< 1 Mbiri 11 >

1 Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife abale anu.
[達味為王]那時,全以色列人聚集到赫貝龍,來見達味說:「看,我們都是你的骨肉。
2 Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’”
以前連撒烏耳為王時,也是你率領以色列出入征討;並且上主你的天主,也曾對你說過:你應牧養我的百姓以色列,作我的百姓以色列的領袖。」
3 Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.
以色列所有的長老都到赫貝龍來見君王,達味就在赫貝龍,在上主面前同他們立了約;他們便按照上主藉撒慕爾所吩咐的,給達味傅油,立他為以色列王。[佔領耶路撒冷]
4 Davide ndi Aisraeli onse anapita ku Yerusalemu (ku Yebusi). Ayebusi amene ankakhala kumeneko
達味和全以色列人便向耶路撒冷,即耶步斯進發,當時住在那地方的是耶步斯人。
5 anamuwuza Davide kuti, “Simulowa muno.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.
耶步斯的居民對達味說:「你決攻不進此地。」但是,達味卻佔領了熙雍山堡,即今達味城。
6 Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali.
達味曾說過:「誰首先擊敗耶步斯人,誰將升為將領和元帥。」責魯雅的兒子約阿布首先上去了,所以他成了元帥。
7 Tsono Davide anakhazikika mu lingamo, ndipo mzindawu anawutcha Mzinda wa Davide.
達味便住在那山堡內,因此人稱之為達味城。
8 Iye anamanga malo onse ozungulira, kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Ndipo Yowabu anakonzanso mbali ina ya mzindawu.
達味又重修四周城垣,從米羅起,重修一週;城的其餘部份由約阿布修建。
9 Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Wamphamvuzonse.
達味日漸強盛,萬軍的上主與他同在。[達味的將士名單]
10 Awa ndiye anali atsogoleri amphamvu a Davide. Iwo pamodzi ndi Aisraeli onse, anathandiza kulimbikitsa ufumu wake kuti ukwanire madera onse, monga momwe Yehova analonjezera.
以下這些人,是極力擁護達味建國,與全以色列人照上主對以色列所吩咐的,立他為王的主要將士。
11 Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yasobeamu Mhakimoni anali mkulu wa atsogoleri. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300 nthawi imodzi.
達味的將士名單如下:哈革摩尼的兒子依市巴耳,是三傑之首;一次他曾舉起長矛,擊殺了三百人。
12 Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi, mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu.
次為阿曷亞人多多的兒子厄肋阿匝爾,三傑之一,
13 Iye anali ndi Davide ku Pasi-Damimu pamene Afilisti anasonkhana kudzachita nkhondo. Ankhondo anathawa Afilistiwo pamalo pamene panali munda wodzaza ndi barele.
他以前同達味在帕斯達明,培肋舍特人正在那裏集合準備交戰時,【以色列人退卻,他卻固守陣地,擊殺培肋舍特人,直到他手軟無力,粘在刀柄上。上主在那一天完成了一大勝利;民眾返回,隨著他去搶戰利品。再其次是哈辣黎人厄拉的兒子沙瑪,那時培肋舍特人在肋希集合,】在那裏有一塊長滿大麥的田地,民眾由培肋舍特人面前逃走,
14 Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.
他卻立在田間保護了那塊田地,殺敗了培肋舍特人,如此上主又完成了一次大勝利。
15 Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu.
一次三十勇士中,有三位下到阿杜藍山砦附近的岩石裏去見達味,那時培肋舍特人正紮營在勒法因平原,
16 Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu.
同時達味恰在山砦內,培肋舍特人當時也在白冷駐防,
17 Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!”
達味渴望說:「誰能從白冷城門旁的井中,給我打一點水來喝呢﹖」
18 Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova.
那三位勇士就衝過培肋舍特人的營幕,從白冷城門旁的井中打了水,將水取來帶到達味前;但達味不肯喝,反而將水奠於上主前,
19 Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.
說「我的天主決不許我做這事! 我豈能喝這些冒生命危險者的血﹖因為這是他們冒生命危險取來的。」所以他不肯喝。這是這三個勇士所做的。
20 Abisai mʼbale wa Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300. Choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja.
約阿布的兄弟阿彼瑟,是三十勇士的領袖,他揮舞長矛殺了三百人,因此在三十勇士中出了名;
21 Iye analandira ulemu woposa atatuwo. Kotero anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti iyeyo sanali mʼgulu la anthu atatu aja.
