< Mark 14 >

1 a don viha duba ti ngan u passover idi mba ngan u bredi wa asa binikoh bi ton du irji baba bi han ibe ba sun diba yib yesu da wuu
Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha.
2 ba tre ana hei nitoh gan nadutsi kanalude ni tsutsu ndi na
Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”
3 da yesu a hei nikoh siman u lo shia basi rhi biri u wa hri a riye niwu da ji kpalaba alabaster u klen ma wa ba you di nard ayar kpalaba da kayen a sur nitu yesu
Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.
4 ndi bari ha hei niki da tifu ni kpaba da tre ai higye kpei wa iwa yi tidu migye
Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa?
5 smsl du bs ban tutate a le ru kle wa ani kai deri tra wa ba zo biti ya ba tre a
Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.
6 yesu ka tre ahi kpei didima ati nimu
Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino.
7 bihei nibi yaba chachuu wadi ko ni tan biya zoba ama bina hei ni me chachuu na
Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse.
8 iwayi ti kpe wa a iya ti a asur turare don chachu rhumu
Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda.
9 misi hla tre jaji niyuu konitsen ba hla tre irji nimi gbugbulu sei ba hla ikpie wadi wayi ti ko ni kogon kuq
Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”
10 sei vre koh ma rhi wa ba you di Yohuda iskarioti ruhu hini bi ton du irji don du vuu noba
Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu.
11 da bi toh du irji ba woh da ngri kpukpome niwu da you iyei ba no kle wa sima ni wa koh wa di aru vu yesu noba
Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.
12 niyi u mumla u berdi wa ana saana waba nha yi krju ton ngla lah tre ntoh u inga ni sei nisei u mrikohma ba miyei anitse ki hi mla bubu u ri biria?
Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”
13 atohmrikohma hari da hla bawu duba hi mi gbu ndiri hluiri u fo ma bi aka hu hi
Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye.
14 ahi ta rhi nikoh bi ka hu idia hla u di la di ukoa malla tre ikoh mu wa mirhi biri baba mrikohmu?
Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’
15 anitsro yi kikla mikoh wu koshu waba mlati bikah mla ti ni tawu
Iye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.”
16 mrikoh ma ba hi ni mi gbua da ka toh inpie da a tre hei nakima da ti birhi ketarewa
Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.
17 da yalu ti wa ji mrikohma tsoh hi
Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo.
18 da ba kru da si rhibiri nitu tabur yesu katre jaji mi si hla niyi wu iri nimi bi nivu me noba
Pamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.”
19 bayi ni suron ba da nimiyei ahime?
Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”
20 yesu kasa nibawu wa da si you woh ni me ni gbugban
Iye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine.
21 ivrendi nihi na a han niyuma iya ndikima wadi ani vu yesu noba abi di na grhi ndi kimana
Mwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
22 bashei ninu rhi biri yesu ban bresdis da ti lulu you nibredia da mere ga niba wu datre wayi hi nma kpamu
Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”
23 a bangbaju datre
Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.
24 wayi a hu yimu wa mi sur iyieu ni yuwu wa ani kahle nigbubuu baka so wawu bauu
Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri.
25 me hla tre jaji mina la somi klo kukru gana sei ivi wa mi so ni mikoh irji
Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”
26 bayou sei da rhu hini gbulu olives
Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.
27 yesu hla ni bawu wawubi bi joku yada ba han iq mi vu ndiu krhutimaa iq u itima bavra ni kagakaga
Yesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “‘Kantha Mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’
28 bata zume lude in mi hi Galilee guchi niyuu
Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”
29 Bitrus kahla ru yesu ko ba hi kpamba wawuu ine mina hina
Petro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.”
30 yesu ka hla u nichu luwa du gba du tub tup kpu u kpa tron di u una tohme na in kpu tra
Yesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.”
31 Bitrus tre ko mi qu bu wu mina tre dimina toh una baka you inveu ni yesu wawuba wu
Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.
32 ba ye ni bubu ri you di Gethsemane yesu ka hla ni mrikoma kuson wayi ime me hi bre
Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.”
33 a banBitrus Yakub u Yohana ni kpama a rimer da ni damu
Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima.
34 ahla bawu isuromu ni lome har na u qu ki mai di ta gbe har hi ni kuqu
Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.”
35 yesu for zre fime da ku joku ni meme da bre inde aru bie ka wur ton a hle niwawu
Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire.
36 datre abba ti bu ikpi ba yereyere niwu wuka cu gbaju yi ru ni mu aman ana ti muna ahi wume
Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”
37 aka kam ye da yetoh ba basi kruna da miye Bitrus sima bi si kruna? koh niton riri me bi na iya gben na?
Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi?
38 gbien di bre don di na joku nimi lah tre na isuron a nyme ama ika a si
Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”
39 a la hi da tretre wu mumla gari
Kenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi.
