Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Jeremiah Chapter 47 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Jeremiah/47 1) Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu: 2) Yehova akuti, “Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto; adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo. Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo, mizinda ndi onse okhala mʼmenemo. Anthu adzafuwula; anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira 3) akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga, phokoso la magaleta ake ndi kulira kwa mikombero yake. Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo; manja awo adzangoti khoba. 4) Pakuti tsiku lafika lowononga Afilisti onse ndi kupha onse otsala, onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni. Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti, otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori. 5) Anthu a ku Gaza ameta mipala; anthu a ku Asikeloni akhala chete. Inu otsala a ku chigwa, mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti? 6) “Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova, kodi udzapumula liti? Bwerera mʼmalo ako; ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’ 7) Koma lupangalo lidzapumula bwanji pamene Yehova walilamulira kuti lithire nkhondo Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?” Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!