< 1 Mbiri 14 >
1 Hiramu mfumu ya ku Turo inatumiza amithenga kwa Davide pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri a miyala ndi amisiri a matabwa kuti adzamumangire nyumba yaufumu.
2 Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza kwambiri ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.
3 Davide anakwatira akazi ena ambiri ku Yerusalemu ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri.
4 Mayina a ana amene anaberekera ku Yerusalemu anali awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni,
5 Ibihari, Elisua, Elipeleti,
6 Noga, Nefegi, Yafiya,
7 Elisama, Beeliada ndi Elifeleti.
8 Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya dziko lonse la Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anapita kukakumana nawo.
9 Ndipo Afilisti anabwera ndi kulanda zinthu mʼChigwa cha Refaimu.
10 Davide anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka mʼmanja mwako.”
11 Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Mulungu waphwanya adani anga ine ndikuona.” Motero anawatcha malowa Baala Perazimu.
12 Afilisti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide analamulira kuti itenthedwe ndi moto.
13 Nthawi inanso Afilisti anadzalanda katundu mu Chigwamo.
14 Choncho Davide anafunsa Mulungu ndipo Mulunguyo anayankha kuti, “Usapite molunjika, koma uzungulire kumbuyo kwawo. Ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku.
15 Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukapite kukamenyana nawo, chifukwa izi zikasonyeza kuti Mulungu ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.”
16 Kotero Davide anachita zimene Mulungu anamulamulira ndipo anakantha ankhondo a Afilisti njira yonse kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri.
17 Choncho mbiri ya Davide inafalikira dziko lonse, ndipo Yehova anachititsa kuti mayiko ena azimuopa.