40 da aka kam ye da toh basi kruna na u mumla shishi ba a ron u bana toh kpie wa ba hla wuna
Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.
41 akma ye kpututra da miye ba bu risi kurnari di ni siri? atsra no toh a yeye to bavu vre ndi you ni woh bi latre
Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa.
42 lude kinihi to idi wa a vu me ni noba a he weiweire
Nyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!”
43 a sihei nimi tre a u Yahuda iri ni mi a aye ni gbugbu idi ni ba ijin gban nibi toh du irji ni bi han be ni bi nikoh
Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.
44 indi wa a vu haba a guci tsro ba woh ni wuye Biti toh diwa mi sumbace u wa wu yi bika vu di griwu di hi ba ba bi gadi
Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.”
45 da Yahuda ye ahi ni yesu gbla me da you
Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona.
46 di ranni da rhugume ni u indi ba kavu na ki u ri ni ciki mba waa kli niba kia
Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga.
47 chu inji gbama da chu vuvu to diri ni mi biwu niko pristoci ba
Kenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake.
48 yesu a mieye ba bi ye vu me na diwu yib ni ji gban ni kpe iku
Yesu anati, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira, kuti mubwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira?
49 mitahei niyi chachuu dita bla tre irji ni yiu nitra rji bi na vu me na a hei na ki don du tre rji cika
Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.”
50 duka bi wa ba na hei ni yesu ba tsutsu da kaa don niu ba tsutsu hi kpaba
Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.
51 vivren nze ri wa alo vi gbajanklo u kaakpa megen a sia hu e mri nzeba ba yo wo vuu
Mnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira,
52 a ka gbanjanklo chuwo ni bawu nda tsutsu ru ni ngbre
anathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo.
53 niki ba nki yesu hini ninko prist nikima ba kikle prists ba ni chiche mba bi nha ba zontu kii nha niwu
Anamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi.
54 e Bitrus a nha huba kari ni tra nkon wu nikon prist a ndaka kuson ni ba mriko nduba nda sia mu kpama ni lu
Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.
55 nikon prist baba bison nda bla tre ni trankon a ba wa biwa ba njitre kpewa bato nitu yesu ni duba wuu nda wa hama
Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse.
56 gbugbu mbawu ba sia blatre che nituma e nyu bitre ba ti nkankan ndana hu nyu ri na
Ambiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane.
57 niki bari ba la lu kri nda bla tre che nituma ndi
Kenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti,
58 ki wowu a sia bla ndi wawu ni zii hekali wa ba me ni wondi nda ni mi vi tra la me ri hama ni tindu ni wondi
“Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’”
59 nikima ngame bi tre ba nyumba ana hu nkon riri na
Ngakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane.
60 ninkon prist a lu kri nimimba nda yesu ndi wuna he ni kpe wu sa bawu na? ni tutre wa bi nu shaida biyi basi bla nitume a?
Kenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?”
61 nikima a kri gbangbi ndana sa na ninkon prist a la myeu ndi wuyi wu kristi vren u wa ba ti lulu zanzan niwua?
Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe. Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?”
62 yesu a trendi ahi me ngame bi to vreninji si son ni wo korhi u gbengble nda si ye nimi klalu wu shulu
Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”
63 niki ninkon prist a yba nklon kpama nda tre ndi kila wa saidu u ngye gari?
Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso?
64 bi wo tre wu kpande irji timeme kimbi bi to ni he? wawumba ba nyme ndi latrema a tsra du ba wuu
Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?” Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa.
65 bari ba lu si junte ni vra nituma nda ni ka shishima ndani tsiwu nda hlawu ndi du nran tre e mrikondumba ba tsi ni ndawomba
Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.
66 niwa Bitrus a son ni meme ni ra koa ninrenwa ri wu tindu niko ninkon prist
Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera.
67 a to Bitrus si son si si zu isi ni yesu u Nazarat
Ataona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa. Iye anati, “Iwenso unali pamodzi ndi Mnazareti, Yesu.”
68 a kpa tre ndi mina to na nina to tu kpewa wu tre a na wa a rhu hi ni kalhan e igbaa a tbu
Koma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata.
69 vrenwa wu ndu ri a too ngari nda lu si bla ni biwa ba ki whi niki ndi iwayi hi rimba
Pamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.”
70 a la kpa tron ngari nton fiime ka huki biwa ba ki nhan niki ba la tre ni Bitrus ndi ahi janji wu ri mba nitu wu ndi u Galilee e lpn nyu me kpanyeme nikima
Anakananso kachiwiri. Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.”
71 niki a lusi yoban ndani shirhi ni kpama ndi mina to iguyi wa bisi tre nituma na
Iye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.”
72 igba a la tbu nkpu u ha rhi du igba tbu nkpu ha wu shirhi kpatron ni me nkpu tra niwa a rhimren ni kima a ybo yi
Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.

< Mark 14 >