< 1 Mbiri 13 >

1 Davide anakambirana ndi akuluakulu ake, atsogoleri a anthu 1,000 ndi atsogoleri a anthu 100.
And David consulted with the captains of thousands and of hundreds, and with every leader.
2 Ndipo anati kwa gulu lonse la Israeli, “Ngati kukukomerani komanso ngati chili chifuniro cha Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kulikonse kumene kuli abale athu ena onse ku dziko lonse la Israeli ndiponso kwa ansembe ndi Alevi amene ali nawo mʼmidzi yawo ndi madera odyetsera ziweto, kuti abwere adzakhale nafe.
And David said to all the congregation of Israel, If it seemeth good to you, and that it is of the LORD our God, let us send abroad to our brethren every where, that are left in all the land of Israel, and with them also to the priests and Levites who are in their cities and common lands, that they may assemble to us:
3 Tiyeni tibweretsenso Bokosi la Mulungu wathu kuno kwathu, pakuti nthawi ya Sauli sitinafunse za bokosili.”
And let us bring again to us the ark of our God: for we enquired not at it in the days of Saul.
4 Gulu lonse linavomereza izi, pakuti anthu onse anaona kuti kunali kofunika kutero.
And all the congregation said that they would do so: for the thing was right in the eyes of all the people.
5 Kotero Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse, kuchokera ku mtsinje wa Sihori ku Igupto mpaka ku Lebo Hamati, kuti abweretse Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriati-Yearimu.
So David gathered all Israel together, from Shihor of Egypt even to the entrance of Hemath, to bring the ark of God from Kirjathjearim.
6 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse anapita ku Baalahi (Kiriati-Yearimu) ku Yuda kukatenga Bokosi la Yehova Mulungu, amene amakhala pakati pa akerubi. Limeneli ndiye Bokosi la Chipangano lomwe limadziwika ndi Dzina lake.
And David went up, and all Israel, to Baalah, that is, to Kirjathjearim, which belonged to Judah, to bring up from there the ark of God the LORD, that dwelleth between the cherubim, whose name is called on it.
7 Iwo anachotsa Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu pa ngolo yatsopano. Uza ndi Ahiyo ndiwo ankayendetsa ngoloyo.
And they carried the ark of God in a new cart out of the house of Abinadab: and Uzza and Ahio drove the cart.
8 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Mulungu, poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.
And David and all Israel played before God with all their might, and with singing, and with harps, and with psalteries, and with timbrels, and with cymbals, and with trumpets.
9 Atafika pa malo opunthira tirigu ku Kidoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire bokosilo, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa.
And when they came to the threshingfloor of Chidon, Uzza put forth his hand to hold the ark; for the oxen stumbled.
10 Yehova anapsera mtima Uza ndipo anamukantha chifukwa chogwira bokosilo. Choncho iyeyo anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.
And the anger of the LORD was kindled against Uzza, and he smote him, because he put his hand to the ark: and there he died before God.
11 Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.
And David was displeased, because the LORD had broken forth upon Uzza: therefore that place is called Perezuzza to this day.
12 Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Mulungu ndipo anafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu lingafike bwanji kwathu?”
And David was afraid of God that day, saying, How shall I bring the ark of God home to me?
13 Iye sanapitenso nalo Bokosi la Mulungu ku Mzinda wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.
So David brought not the ark to himself to the city of David, but carried it aside into the house of Obededom the Gittite.
14 Ndipo Bokosi la Mulungu linakhala mʼbanja la Obedi-Edomu mʼnyumba mwake kwa miyezi itatu ndipo Yehova anadalitsa nyumba yake ndi chilichonse chimene anali nacho.
And the ark of God remained with the family of Obededom in his house three months. And the LORD blessed the house of Obededom, and all that he had.

< 1 Mbiri 13 >