< תהילים 32 >
לדוד משכיל אשרי נשוי פשע כסוי חטאה׃ | 1 |
Salimo la Davide. Malangizo. Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa.
אשרי אדם לא יחשב יהוה לו עון ואין ברוחו רמיה׃ | 2 |
Ngodala munthu amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.
כי החרשתי בלו עצמי בשאגתי כל היום׃ | 3 |
Pamene ndinali chete, mafupa anga anakalamba chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
כי יומם ולילה תכבד עלי ידך נהפך לשדי בחרבני קיץ סלה׃ | 4 |
Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu linandipsinja; mphamvu zanga zinatha monga nthawi yotentha yachilimwe. (Sela)
חטאתי אודיעך ועוני לא כסיתי אמרתי אודה עלי פשעי ליהוה ואתה נשאת עון חטאתי סלה׃ | 5 |
Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” (Sela)
על זאת יתפלל כל חסיד אליך לעת מצא רק לשטף מים רבים אליו לא יגיעו׃ | 6 |
Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo pomwe mukupezeka; ndithu pamene madzi amphamvu auka, sadzamupeza.
אתה סתר לי מצר תצרני רני פלט תסובבני סלה׃ | 7 |
Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. (Sela)
אשכילך ואורך בדרך זו תלך איעצה עליך עיני׃ | 8 |
Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
אל תהיו כסוס כפרד אין הבין במתג ורסן עדיו לבלום בל קרב אליך׃ | 9 |
Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
רבים מכאובים לרשע והבוטח ביהוה חסד יסובבנו׃ | 10 |
Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa koma chikondi chosatha cha Yehova chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.
שמחו ביהוה וגילו צדיקים והרנינו כל ישרי לב׃ | 11 |
Kondwerani mwa Yehova inu olungama; imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!