< 여호수아 15 >
1 유다 자손의 지파가 그 가족대로 제비 뽑은 땅의 극남단은 에돔 지경에 이르고 또 남으로 신 광야까지라
Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni.
2 그 남편 경계는 염해의 극단 곧 남향한 해만에서부터
Malire awo a kummwera anayambira kummwera kwenikweni kwa Nyanja ya Mchere,
3 아그랍빔 비탈 남편으로 지나 신에 이르고 가데스 바네아 남편으로 올라가서 헤스론을 지나며 아달로 올라가서 돌이켜 갈가에 이르고
kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika.
4 거기서 아스몬에 이르고 애굽 시내에 미치며 바다에 이르러 경계의 끝이 되나니 이것이 너희 남편 경계가 되리라
Anapitirira mpaka ku Azimoni motsata mtsinje umene uli malire a Igupto mpaka ku nyanja. Awa ndiwo malire awo a kummwera.
5 그 동편 경계는 염해니 요단 끝까지요 그 북편 경계는 요단 끝에 당한 해만에서부터
Malire a kummawa anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yorodani amathira mu Nyanja ya Mchere. Malire a kumpoto anayambira kumene Yorodani amathirira nyanjayo,
6 벧호글라로 올라가서 벧 아라바 북편을 지나 르우벤 자손 보한의 돌에 이르고
napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani.
7 또 아골 골짜기에서부터 드빌을 지나 북으로 올라가서 강 남편에 있는 아둠빔 비탈 맞은편 길갈을 향하고 나아가 엔 세메스 물을 지나 엔로겔에 이르며
Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli.
8 또 힌놈의 아들의 골짜기로 올라가서 여부스 곧 예루살렘 남편 어깨에 이르며 또 힌놈의 골짜기 앞 서편에 있는 산 꼭대기로 올라가나니 이곳은 르바임 골짜기 북편 끝이며
Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu.
9 또 이 산 꼭대기에서부터 넵도아 샘물까지 이르러 에브론 산 성읍들에 미치고 또 바알라 곧 기럇 여아림에 미치며
Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu).
10 또 바알라에서부터 서편으로 돌이켜 세일 산에 이르러 여아림 산 곧 그살론 곁 북편에 이르고 또 벧 세메스로 내려가서 딤나로 지나고
Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna.
11 또 에그론 북편으로 나아가 식그론에 이르러 바알라 산에 미치고 얍느엘에 이르나니 그 끝은 바다며
Malirewo anapitirira kumatsitso a mapiri chakumpoto kwa Ekroni, ndi kukhotera ku Sikeroni. Malirewo anadutsa phiri la Baalahi ndi kufika ku Yabineeli. Malirewo anathera ku nyanja.
12 서편 경계는 대해와 그 해변이니 유다 자손이 그 가족대로 얻은 사면 경계가 이러하니라
Malire a mbali ya kumadzulo anali Nyanja Yayikulu. Awa ndi malire ozungulira malo amene anapatsidwa kwa mabanja a fuko la Yuda.
13 여호와께서 여호수아에게 명하신 대로 여호수아가 기럇 아르바 곧 헤브론 성을 유다 자손 중에서 분깃으로 여분네의 아들 갈렙에게 주었으니 아르바는 아낙의 아비였더라
Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki).
14 갈렙이 거기서 아낙의 소생 곧 그 세 아들 세새와 아히만과 달매를 쫓아내었고
Kuchokera ku Hebroni, Kalebe anathamangitsamo mafuko a Aanaki awa: Sesai, Ahimani ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki.
15 거기서 올라가서 드빌 거민을 쳤는데 드빌의 본 이름은 기럇 세벨이라
Kuchokera kumeneko, Kalebe anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi).
