< 1 तवा 24 >
1 और बनी हारून के फ़रीक़ यह थे हारून के बेटे नदब, अबीहू और इली'एलियाज़र और ऐतामर थे।
Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
2 नदब और अबीहू अपने बाप से पहले मर गए और उनके औलाद न थी, इसलिए इली'एलियाज़र और ऐतामर ने कहानत का काम किया।
Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe.
3 दाऊद ने इली'एलियाज़र के बेटों में से सदोक़, और ऐतामर के बेटों में से अख़ीमलिक को उनकी ख़िदमत की तरतीब के मुताबिक़ तक़्सीम किया।
Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira.
4 इतमर के बेटों से ज़्यादा इली'एलियाज़र के बेटों में रईस मिले, और इस तरह से वह तक़्सीम किए गए के इली'एलियाज़र के बेटों में आबाई ख़ान्दानों के सोलह सरदार थे; और ऐतामर के बेटों में से आबाई ख़ान्दानों के मुताबिक़ आठ।
Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara.
5 इस तरह पर्ची डाल कर और एक साथ ख़ल्त मल्त होकर वह तक़्सीम हुए, क्यूँकि मक़दिस के सरदार और ख़ुदा के सरदार बनी इली'एलियाज़र और बनी ऐतामर दोनों में से थे।
Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.
6 और नतनीएल मुन्शी के बेटे समायाह ने जो लावियों में से था, उनके नामों को बादशाह और अमीरों और सदोक़ काहिन और अख़ीमलिक बिन अबीयातर और काहिनों और लावियों के आबाई ख़ान्दानों के सरदारों के सामने लिखा। जब इली'एलियाज़र का एक आबाई ख़ान्दान लिया गया, तो ऐतामर का भी एक आबाई ख़ान्दान लिया गया।
Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.
7 और पहली चिट्ठी यहूयरीब की निकली, दूसरी यद'अयाह की,
Maere woyamba anagwera Yehoyaribu, achiwiri anagwera Yedaya,
8 तीसरी हारिम की, चौथी श'ऊरीम,
achitatu anagwera Harimu, achinayi anagwera Seorimu,
9 पाँचवीं मलकियाह की, छटी मियामीन की
achisanu anagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,
10 सातवीं हक्कूज़ की, आठवीं अबियाह की,
achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,
11 नवीं यशू'आ की, दसवीं सिकानियाह की,
achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa, a khumi anagwera Sekaniya,
12 ग्यारहवीं इलियासब की, बारहवीं यक़ीम की,
a 11 anagwera Eliyasibu, a 12 anagwera Yakimu,
13 तेरहवीं खुफ़्फ़ाह की, चौदहवीं यसबाब की,
a 13 anagwera Hupa, a 14 anagwera Yesebeabu,
14 पन्द्रहवीं बिल्जाह की, सोलहवीं इम्मेर की,
a 15 anagwera Biliga, a 16 anagwera Imeri,
15 सत्रहवीं हज़ीर की, अठारहवीं फ़ज़ीज़ की,
a 17 anagwera Heziri, a 18 anagwera Hapizezi,
16 उन्नीसवीं फ़तहियाह की, बीसवीं यहज़िकेल की,
a 19 anagwera Petahiya, a 20 anagwera Ezekieli,
17 इक्कीसवीं यकिन की, बाइसवीं जम्मूल की,
a 21 anagwera Yakini, a 22 anagwera Gamuli,
18 तेइसवीं दिलायाह की, चौबीसवीं माज़ियाह की।
a 23 anagwera Delaya, ndipo a 24 anagwera Maaziya.
19 यह उनकी ख़िदमत की तरतीब थी, ताकि वह ख़ुदावन्द के घर में उस क़ानून के मुताबिक़ आएँ जो उनको उनके बाप हारून की ज़रिए' वैसा ही मिला, जैसा ख़ुदावन्द इस्राईल के ख़ुदा ने उसे हुक्म किया था।
Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.
20 बाक़ी बनी लावी में से:'अमराम के बेटों में से सूबाएल, सूबाएल के बेटों में से यहदियाह;
Za zidzukulu zina zonse za Levi: Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli; kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.
21 रहा रहबियाह, सो रहबियाह के बेटों में से पहला यस्सियाह।
Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake: Mtsogoleri anali Isiya.
22 इज़हारियों में से सलूमोत, बनी सलूमोत में से यहत।
Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti; kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.
23 बनी हबरून में से: यरियाह पहला, अमरियाह दूसरा, यहज़िएल तीसरा, यकमि'आम चौथा।
Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.
24 बनी उज़्ज़ीएल में से: मीकाह; बनी मीकाह में से: समीर।
Mwana wa Uzieli: Mika; kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.
25 मीकाह का भाई यस्सियाह, बनी यस्सियाह में से ज़करियाह।
Mʼbale wa Mika: Isiya; kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.
26 मिरारी के बेटे: महली और मूशी। बनी याज़ियाह में से बिनू
Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Mwana wa Yaaziya: Beno.
27 रहे बनी मिरारी, सो याज़ियाह से बिनू और सूहम और ज़क्कूर और 'इब्री।
Ana a Merari: Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.
28 महली से: इली'एलियाज़र, जिसके कोई बेटा न था।
Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.
29 क़ीस से, क़ीस का बेटा: यरहमिएल।
Kuchokera kwa Kisi: Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.
30 और मूशी के बेटे: महली और 'ऐदर और यरीमीत। लावियों की औलाद अपने आबाई ख़ान्दानों के मुताबिक़ यही थी।
Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti. Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo.
31 इन्होंने भी अपने भाई बनी हारून की तरह, दाऊद बादशाह और सदूक़ और अख़ीमलिक और काहिनों और लावियों के आबाई ख़ान्दानों के सरदारों के सामने अपना अपनी पर्ची डाला, या'नी सरदार के आबाई ख़ान्दानों का जो हक़ था वही उसके छोटे भाई के ख़ान्दानों का था।
Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.