< 1 Yohana 5 >
1 Indi wa akpa yiem di yesu a kristi bagrji u rji ni Irji inde di wa a kpayiem ni ti'a naki ani yiem ni vre wa ba grji ni u.
Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake.
2 Ahe naki ki toh di ki kpayiem mri Irji inde ki yiem ni Irji di zi tre ma.
Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake.
3 Naki wa yi a yiem u'Irji: wa ki yiem ni tre ma kuma itre ma ba na u' di'na.
Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa,
4 Du ndi wa ba grji rji ni Irji ani zan gbengbenlen gbugbulu. Nakima hi nasara wa a zan gbengbenlen gbugbulu wato jaji bu.
chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi.
5 Ahi wu han wa a zan gbengbenlen gbugbulu'a? Ahi ndi wa a kpa yeim di yesu a vre Irji.
Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
6 Wa yi i, hi wa aye ni ma mba yin Yesu kristi aye ni ma ni kangrji na, ama ni ma ba yin.
Uyu ndiye anabwera mwa madzi ndi magazi, ndiye Yesu Khristu. Sanabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi magazi. Ndipo ndi Mzimu Woyera amene akuchitira umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndi choonadi.
7 A baba tra wa ba kpa yiem:
Pakuti pali atatu amene amachitira umboni.
8 Ni Ruhu ni ma u ni yin. Bi yi tra ba ti yaje jeniya ni kpa mba. Ifiift Greek bi sen ba han kpi didima.
Mzimu Woyera, madzi ndi magazi; ndipo atatu amavomerezana.
9 Inde ki kpa jaji u ndi, jaji u Irji a zan wayi hi testimony u' Irji wa a kpa yeim ni vre ma.
Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake.
10 Du ndi wa a kpayeim ni vre Irji ahei ni testimony ni suron ma indi wa ana kpayeim ni Irji na a kma u'ti ndi u' che don ana kpayeim ni testimony wa Irji no nitu vre ma na.
Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake.
11 Testimony a wa yi, Irji nota son u'tutrun u rei ki hei ni mi vre ma. (aiōnios )
Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. (aiōnios )
12 Indi wa ahei ni vre'a ahei ni rei. Indi wa ana hei ni vre Irji na ana hei ni rei na.
Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.
13 Mi han kpie bi i ni yu'u du yi toh di bi hei ni rei u' tutrun ni ndi wa kpa yeim ni de vre Irji. (aiōnios )
Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha. (aiōnios )
14 Wa yi hi gbengbenlen wa ki hei ni u, du ikpie wa ki miye wa hei di di ni mere ma ani woh ta.
Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera.
15 Naki inde ki toh dani wota ko ahi gye ki miye, ki ka toh di ikpie wa ki miye ki kpa ye.
Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.
16 Inde ndi'a atoh vayi si ti latre wa ana tsra u' que na, wa ka bre Irji ni no rei, me gomace ni bi wa latre mba na kai u que na, Lahtre ri hei wa atsra u que, mina tre di du bre nitu kima na.
Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi.
17 Dukikpie u' meme ma a lahtre na ki lahtre wa ana tsra'u que na.
Chilichonse chosalungama ndi tchimo ndipo pali tchimo losadzetsa imfa.
18 Kitoh du ndi wa ba grji'u rji ni Irji ana ti lahtre na. Naki u wa ba grji rji ni Irji gyegyere u bi ibrji na iya da ti u meme na.
Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze.
19 Ki toh di kita ki rji ni Irji kuma kitoh di gbugbulu wawu ahei ni mi gbengbenlen bi brji.
Tikudziwa kuti ndife ana a Mulungu ndi kuti dziko lonse lapansi lili pansi pa ulamuliro wa woyipayo.
20 Na ki ki to di ver Rji ye buh shishi ni ta u di wa yi hi jaji, ki hei ni wu wa wu hi hi jaji ni mi ver ma Yesu kristi. Iwayi yi a Rji u jaji u son kibo (tutrun). (aiōnios )
Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha. (aiōnios )
21 Imir na cib hi ni bi birji na
Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.