他在三十勇士中享有雙重的名望,做了他們的領袖,做了他們的領袖,但尚不及三傑。
22 Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.
約雅達的兒子貝納雅原是卡貝責耳人,是一位英勇大有作為的人,曾擊殺摩阿布人阿黎耳的兩個兒子;又在下雪天,下到旱井裡打死了一隻獅子。
23 Ndipo iye anakanthanso Mwigupto amene anali wotalika mamita awiri ndi theka. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo wofanana ndi ndodo yowombera nsalu mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.
他也曾打死了一個埃及巨人。這埃及人人身高五肘,手中拿著粗如織布機軸的長矛,貝納雅下去,手中僅拿著一根棍杖,從那埃及人手中,把長矛奪了過來,用那長矛將他殺死。
24 Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja.
這是約雅達的兒子貝納雅所做的事。因此在三十勇士中出了名。
25 Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.
他比三十勇士更有名望,但尚不及三傑。達味派他作侍衛長。
26 Ankhondo amphamvuwa anali: Asaheli mʼbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
其餘的勇士:有約阿布的兄弟阿撒耳,白冷人多多的兒子厄耳哈難,
27 Samoti Mharori, Helezi Mpeloni.
哈洛得人沙摩特,帕耳提人赫肋茲,
28 Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiezeri wa ku Anatoti,
特科亞人依刻士的兒子依辣,阿納托特人阿彼厄則爾,
29 Sibekai Mhusati, Ilai Mwahohi,
胡沙人息貝開,阿曷亞人衣來,
30 Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa,
乃托法人瑪哈賴,乃托法人巴阿納的兒子赫肋得,
31 Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini, Benaya Mpiratoni,
本雅明族基貝亞人黎拜的兒子依泰、丕辣通人貝納雅,
32 Hurai wa ku zigwa za Gaasi, Abieli Mwaribati,
加阿士士溪人胡賴,貝特阿辣巴人阿彼巴耳,
33 Azimaveti Mbaharumi, Eliyahiba Msaaliboni,
巴胡陵人阿次瑪委特,沙阿耳賓人厄里雅巴,
34 ana a Hasemu Mgizoni, Yonatani mwana wa Sage Mharari,
基宗人雅笙,哈辣黎人沙革的兒子約納堂,
35 Ahiamu mwana wa Sakari Mharari, Elifali mwana wa Uri,
哈辣黎人撒加爾的兒子阿希楊,烏爾的兒子厄里法耳,
36 Heferi Mmekerati, Ahiya Mpeloni,
默革辣人赫費爾,基羅人阿希雅,
37 Heziro wa ku Karimeli Naara mwana wa Ezibai,
加爾默耳人赫茲賴,厄次拜的兒子納阿賴,
38 Yoweli mʼbale wa Natani, Mibihari mwana wa Hagiri,
納堂的兄弟約厄耳,哈革黎的兒子米貝哈爾,
39 Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya.
阿孟人責肋克,貝厄洛特人納赫賴,他是責魯雅的兒子約阿布的執戟者,
40 Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,
雅提爾人依辣,雅提爾人加勒布,
41 Uriya Mhiti, Zabadi mwana wa Ahilai,
赫特人烏黎雅,阿赫來的兒子匝巴得,
42 Adina mwana wa Siza Mrubeni, amene anali mtsogoleri wa Arubeni ndi anthu makumi atatu pamodzi naye,
勒烏本人史匝的兒子阿狄納,他是勒烏本人的首領,有三十個人跟隨他,
43 Hanani mwana wa Maaka, Yehosafati Mmitini,
瑪加的兒子哈南,默騰人約沙法特,
44 Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyeli ana a Hotamu Mwaroeri,
阿市塔洛特人烏齊雅,阿洛厄爾人曷堂的兒子沙瑪和耶厄耳,
45 Yediaeli mwana wa Simiri, ndi Yoha Mtizi mʼbale wake,
提漆人史默黎的兒子耶狄阿耳和他的兄弟約哈,
46 Elieli Mhavati, Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, Itima Mmowabu,
瑪紅人厄里耳,厄耳納罕的兒子耶黎拜和約沙委雅,摩阿布人依特瑪,
47 Elieli, Obedi ndi Yaasieli Mmeobai.
厄里耳,敖貝得和祚巴人雅息耳。

< 1 Mbiri 11 >