16 갈렙이 말하기를 기럇 세벨을 쳐서 그것을 취하는 자에게는 내가 내 딸 악사를 아내로 주리라 하였더니
Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
17 갈렙의 아우요 그나스의 아들인 옷니엘이 그것을 취함으로 갈렙이 그 딸 악사를 그에게 아내로 주었더라
Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
18 악사가 출가할 때에 그에게 청하여 자기 아비에게 밭을 구하자 하고 나귀에서 내리매 갈렙이 그에게 묻되 네가 무엇을 원하느냐
Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani.”
19 가로되 내게 복을 주소서 아버지께서 나를 남방 땅으로 보내시오니 샘물도 내게 주소서 하매 갈렙이 윗 샘과 아랫 샘을 그에게 주었더라
Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.
20 유다 자손의 지파가 그 가족대로 얻은 기업은 이러하니라
Dziko limene mabanja a fuko la Yuda analandira ngati cholowa chawo ndi ili:
21 유다 자손의 지파의 남으로 에돔 경계에 접근한 성읍들은 갑스엘과 에델과 야굴과
Mizinda yakummwera kwenikweni kwa fuko la Yuda yoyandikana ndi malire a Edomu anali: Kabizeeli, Ederi, Yaguri
Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori)
Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti
Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya,
Elitoladi, Kesili, Horima
Zikilagi, Madimena, Sanisana,
32 실힘과 아인과 림몬이니 모두 이십구 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Mizinda yonse inalipo 29 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
Mizinda ya ku chigwa cha kumadzulo ndi iyi: Esitaoli, Zora, Asina
Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu,
Yarimuti, Adulamu, Soko, Azeka,
36 사아라임과 아디다임과 그데라와 그데로다임이니 모두 십사 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi,
Dileani, Mizipa, Yokiteeli,
Lakisi, Bozikati, Egiloni,
Kaboni, Lahimasi, Kitilisi,
41 그데롯과 벧다곤과 나아마와 막게다니 모두 십육 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
Mizinda ina inali iyi: Libina, Eteri, Asani,
44 그일라와 악십과 마레사니 모두 아홉 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Keila, Akizibu ndi Maresa, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.
Panalinso Ekroni pamodzi ndi midzi yake;
46 에그론에서부터 바다까지 아스돗 곁에 있는 모든 성읍과 그 촌락이었으며
komanso yonse imene inali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake kuyambira ku Ekroni mpaka ku Nyanja Yayikulu.
47 아스돗과 그 향리와 촌락과 가사와 그 향리와 촌락이니 애굽 시내와 대해 가에 이르기까지였으며
Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
Mizinda ya kumapiri inali: Samiri, Yatiri, Soko,
Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri)
51 고센과 홀론과 길로니 모두 십일 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Goseni, Holoni ndi Gilo. Mizinda yonse pamodzi inali khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.
Analandiranso mizinda iyi: Arabu, Duma, Esani,
Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki
54 훔다와 기럇 아르바 곧 헤브론과 시올이니 모두 아홉 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.
Panalinso Maoni, Karimeli, Zifi, Yuta
Yezireeli, Yokideamu, Zanowa,
57 가인과 기브아와 딤나니 모두 열 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Kaini, Gibeya ndi Timna, mizinda khumi ndi midzi yake.
Mizinda ina inali: Halihuli, Beti Zuri, Gedori,
59 마아랏과 벧 아놋과 엘드곤이니 모두 여섯 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake
60 기럇 바알 곧 기럇 여아림과 라빠니 모두 두 성읍이요 또 그 촌락이었으며
Panalinso Kiriati Baala (ndiye kuti Kiriati Yearimu) ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yake.
Mizinda ya ku chipululu inali iyi: Beti-Araba, Midini, Sekaka,
62 닙산과 염성과 엔 게디니 모두 여섯 성읍이요 또 그 촌락이었더라
Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni Gedi, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.
63 예루살렘 거민 여부스 사람을 유다 자손이 쫓아내지 못하였으므로 여부스 사람이 오늘날까지 유다 자손과 함께 예루살렘에 거하니라
Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.