< ܓܠܛܝ̈ܐ 3 >

ܐܘ ܚܤܝܪܝ ܪܥܝܢܐ ܓܠܛܝܐ ܡܢܘ ܚܤܡ ܒܟܘܢ ܕܗܐ ܐܝܟ ܗܘ ܕܡܨܪ ܨܝܪ ܗܘܐ ܩܕܡ ܥܝܢܝܟܘܢ ܝܫܘܥ ܡܫܝܚܐ ܟܕ ܨܠܝܒ 1
Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani? Tinamuonetsa poyera pamaso panu Yesu Khristu monga wopachikidwa pa mtanda.
ܗܕܐ ܒܠܚܘܕ ܨܒܐ ܐܢܐ ܕܐܕܥ ܡܢܟܘܢ ܡܢ ܥܒܕܐ ܕܢܡܘܤܐ ܢܤܒܬܘܢ ܪܘܚܐ ܐܘ ܡܢ ܫܡܥܐ ܕܗܝܡܢܘܬܐ 2
Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva?
ܗܟܢܐ ܤܟܠܝܢ ܐܢܬܘܢ ܕܫܪܝܬܘܢ ܒܪܘܚܐ ܘܗܫܐ ܒܒܤܪ ܡܫܠܡܝܢ ܐܢܬܘܢ 3
Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi?
ܗܠܝܢ ܟܠܗܝܢ ܐܝܩܐ ܤܝܒܪܬܘܢ ܘܐܫܬܘܦ ܕܝܢ ܐܝܩܐ 4
Kodi munavutika kwambiri pachabe, ngati kunali kwachabedi?
ܗܘ ܗܟܝܠ ܕܝܗܒ ܒܟܘܢ ܪܘܚܐ ܘܤܥܪ ܒܟܘܢ ܚܝܠܐ ܡܢ ܥܒܕܐ ܕܢܡܘܤܐ ܐܘ ܡܢ ܫܡܥܐ ܕܗܝܡܢܘܬܐ 5
Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva?
ܐܝܟܢܐ ܕܗܝܡܢ ܐܒܪܗܡ ܠܐܠܗܐ ܘܐܬܚܫܒܬ ܠܗ ܠܙܕܝܩܘ 6
Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.”
ܕܥܘ ܗܟܝܠ ܕܐܝܠܝܢ ܕܡܢ ܗܝܡܢܘܬܐ ܐܢܘܢ ܗܢܘܢ ܐܢܘܢ ܒܢܝܐ ܕܐܒܪܗܡ 7
Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu.
ܡܛܠ ܓܝܪ ܕܩܕܡ ܝܕܥ ܐܠܗܐ ܕܒܗܝܡܢܘܬܐ ܗܘ ܡܙܕܕܩܝܢ ܥܡܡܐ ܩܕܡ ܤܒܪ ܠܐܒܪܗܡ ܐܝܟ ܕܐܡܪ ܟܬܒܐ ܩܕܝܫܐ ܕܒܟ ܢܬܒܪܟܘܢ ܟܠܗܘܢ ܥܡܡܐ 8
Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.”
ܡܕܝܢ ܡܗܝܡܢܐ ܗܘ ܡܬܒܪܟܝܢ ܒܐܒܪܗܡ ܡܗܝܡܢܐ 9
Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro.
ܐܝܠܝܢ ܓܝܪ ܕܡܢ ܥܒܕܐ ܐܢܘܢ ܕܢܡܘܤܐ ܬܚܝܬ ܠܘܛܬܐ ܐܢܘܢ ܟܬܝܒ ܓܝܪ ܕܠܝܛ ܗܘ ܟܠܡܢ ܕܠܐ ܢܥܒܕ ܟܠ ܕܟܬܝܒ ܒܢܡܘܤܐ ܗܢܐ 10
Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.”
