitae ut portarent arcam Domini Dei Israhel
15 Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova.
et tulerunt filii Levi arcam Dei sicut praeceperat Moses iuxta verbum Domini umeris suis in vectibus
16 Davide anawuza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo kuti akhale oyimba nyimbo zachisangalalo, zoyimba ndi zida: azeze, apangwe ndi ziwaya za malipenga.
dixit quoque David principibus Levitarum ut constituerent de fratribus suis cantores in organis musicorum nablis videlicet et lyris et cymbalis ut resonaret in excelsum sonitus laetitiae
17 Kotero Alevi anasankha Hemani mwana wa Yoweli; ndipo mwa abale ake anasankha Asafu mwana wa Berekiya; ndipo mwa ana a Merari, abale awo, anasankha Etani mwana wa Kusaya;
constitueruntque Levitas Heman filium Iohel et de fratribus eius Asaph filium Barachiae de filiis vero Merari fratribus eorum Ethan filium Casaiae
18 ndipo pamodzi ndi iwowa abale awo otsatana nawo: Zekariya, Yaazieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli, alonda a pa chipata.
et cum eis fratres eorum in secundo ordine Zacchariam et Ben et Iazihel et Semiramoth et Iahihel et Ani Eliab et Banaiam et Maasiam et Matthathiam et Eliphalu et Macheniam et Obededom et Ieihel ianitores
19 Anthu oyimba aja Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo ankayimba ziwaya za malipenga zamkuwa;
porro cantores Heman Asaph et Ethan in cymbalis aeneis concrepantes
20 Zekariya, Azieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Maaseya ndi Benaya ankayimba azeze a liwu lokwera;
Zaccharias autem et Ozihel et Semiramoth et Iahihel et Ani et Eliab et Maasias et Banaias in nablis arcana cantabant
21 ndipo Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu, Yeiyeli ndi Azaziya ankayimba apangwe a liwu lotsika.
porro Matthathias et Eliphalu et Machenias et Obededom et Ieihel et Ozaziu in citharis pro octava canebant epinikion
22 Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi anali woyangʼanira mayimbidwe; uwu ndiye unali udindo wake pakuti anali waluso pa zimenezi.
Chonenias autem princeps Levitarum prophetiae praeerat ad praecinendam melodiam erat quippe valde sapiens
23 Berekiya ndi Elikana anali olondera pa khomo la bokosilo.
et Barachias et Helcana ianitores arcae
24 Ansembe awa; Sebaniya, Yehosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezara ndiwo ankayimba malipenga patsogolo pa Bokosi la Mulungu. Obedi-Edomu ndi Yehiya analinso alonda a pa khomo la bokosilo.
porro Sebenias et Iosaphat et Nathanahel et Amasai et Zaccharias et Banaias et Eliezer sacerdotes clangebant tubis coram arca Dei et Obededom et Ahias erant ianitores arcae
25 Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera.
igitur David et maiores natu Israhel et tribuni ierunt ad deportandam arcam foederis Domini de domo Obededom cum laetitia
26 Popeza Mulungu anathandiza Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, anapereka nsembe ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndiponso nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.
cumque adiuvisset Deus Levitas qui portabant arcam foederis Domini immolabantur septem tauri et septem arietes
27 Ndipo Davide anali atavala mkanjo wa nsalu yofewa yosalala, monga anavalira Alevi onse amene ananyamula bokosi pamodzi anthu oyimba, ndiponso Kenaniya, amene anali woyangʼanira magulu oyimba. Davide anavalanso efodi ya nsalu yofewa yosalala.
porro David erat indutus stola byssina et universi Levitae qui portabant arcam cantoresque et Chonenias princeps prophetiae inter cantores David autem indutus erat etiam ephod lineo
28 Kotero Aisraeli onse anabweretsa Bokosi la Chipangano la Yehova ndi mfuwu, ndiponso akuyimba zitoliro zanyanga zankhosa zazimuna, malipenga ndi maseche ndiponso akuyimba azeze ndi apangwe.
universusque Israhel deducebant arcam foederis Domini in iubilo et sonitu bucinae et tubis et cymbalis et nablis et citharis concrepantes
29 Bokosi la Chipangano la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikuvina ndi kukondwera, iye ananyoza Davideyo mu mtima mwake.
cumque pervenisset arca foederis Domini usque ad civitatem David Michol filia Saul prospiciens per fenestram vidit regem David saltantem atque ludentem et despexit eum in corde suo