< מִשְׁלֵי 4 >

שמעו בנים מוסר אב והקשיבו לדעת בינה׃ 1
Ananu, mverani malangizo a abambo anu; tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.
כי לקח טוב נתתי לכם תורתי אל תעזבו׃ 2
Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino. Choncho musasiye malangizo anga.
כי בן הייתי לאבי רך ויחיד לפני אמי׃ 3
Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga; mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.
וירני ויאמר לי יתמך דברי לבך שמר מצותי וחיה׃ 4
Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti, “Ugwiritse mawu anga pa mtima pako, usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.
קנה חכמה קנה בינה אל תשכח ואל תט מאמרי פי׃ 5
Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu; usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.
אל תעזבה ותשמרך אהבה ותצרך׃ 6
Usasiye nzeru ndipo idzakusunga. Uziyikonda ndipo idzakuteteza.
ראשית חכמה קנה חכמה ובכל קנינך קנה בינה׃ 7
Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru. Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.
סלסלה ותרוממך תכבדך כי תחבקנה׃ 8
Uyilemekeze nzeruyo ndipo idzakukweza; ikumbatire nzeruyo ndipo idzakupatsa ulemu.
תתן לראשך לוית חן עטרת תפארת תמגנך׃ 9
Idzayika sangamutu yokongola yamaluwa pamutu pako; idzakupatsa chipewa chaufumu chaulemu.”
שמע בני וקח אמרי וירבו לך שנות חיים׃ 10
Mwana wanga, umvere ndi kuvomereza zimene ndikunena, ndipo zaka za moyo wako zidzakhala zochuluka.
בדרך חכמה הרתיך הדרכתיך במעגלי ישר׃ 11
Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera mʼnjira zolungama.
בלכתך לא יצר צעדך ואם תרוץ לא תכשל׃ 12
Pamene ukuyenda, mapazi ako sadzawombana; ukamadzathamanga, sudzapunthwa.
החזק במוסר אל תרף נצרה כי היא חייך׃ 13
Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi. Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.
בארח רשעים אל תבא ואל תאשר בדרך רעים׃ 14
Usayende mʼnjira za anthu oyipa kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.
פרעהו אל תעבר בו שטה מעליו ועבור׃ 15
Pewa njira zawo, usayende mʼmenemo; uzilambalala nʼkumangopita.
כי לא ישנו אם לא ירעו ונגזלה שנתם אם לא יכשולו׃ 16
Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa; tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.
כי לחמו לחם רשע ויין חמסים ישתו׃ 17
Paja chakudya chawo ndicho kuchita zoyipa basi ndipo chakumwa chawo ndi chiwawa.
וארח צדיקים כאור נגה הולך ואור עד נכון היום׃ 18
Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.
דרך רשעים כאפלה לא ידעו במה יכשלו׃ 19
Koma njira ya anthu oyipa ili ngati mdima wandiweyani; iwo sadziwa chomwe chimawapunthwitsa.
בני לדברי הקשיבה לאמרי הט אזנך׃ 20
Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena; tchera khutu ku mawu anga.
אל יליזו מעיניך שמרם בתוך לבבך׃ 21
Usayiwale malangizo angawa, koma uwasunge mu mtima mwako.
כי חיים הם למצאיהם ולכל בשרו מרפא׃ 22
Pakuti amapatsa moyo kwa aliyense amene awapeza ndipo amachiritsa thupi lake lonse.
מכל משמר נצר לבך כי ממנו תוצאות חיים׃ 23
Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.
הסר ממך עקשות פה ולזות שפתים הרחק ממך׃ 24
Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota; ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.
עיניך לנכח יביטו ועפעפיך יישרו נגדך׃ 25
Maso ako ayangʼane patsogolo; uziyangʼana kutsogolo molunjika.
פלס מעגל רגלך וכל דרכיך יכנו׃ 26
Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.
אל תט ימין ושמאול הסר רגלך מרע׃ 27
Usapatukire kumanja kapena kumanzere; usapite kumene kuli zoyipa.

< מִשְׁלֵי 4 >