< ܡܪܩܘܣ 5 >

ܘܐܬܐ ܠܥܒܪܐ ܕܝܡܐ ܠܐܬܪܐ ܕܓܕܪܝܐ 1
Ndipo anawoloka nyanja napita ku dera la Gerasa.
ܘܟܕ ܢܦܩ ܡܢ ܤܦܝܢܬܐ ܦܓܥ ܒܗ ܡܢ ܒܝܬ ܩܒܘܪܐ ܓܒܪܐ ܕܐܝܬ ܒܗ ܪܘܚܐ ܛܢܦܬܐ 2
Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye.
ܘܥܡܪ ܗܘܐ ܒܝܬ ܩܒܘܪܐ ܘܒܫܫܠܬܐ ܐܢܫ ܠܐ ܡܫܟܚ ܗܘܐ ܠܡܐܤܪܗ 3
Munthuyu amakhala ku manda, ndipo panalibe amene akanatha kumumanganso ngakhale ndi unyolo.
ܡܛܠ ܕܟܠ ܐܡܬܝ ܕܒܤܘܛܡܐ ܘܒܫܫܠܬܐ ܡܬܐܤܪ ܗܘܐ ܫܫܠܬܐ ܡܬܒܪ ܗܘܐ ܘܤܘܛܡܐ ܡܦܤܩ ܗܘܐ ܘܠܐ ܐܢܫ ܡܫܟܚ ܗܘܐ ܠܡܟܒܫܗ 4
Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa.
ܘܒܟܠ ܙܒܢ ܒܠܠܝܐ ܘܒܐܝܡܡܐ ܒܒܝܬ ܩܒܘܪܐ ܘܒܛܘܪܐ ܐܝܬܘܗܝ ܗܘܐ ܘܩܥܐ ܗܘܐ ܘܡܨܠܦ ܢܦܫܗ ܒܟܐܦܐ 5
Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala.
ܟܕ ܚܙܐ ܕܝܢ ܠܝܫܘܥ ܡܢ ܪܘܚܩܐ ܪܗܛ ܤܓܕ ܠܗ 6
Ataona Yesu ali patali, anathamanga nagwa pa mawondo ake pamaso pake.
ܘܩܥܐ ܒܩܠܐ ܪܡܐ ܘܐܡܪ ܡܐ ܠܝ ܘܠܟ ܝܫܘܥ ܒܪܗ ܕܐܠܗܐ ܡܪܝܡܐ ܡܘܡܐ ܐܢܐ ܠܟ ܒܐܠܗܐ ܕܠܐ ܬܫܢܩܢܝ 7
Iye anafuwula kwambiri nati, “Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!”
ܐܡܪ ܗܘܐ ܠܗ ܓܝܪ ܦܘܩ ܡܢ ܒܪܢܫܐ ܪܘܚܐ ܛܢܦܐ 8
Pakuti Yesu anati kwa iye, “Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!”
ܘܫܐܠܗ ܐܝܟܢܐ ܫܡܟ ܐܡܪ ܠܗ ܠܓܝܘܢ ܫܡܢ ܡܛܠ ܕܤܓܝܐܐ ܚܢܢ 9
Ndipo Yesu anamufunsa iye, “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri.”
ܘܒܥܐ ܗܘܐ ܡܢܗ ܤܓܝ ܕܠܐ ܢܫܕܪܝܘܗܝ ܠܒܪ ܡܢ ܐܬܪܐ 10
Ndipo anamupempha Yesu mobwerezabwereza kuti asazitulutse mʼderalo.
ܐܝܬ ܗܘܐ ܕܝܢ ܬܡܢ ܠܘܬ ܛܘܪܐ ܒܩܪܐ ܪܒܬܐ ܕܚܙܝܪܐ ܕܪܥܝܐ 11
Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi.
ܘܒܥܝܢ ܗܘܘ ܡܢܗ ܗܢܘܢ ܫܐܕܐ ܘܐܡܪܝܢ ܫܕܪܝܢ ܥܠ ܗܢܘܢ ܚܙܝܪܐ ܕܒܗܘܢ ܢܥܘܠ 12
Ziwandazo zinapempha Yesu kuti, “Titumizeni pakati pa nkhumbazo; ndipo mutilole tilowe mwa izo.”
