< תהילים 9 >

למנצח עלמות לבן מזמור לדוד אודה יהוה בכל לבי אספרה כל נפלאותיך׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a nyimbo ya “Imfa ya Mwana.” Salimo la Davide. Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse; ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.
אשמחה ואעלצה בך אזמרה שמך עליון׃ 2
Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu; Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.
בשוב אויבי אחור יכשלו ויאבדו מפניך׃ 3
Adani anga amathawa, iwo amapunthwa ndi kuwonongedwa pamaso panu.
כי עשית משפטי ודיני ישבת לכסא שופט צדק׃ 4
Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga; Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.
גערת גוים אבדת רשע שמם מחית לעולם ועד׃ 5
Mwadzudzula mitundu ya anthu ndipo mwawononga anthu oyipa; Inu mwafafaniza dzina lawo kwamuyaya.
האויב תמו חרבות לנצח וערים נתשת אבד זכרם המה׃ 6
Chiwonongeko chosatha chagwera adani, mwafafaniza mizinda yawo; ngakhale chikumbutso chawo chawonongedwa.
ויהוה לעולם ישב כונן למשפט כסאו׃ 7
Yehova akulamulira kwamuyaya; wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira.
והוא ישפט תבל בצדק ידין לאמים במישרים׃ 8
Iye adzaweruza dziko mwachilungamo; adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.
ויהי יהוה משגב לדך משגב לעתות בצרה׃ 9
Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto.
ויבטחו בך יודעי שמך כי לא עזבת דרשיך יהוה׃ 10
Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.
זמרו ליהוה ישב ציון הגידו בעמים עלילותיו׃ 11
Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni; lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
כי דרש דמים אותם זכר לא שכח צעקת עניים׃ 12
Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira; Iye salekerera kulira kwa ozunzika.
חננני יהוה ראה עניי משנאי מרוממי משערי מות׃ 13
Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira! Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
למען אספרה כל תהלתיך בשערי בת ציון אגילה בישועתך׃ 14
kuti ndilengeze za matamando anu pa zipata za ana aakazi a Ziyoni, kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
טבעו גוים בשחת עשו ברשת זו טמנו נלכדה רגלם׃ 15
Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba; mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
נודע יהוה משפט עשה בפעל כפיו נוקש רשע הגיון סלה׃ 16
Yehova amadziwika ndi chilungamo chake; oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo. Higayoni. (Sela)
ישובו רשעים לשאולה כל גוים שכחי אלהים׃ (Sheol h7585) 17
Oyipa amabwerera ku manda, mitundu yonse imene imayiwala Mulungu. (Sheol h7585)
כי לא לנצח ישכח אביון תקות ענוים תאבד לעד׃ 18
Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse, kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.
קומה יהוה אל יעז אנוש ישפטו גוים על פניך׃ 19
Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane; mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
שיתה יהוה מורה להם ידעו גוים אנוש המה סלה׃ 20
Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova; mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba. (Sela)

< תהילים 9 >