< Mark 4 >

1 Yesu ni mu mummlan a hla tre ma ni gbugbu ndi waba shuti ni Yun nei. A lude ri ni mi gyue ni mi-nei.
Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi.
2 A lla tre ma u-jaji gbugbu da ka yiyi ani.
Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati:
3 Wo-me, idi uron a ban ibi hichu ni rjumaa
“Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake.
4 a chu bari ba kuhle ni kon u chichen ba tanri
Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya.
5 bari ba khule ni tu han iwa ama hei mi meme gbugbun a warju.
Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri.
6 Irji rju hongan wa kue niwa in-jah ma na gburonkonna.
Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu.
7 Bari ba kuhle ni zahchon, I Chon ba gburon ti rigra da k tiwu wa ti me me.
Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula.
8 Bari kuma ku “lle ni “llar meme didima da gburon na ni sho bari, I wulon iknutra, bari I wulon ikpu tanne, bari I wulon kpu wulon.
Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”
9 Yesu tre indi wa a hei ton u wo kawo
Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”
10 Wa Yesu a ye he ni kriji ma bi wa ba hei niki ni mimriko ma wulon don ha, ba miyen tu tree ka yiyi a.
Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo.
11 A biyi yi ba “llar you wawu multi Irji wa, a ririn, mibiwa ba he nira ba tree ni ka yiyin me.
Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo:
12 Ni duba ye ama da na toh na ni duba wo “llan da na toh “llan na I ba wo na kame ye Irji ni wuru “lle ni bwu.
kotero kuti, “‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu, kumva mudzamva koma osamvetsetsa, kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’”
13 A miyen ba bina to tu itre u ka you na?
Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse?
14 Bi ya di bi to wawu u?
Wofesa amafesa mawu.
15 Idi ichu a ni chu tre.
Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo.
16 Ni tu kon ba a bubu wa ba chutre iba wo meme brji a ye, wa vuba kpa tre wa ba chusa.
Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe.
17 Bana he ni ja na ni mi bana. Ama ba vu sunron mu ni mi iton fie me, na joku ni ton uya.
Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira.
18 Bi wa ba kpa tre na kalle ni
Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu;
19 tu gbi gbugbulu yo khlen, iko bari kpii bari naki, iri mba ba chu wa a khule ni chon. (aiōn g165)
koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. (aiōn g165)
20 Bi wa ba kpatre rji da vusuron na ni ji ndi ye nitre rji baba yi ba ichu wa kulle ni meme didi wa a ni klo 30-30 60-60 100-100
Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”
21 A miyen ba, Indi ba zi fitila ni mi sisen ko ba zi ni zah tebru? Ba zi nitu tebur, di du kpan ni Indi bi koh.
Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake?
22 Ikperi na riri na, see ka he ni rira ni ndi ba ka to na hlar.
Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera.
23 Indi wa ahei niton u wo ka wo.
Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”
24 A hla bawa, srenton ni wo kpie wa bi wo. Kongo wa wu tsar niwu, ni ki ba tsar niwu.
Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri.
25 Indi wa a heiwu, ba ka fon surwu Indi wa ana hei niwuna, baka vukpa fie wa a hei niwua.
Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”
26 A tree, mulki Irji a hei nawa indi ani ban bikpie hichu nimeme.
Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka.
27 Indi ni kruna, na shime ni rji, biri nirju na gbrun, wana tohna.
Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira.
28 Menme nina biri kima ani yarbe ku nira, ngwugwu ka fu wa ka gbrun nikle ma da ti wolo.
Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo.
29 I dan biri a weri u ba cham.
Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
30 Ki ya tree mulki rji ahe naki kā ki tsar ba bawu?
Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera?
31 Ga aheifieme na wolo mustard wa i dan u chu ani rju da gburon.
Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka.
32 Har chinchen baka son ni wuma.
Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”
33 Naki tre mba ni kayiyi ni kon gbubu'u.
Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa.
34 Ni kogie a tre ni ba wu ni ka yiyi duba tohtre a.
Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.
35 Ni yalu chachuki a tree diba zah gran hi komu.
Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.”
36 I ba lude niwume a ni mique na ka ndiba don.
Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye.
37 Se ihen lude ni gbegbelen na wuru man sur ni mi guea ta shu.
Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira.
38 Wa si kurna ni kogon mi gue iba shemme u du lude na ya duna kur kpahlena ndi ba ba kuhlema.
Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”
39 Iwa lude da yarhan ni kikle gwugwu mba ima duba son nigbagbi shishiman ba chu
Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
40 A miyen ba, age nuyi sisiri? Har zizan bina hei ni bangaiskiya na?
Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”
41 Iba tie sisiri, adi a indi birimen nayi a tre ni gwugwu ba I ma u ba wo niwu.
Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”

< Mark 4 >