ܘܐܦܤ ܠܗܘܢ ܘܢܦܩ ܪܘܚܐ ܗܠܝܢ ܛܢܦܬܐ ܘܥܠ ܒܚܙܝܪܐ ܘܪܗܛܬ ܗܝ ܒܩܪܐ ܠܫܩܝܦܐ ܘܢܦܠܬ ܒܝܡܐ ܐܝܟ ܬܪܝܢ ܐܠܦܝܢ ܘܐܬܚܢܩܘ ܒܡܝܐ 13
Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.
ܘܗܢܘܢ ܕܪܥܝܢ ܗܘܘ ܠܗܘܢ ܥܪܩܘ ܘܐܡܪܘ ܒܡܕܝܢܬܐ ܘܐܦ ܒܩܘܪܝܐ ܘܢܦܩܘ ܠܡܚܙܐ ܡܕܡ ܕܗܘܐ 14
Omwe amaweta nkhumbazo anathawa ndi kukawuza anthu za izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi, ndipo anthu anapita kukaona zomwe zinachitika.
ܘܐܬܘ ܠܘܬ ܝܫܘܥ ܘܚܙܐܘܗܝ ܠܗܘ ܕܫܐܕܘܗܝ ܟܕ ܠܒܝܫ ܘܡܢܟܦ ܘܝܬܒ ܗܘ ܕܐܝܬ ܗܘܐ ܒܗ ܠܓܝܘܢ ܘܕܚܠܘ 15
Atafika kwa Yesu, anaona munthu amene anagwidwa ndi ziwanda zambiri uja atakhala pansi pomwepo, atavala, ndipo ali bwinobwino. Iwo anachita mantha.
ܘܐܫܬܥܝܘ ܠܗܘܢ ܗܢܘܢ ܕܚܙܘ ܕܐܝܟܢܐ ܗܘܐ ܠܗܘ ܕܫܐܕܘܗܝ ܘܐܦ ܥܠ ܗܢܘܢ ܚܙܝܪܐ 16
Amene anaona zimenezi anawuza anthu zomwe zinachitika kwa munthu wogwidwa ndi ziwandayo ndipo anawawuzanso za nkhumbazo.
ܘܫܪܝܘ ܒܥܝܢ ܡܢܗ ܕܢܐܙܠ ܠܗ ܡܢ ܬܚܘܡܗܘܢ 17
Ndipo anthu anayamba kumupempha Yesu kuti achoke mʼdera lawo.
ܘܟܕ ܤܠܩ ܠܤܦܝܢܬܐ ܒܥܐ ܗܘܐ ܡܢܗ ܗܘ ܕܫܐܕܘܗܝ ܕܥܡܗ ܢܗܘܐ 18
Yesu akulowa mʼbwato, munthu amene anagwidwa ndi ziwanda uja anamupempha kuti apite nawo.
ܘܠܐ ܫܒܩܗ ܐܠܐ ܐܡܪ ܠܗ ܙܠ ܠܒܝܬܟ ܠܘܬ ܐܢܫܝܟ ܘܐܫܬܥܐ ܠܗܘܢ ܡܕܡ ܕܥܒܕ ܠܟ ܡܪܝܐ ܘܕܐܬܪܚܡ ܥܠܝܟ 19
Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.”
ܘܐܙܠ ܘܫܪܝ ܡܟܪܙ ܒܥܤܪܬ ܡܕܝܢܬܐ ܡܕܡ ܕܥܒܕ ܠܗ ܝܫܘܥ ܘܟܠܗܘܢ ܬܡܝܗܝܢ ܗܘܘ 20
Pomwepo munthuyo anapita nayamba kuwuza anthu a ku Dekapoli zinthu zimene Yesu anamuchitira. Ndipo anthu onse anadabwa.