ܕܠܐ ܕܝܢ ܡܙܕܕܩ ܐܢܫ ܒܢܡܘܤܐ ܠܘܬ ܐܠܗܐ ܗܕܐ ܓܠܝܐ ܗܝ ܡܛܠ ܕܟܬܝܒ ܕܙܕܝܩܐ ܒܗܝܡܢܘܬܐ ܢܚܐ 11
Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
ܢܡܘܤܐ ܕܝܢ ܠܐ ܗܘܐ ܡܢ ܗܝܡܢܘܬܐ ܐܠܐ ܡܢ ܕܢܥܒܕ ܐܝܠܝܢ ܕܟܬܝܒܢ ܒܗ ܢܚܐ ܒܗܝܢ 12
Koma chikhulupiriro si Malamulo, chifukwa Malemba akuti, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
ܠܢ ܕܝܢ ܡܫܝܚܐ ܙܒܢܢ ܡܢ ܠܘܛܬܐ ܕܢܡܘܤܐ ܘܗܘ ܗܘܐ ܚܠܦܝܢ ܠܘܛܬܐ ܟܬܝܒ ܓܝܪ ܕܠܝܛ ܗܘ ܟܠܡܢ ܕܡܬܬܠܐ ܒܩܝܤܐ 13
Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”
ܕܒܥܡܡܐ ܬܗܘܐ ܒܘܪܟܬܗ ܕܐܒܪܗܡ ܒܝܫܘܥ ܡܫܝܚܐ ܘܚܢܢ ܢܤܒ ܫܘܘܕܝܐ ܕܪܘܚܐ ܒܗܝܡܢܘܬܐ 14
Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.
ܐܚܝ ܐܝܟ ܕܒܝܬ ܒܢܝܢܫܐ ܐܡܪ ܐܢܐ ܕܕܝܬܩܐ ܕܒܪܢܫܐ ܕܐܫܬܪܪܬ ܐܢܫ ܠܐ ܡܤܠܐ ܐܘ ܡܫܚܠܦ ܒܗ ܡܕܡ 15
Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi.
ܠܐܒܪܗܡ ܕܝܢ ܐܬܡܠܟ ܡܘܠܟܢܐ ܘܠܙܪܥܗ ܘܠܐ ܐܡܪ ܠܗ ܕܠܙܪܥܝܟ ܐܝܟ ܕܠܤܓܝܐܐ ܐܠܐ ܠܙܪܥܟ ܐܝܟ ܕܠܚܕ ܗܘ ܕܐܝܬܘܗܝ ܡܫܝܚܐ 16
Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu.
ܗܕܐ ܕܝܢ ܐܡܪ ܐܢܐ ܕܕܝܬܩܐ ܕܡܢ ܩܕܝܡ ܐܫܬܪܪܬ ܡܢ ܐܠܗܐ ܒܡܫܝܚܐ ܢܡܘܤܐ ܗܘ ܕܗܘܐ ܡܢ ܒܬܪ ܐܪܒܥ ܡܐܐ ܘܬܠܬܝܢ ܫܢܝܢ ܠܐ ܡܫܟܚ ܕܢܤܠܝܗ ܘܢܒܛܠ ܡܘܠܟܢܐ 17
Chimene ndikutanthauza ine ndi ichi: Malamulo amene anabwera patatha zaka 430, sangathetse pangano limene linakhazikitsidwa kale ndi Mulungu ndi kuliwononga lonjezolo.
ܐܢ ܕܝܢ ܡܢ ܢܡܘܤܐ ܗܝ ܝܪܬܘܬܐ ܡܟܝܠ ܠܐ ܗܘܬ ܡܢ ܡܘܠܟܢܐ ܠܐܒܪܗܡ ܕܝܢ ܒܡܘܠܟܢܐ ܗܘ ܝܗܒ ܠܗ ܐܠܗܐ 18
Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo.
ܡܢܐ ܗܟܝܠ ܢܡܘܤܐ ܡܛܠ ܡܤܛܝܢܘܬܐ ܐܬܬܘܤܦ ܥܕܡܐ ܕܢܐܬܐ ܙܪܥܐ ܗܘ ܕܠܗ ܗܘܐ ܫܘܘܕܝܐ ܘܐܬܝܗܒ ܗܘ ܢܡܘܤܐ ܒܝܕ ܡܠܐܟܐ ܒܐܝܕܐ ܕܡܨܥܝܐ 19
Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati.
ܡܨܥܝܐ ܕܝܢ ܠܐ ܗܘܐ ܕܚܕ ܐܠܗܐ ܕܝܢ ܚܕ ܗܘ 20
Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi.
