< Titus 3 >
1 Ba de ya bi wa ba bahtu mba nu beh chua mba wo tere mba.
Uwakumbutse anthu kuti azigonjera oweruza ndi olamulira, aziwamvera ndi kukhala okonzeka kuchita chilichonse chabwino.
2 U ka llah ni bawu du mba na mere idi na mba kana sen iyu ni idina. du mba zo mba ni mi sisunron.
Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
3 Na kima khi na sun ni buh na khi na kpakyeme ni kpabuna.
Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake.
4 Ni toh kima Irji a ji ikpan shishi ye.
Koma kukoma mtima ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chitaonekera,
5 Ana hei ni tu indu dedema wa khi ti na. irji a glata ni iyi Yesu
Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera
6 irji a nuta Ibrji Tsra tsra gbugbuu ni tu Yesu. Wa a ye kpata chuwoa.
amene anatipatsa mowolowamanja kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu,
7 A teenaki du khi sun kasaisai ni seisei. (aiōnios )
kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (aiōnios )
8 I wayi a hi ton du jaji. Mei sun du tere tere ki bei wa ba kpa Irji teh u jaji mba zere zere u dedema.
Mawuwa ndi okhulupirika ndipo ine ndikufuna kuti iwe utsindike zinthu izi, kuti amene akhulupirira Mulungu adzipereke kuchita ntchito zabwino. Zinthu izi ndi zabwino kwambiri ndi zopindulitsa kwa aliyense.
9 U ka domeh ni seh yun u kukulu. ni mbala gye gyere. U sun yun ni tu ibeh U Irji. Ikpi mba ki mba na no ta ipkina.
Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kuwerengawerenga mndandanda wa mibado ya makolo, mikangano ndi mitsutso pa za Malamulo, chifukwa zimenezi ndi zosapindulitsa ndi zopanda pake.
10 Kahme ni idi wa ani chah mba wa ana son tsrei tsrei niyi na.
Munthu woyambitsa mipatuko umuchenjeze koyamba, ndiponso umuchenjeze kachiwiri. Kenaka umupewe.
11 Bika toh nji kima ana zren tsrei tsrei na.
Iwe udziwe kuti munthu wotero ngosokoneza ndi wochimwa, ndipo akudzitsutsa yekha.
12 Uwa me ton Artemas ka Tychikus ni wu, ndu ye gbagbla ni me ni Nicopolis ndu su son ni men.
Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira.
13 U tru Zinas gbagbla, wa a to mlazren ni Appolos ni kon wa ba he ni
Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu.
14 A bi duu ijinbu idi bu khi yah de te kpi dedema da yibi ulu'a ani ye gba gbla du mba na sun hlegana.
Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.
15 Bei wa'a ba hey ni mei mba chiu. chi bei wa'a mba kpakyeme ni ta ni mi itere u jaji. zeze i irji du sun ni yi wa wuu.
Onse amene ali ndi ine akupereka moni. Upereke moni kwa amene amatikonda ife mʼchikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.