ܘܟܕ ܥܒܪ ܝܫܘܥ ܒܤܦܝܢܬܐ ܠܗܘ ܥܒܪܐ ܬܘܒ ܐܬܟܢܫܘ ܥܠܘܗܝ ܟܢܫܐ ܤܓܝܐܐ ܟܕ ܐܝܬܘܗܝ ܥܠ ܝܕ ܝܡܐ 21
Yesu atawolokeranso pa bwato kupita mbali ina ya nyanja, gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira. Ali mʼmbali mwa nyanja,
ܘܐܬܐ ܚܕ ܕܫܡܗ ܝܘܐܪܫ ܡܢ ܪܒܝ ܟܢܘܫܬܐ ܘܟܕ ܚܙܝܗܝ ܢܦܠ ܠܘܬ ܪܓܠܘܗܝ 22
mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake,
ܘܒܥܐ ܗܘܐ ܡܢܗ ܤܓܝ ܘܐܡܪ ܠܗ ܒܪܬܝ ܒܝܫܐܝܬ ܥܒܝܕܐ ܬܐ ܤܝܡ ܐܝܕܟ ܥܠܝܗ ܘܬܬܚܠܡ ܘܬܚܐ 23
ndi kumudandaulira kwambiri nati, “Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo.”
ܘܐܙܠ ܥܡܗ ܝܫܘܥ ܘܕܒܝܩ ܗܘܐ ܠܗ ܟܢܫܐ ܤܓܝܐܐ ܘܚܒܨܝܢ ܗܘܘ ܠܗ 24
Ndipo Yesu anapita naye. Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye.
ܐܢܬܬܐ ܕܝܢ ܚܕܐ ܕܐܝܬܝܗ ܗܘܬ ܒܡܪܕܝܬܐ ܕܕܡܐ ܫܢܝܢ ܬܪܬܥܤܪܐ 25
Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri.
ܐܝܕܐ ܕܤܓܝ ܤܒܠܬ ܡܢ ܐܤܘܬܐ ܤܓܝܐܐ ܘܐܦܩܬ ܟܠ ܡܕܡ ܕܐܝܬ ܠܗ ܘܡܕܡ ܠܐ ܐܬܥܕܪܬ ܐܠܐ ܐܦ ܝܬܝܪܐܝܬ ܐܬܐܠܨܬ 26
Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe.
ܟܕ ܫܡܥܬ ܥܠ ܝܫܘܥ ܐܬܬ ܒܚܒܨܐ ܕܟܢܫܐ ܡܢ ܒܤܬܪܗ ܩܪܒܬ ܠܠܒܘܫܗ 27
Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake,
ܐܡܪܐ ܗܘܬ ܓܝܪ ܕܐܦܢ ܠܠܒܘܫܗ ܩܪܒܐ ܐܢܐ ܚܝܐ ܐܢܐ 28
chifukwa anaganiza kuti, “Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa.”
ܘܡܚܕܐ ܝܒܫܬ ܡܥܝܢܐ ܕܕܡܗ ܘܐܪܓܫܬ ܒܦܓܪܗ ܕܐܬܐܤܝܬ ܡܢ ܡܚܘܬܗ 29
Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.
ܝܫܘܥ ܕܝܢ ܡܚܕܐ ܝܕܥ ܒܢܦܫܗ ܕܚܝܠܐ ܢܦܩ ܡܢܗ ܘܐܬܦܢܝ ܠܘܬ ܟܢܫܐ ܘܐܡܪ ܡܢܘ ܩܪܒ ܠܡܐܢܝ 30
Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, “Ndani wakhudza zovala zanga?”
ܘܐܡܪܝܢ ܠܗ ܬܠܡܝܕܘܗܝ ܚܙܐ ܐܢܬ ܠܟܢܫܐ ܕܚܒܨܝܢ ܠܟ ܘܐܡܪ ܐܢܬ ܡܢܘ ܩܪܒ ܠܝ 31
Ophunzira ake anayankha kuti, “Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, ‘Ndani wandikhudza?’”
ܘܚܐܪ ܗܘܐ ܕܢܚܙܐ ܡܢܘ ܗܕܐ ܥܒܕ 32
Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi.
ܗܝ ܕܝܢ ܐܢܬܬܐ ܟܕ ܕܚܝܠܐ ܘܪܬܝܬܐ ܕܝܕܥܬ ܡܐ ܕܗܘܐ ܠܗ ܐܬܬ ܢܦܠܬ ܩܕܡܘܗܝ ܘܐܡܪܬ ܠܗ ܟܠܗ ܫܪܪܐ 33
Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha.