ܢܡܘܤܐ ܗܟܝܠ ܤܩܘܒܠܐ ܗܘ ܕܡܘܠܟܢܐ ܕܐܠܗܐ ܚܤ ܐܠܘ ܓܝܪ ܐܬܝܗܒ ܗܘܐ ܢܡܘܤܐ ܐܝܢܐ ܕܡܫܟܚ ܗܘܐ ܠܡܚܝܘ ܫܪܝܪܐܝܬ ܡܢ ܢܡܘܤܐ ܗܘܝܐ ܗܘܬ ܙܕܝܩܘܬܐ 21
Kodi ndiye kuti lamulo limatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Ayi. Nʼkosatheka! Pakuti ngati tikanapatsidwa malamulo opatsa moyo ndiye kuti mwa lamulo tikanakhala olungama.
ܐܠܐ ܚܒܫ ܟܬܒܐ ܟܠܡܕܡ ܬܚܝܬ ܚܛܝܬܐ ܕܡܘܠܟܢܐ ܒܗܝܡܢܘܬܐ ܕܝܫܘܥ ܡܫܝܚܐ ܢܬܝܗܒ ܠܐܝܠܝܢ ܕܡܗܝܡܢܝܢ 22
Koma Malemba akunenetsa kuti dziko lonse lili mu ulamuliro wauchimo, kuti mwachikhulupiriro mwa Yesu Khristu, chimene chinalonjezedwa chiperekedwe kwa amene akhulupirira.
ܥܕܠܐ ܕܝܢ ܬܐܬܐ ܗܝܡܢܘܬܐ ܢܡܘܤܐ ܢܛܪ ܗܘܐ ܠܢ ܟܕ ܚܒܝܫܝܢܢ ܠܗܝܡܢܘܬܐ ܕܥܬܝܕܐ ܗܘܬ ܠܡܬܓܠܝܘ 23
Chikhulupiriro ichi chisanabwere, ife tinali mʼndende ya lamulo, otsekeredwa mpaka pamene chikhulupiriro chikanavumbulutsidwa.
ܢܡܘܤܐ ܗܟܝܠ ܬܪܐܐ ܗܘܐ ܠܢ ܠܘܬ ܡܫܝܚܐ ܕܡܢ ܗܝܡܢܘܬܐ ܢܙܕܕܩ 24
Choncho lamulo linayikidwa kukhala lotiyangʼanira kuti lititsogolere kwa Khristu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro.
ܟܕ ܐܬܬ ܕܝܢ ܗܝܡܢܘܬܐ ܠܐ ܗܘܝܢ ܬܚܝܬ ܬܪܐܐ 25
Tsopano pakuti chikhulupiriro chabwera, ife sitilinso mu ulamuliro wa lamulo.
ܟܠܟܘܢ ܓܝܪ ܒܢܝܐ ܐܢܬܘܢ ܕܐܠܗܐ ܒܗܝܡܢܘܬܐ ܕܝܫܘܥ ܡܫܝܚܐ 26
Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,
ܐܝܠܝܢ ܓܝܪ ܕܒܡܫܝܚܐ ܥܡܕܬܘܢ ܠܡܫܝܚܐ ܠܒܫܬܘܢ 27
pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu.
ܠܝܬ ܝܗܘܕܝܐ ܘܠܐ ܐܪܡܝܐ ܠܝܬ ܥܒܕܐ ܘܠܐ ܒܪ ܚܐܪܐ ܠܝܬ ܕܟܪܐ ܘܠܐ ܢܩܒܬܐ ܟܠܟܘܢ ܓܝܪ ܚܕ ܐܢܬܘܢ ܒܝܫܘܥ ܡܫܝܚܐ 28
Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
ܘܐܢ ܕܡܫܝܚܐ ܐܢܬܘܢ ܡܟܝܠ ܙܪܥܗ ܐܢܬܘܢ ܕܐܒܪܗܡ ܘܝܪܬܐ ܒܡܘܠܟܢܐ 29
Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbewu ya Abrahamu, ndi olowamʼmalo molingana ndi lonjezo.

< ܓܠܛܝ̈ܐ 3 >