ܗܘ ܕܝܢ ܐܡܪ ܠܗ ܒܪܬܝ ܗܝܡܢܘܬܟܝ ܐܚܝܬܟܝ ܙܠܝ ܒܫܠܡܐ ܘܗܘܝܬܝ ܚܠܝܡܐ ܡܢ ܡܚܘܬܟܝ 34
Anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako.”
ܘܥܕ ܗܘ ܡܡܠܠ ܐܬܘ ܡܢ ܕܒܝܬ ܪܒ ܟܢܘܫܬܐ ܘܐܡܪܝܢ ܕܒܪܬܟ ܡܝܬܬ ܠܡܢܐ ܡܟܝܠ ܡܥܡܠ ܐܢܬ ܠܡܠܦܢܐ 35
Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, “Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?”
ܝܫܘܥ ܕܝܢ ܫܡܥ ܠܡܠܬܐ ܕܐܡܪܘ ܘܐܡܪ ܠܗܘ ܪܒ ܟܢܘܫܬܐ ܠܐ ܬܕܚܠ ܒܠܚܘܕ ܗܝܡܢ 36
Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, “Usachite mantha; ingokhulupirira.”
ܘܠܐ ܫܒܩ ܠܐܢܫ ܕܢܐܙܠ ܥܡܗ ܐܠܐ ܠܫܡܥܘܢ ܟܐܦܐ ܘܠܝܥܩܘܒ ܘܠܝܘܚܢܢ ܐܚܘܗܝ ܕܝܥܩܘܒ 37
Iye sanalole munthu wina aliyense kuti amutsatire koma Petro, Yakobo ndi Yohane mʼbale wa Yakobo.
ܘܐܬܘ ܠܒܝܬܐ ܕܗܘ ܪܒ ܟܢܘܫܬܐ ܘܚܙܐ ܕܪܗܝܒܝܢ ܘܒܟܝܢ ܘܡܝܠܠܝܢ 38
Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri.
ܘܥܠ ܘܐܡܪ ܠܗܘܢ ܡܢܐ ܪܗܝܒܝܢ ܐܢܬܘܢ ܘܒܟܝܢ ܛܠܝܬܐ ܠܐ ܡܝܬܬ ܐܠܐ ܕܡܟܐ ܗܝ 39
Analowa nati kwa iwo, “Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo.”
ܘܓܚܟܝܢ ܗܘܘ ܥܠܘܗܝ ܗܘ ܕܝܢ ܐܦܩ ܠܟܠܗܘܢ ܘܕܒܪ ܠܐܒܘܗ ܕܛܠܝܬܐ ܘܠܐܡܗ ܘܠܗܢܘܢ ܕܥܡܗ ܘܥܠ ܠܐܝܟܐ ܕܪܡܝܐ ܗܘܬ ܛܠܝܬܐ 40
Koma anamuseka Iye. Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo.
ܘܐܚܕ ܒܐܝܕܗ ܕܛܠܝܬܐ ܘܐܡܪ ܠܗ ܛܠܝܬܐ ܩܘܡܝ 41
Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, “Talita Kumi!” (Kutanthauza kuti, “Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!”)
ܘܒܪ ܫܥܬܗ ܩܡܬ ܛܠܝܬܐ ܘܡܗܠܟܐ ܗܘܬ ܐܝܬܝܗ ܗܘܬ ܓܝܪ ܒܪܬ ܫܢܝܢ ܬܪܬܥܤܪܐ ܘܡܬܕܡܪܝܢ ܗܘܘ ܕܘܡܪܐ ܪܒܐ 42
Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri.
ܘܦܩܕ ܐܢܘܢ ܤܓܝ ܕܠܐ ܐܢܫ ܢܕܥ ܗܕܐ ܘܐܡܪ ܕܢܬܠܘܢ ܠܗ ܠܡܠܥܤ 43
Anawalamulira kwambiri kuti asawuze wina aliyense za ichi, ndipo anawawuza kuti amupatse kanthu koti adye.

< ܡܪܩܘܣ 5 >