< נחמיה 6 >
ויהי כאשר נשמע לסנבלט וטוביה ולגשם הערבי וליתר איבינו כי בניתי את החומה ולא נותר בה פרץ גם עד העת ההיא דלתות לא העמדתי בשערים׃ | 1 |
Pamenepo Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndi adani athu anamva kuti ndatsiriza ntchito yomanganso khoma ndi kuti palibe mpata umene watsala ngakhale kuti pa nthawi imeneyi ndinali ndisanayike zitseko pa zipata.
וישלח סנבלט וגשם אלי לאמר לכה ונועדה יחדו בכפירים בבקעת אונו והמה חשבים לעשות לי רעה׃ | 2 |
Sanibalati ndi Gesemu, ananditumizira uthenga uwu: “Bwerani tidzakumane pa mudzi wina ku chigwa cha Ono.” Koma iwo anakonzekera kuti akandichite chiwembu kumeneko.
ואשלחה עליהם מלאכים לאמר מלאכה גדולה אני עשה ולא אוכל לרדת למה תשבת המלאכה כאשר ארפה וירדתי אליכם׃ | 3 |
Choncho ine ndinatuma amithenga ndi yankho ili: “Ine ndikugwira ntchito yayikulu kuno ndipo sindingathe kubwera kumeneko. Kodi ntchito iyime pofuna kuti ndibwere kumeneko?”
וישלחו אלי כדבר הזה ארבע פעמים ואשיב אותם כדבר הזה׃ | 4 |
Ananditumizira uthenga umodzimodzi omwewu kanayi ndipo ndinawayankha chimodzimodzi.
וישלח אלי סנבלט כדבר הזה פעם חמישית את נערו ואגרת פתוחה בידו׃ | 5 |
Tsono kachisanu, Sanibalati anatumiza wantchito wake ndi kalata yosamata.
כתוב בה בגוים נשמע וגשמו אמר אתה והיהודים חשבים למרוד על כן אתה בונה החומה ואתה הוה להם למלך כדברים האלה׃ | 6 |
Mu kalatamo munali mawu akuti, “Pali mphekesera pakati pa mitundu ya anthu, ndiponso Gesemu akunena zomwezo kuti inu ndi Ayuda onse mufuna kuwukira boma. Nʼchifukwa chake mukumanga khoma. Mphekeserazo zikutinso inu mukufuna kudzakhala mfumu yawo.
וגם נביאים העמדת לקרא עליך בירושלם לאמר מלך ביהודה ועתה ישמע למלך כדברים האלה ועתה לכה ונועצה יחדו׃ | 7 |
Mwayikanso kale aneneri amene adzalengeza za iwe mu Yerusalemu kuti ‘Mu Yuda muli mfumu!’ Tsono nkhani iyi imveka ndithu kwa mfumu. Choncho bwerani kuti tidzakambirane.”
ואשלחה אליו לאמר לא נהיה כדברים האלה אשר אתה אומר כי מלבך אתה בודאם׃ | 8 |
Ine ndinatumiza yankho ili: “Pa zimene mukunenazo, palibe chimene chinachitikapo. Inu mukungozipeka mʼmutu mwanu.”
כי כלם מיראים אותנו לאמר ירפו ידיהם מן המלאכה ולא תעשה ועתה חזק את ידי׃ | 9 |
Apa adani athu onsewa ankangofuna kutiopseza. Iwo ankaganiza kuti “Tichita mantha ndi kuleka kugwira ntchito.” Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu ndilimbitseni mtima.”
ואני באתי בית שמעיה בן דליה בן מהיטבאל והוא עצור ויאמר נועד אל בית האלהים אל תוך ההיכל ונסגרה דלתות ההיכל כי באים להרגך ולילה באים להרגך׃ | 10 |
Tsiku lina ndinapita ku nyumba ya Semaya mwana wa Delaya mwana wa Mehatabeli. Tsono anandiwuza kuti, “Tiyeni tikakumanire ku Nyumba ya Mulungu. Tikabisale mʼmenemo ndi kutseka zitseko chifukwa akubwera kudzakuphani. Ndithu usiku uno akubwera kudzakuphani.”
ואמרה האיש כמוני יברח ומי כמוני אשר יבוא אל ההיכל וחי לא אבוא׃ | 11 |
Koma ndinayankha kuti, “Kodi munthu ngati ine nʼkuthawa? Kapena munthu wofanana ndi ine nʼkupita ku Nyumba ya Mulungu kuti apulumutse moyo wake? Ayi, ine sindipita!”
ואכירה והנה לא אלהים שלחו כי הנבואה דבר עלי וטוביה וסנבלט שכרו׃ | 12 |
Ndinazindikira kuti Mulungu sanamutume koma kuti anayankhula mawu oloserawa motsutsana nane chifukwa Tobiya ndi Sanibalati anamulemba ntchitoyi.
למען שכור הוא למען אירא ואעשה כן וחטאתי והיה להם לשם רע למען יחרפוני׃ | 13 |
Iye analembedwa ntchitoyi ndi cholinga choti ine ndichite mantha, ndithawe. Ndikanatero ndiye kuti ndikanachimwira Yehova ndiponso iwowo akanandiyipitsira mbiri yanga ndi kumandinyoza.
זכרה אלהי לטוביה ולסנבלט כמעשיו אלה וגם לנועדיה הנביאה וליתר הנביאים אשר היו מיראים אותי׃ | 14 |
Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani Tobiya ndi Sanibalati chifukwa cha zimene achita. Kumbukiraninso mneneri wamkazi Nowadiya ndi aneneri amene akhala akufuna kundiopseza.”
ותשלם החומה בעשרים וחמשה לאלול לחמשים ושנים יום׃ | 15 |
Ndipo khoma linatsirizidwa kumanga pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli. Linamangidwa pa masiku okwana 52.
ויהי כאשר שמעו כל אויבינו ויראו כל הגוים אשר סביבתינו ויפלו מאד בעיניהם וידעו כי מאת אלהינו נעשתה המלאכה הזאת׃ | 16 |
Adani athu onse atamva izi, mitundu yonse ya anthu yozungulira inachita mantha ndi kuchita manyazi. Iwo anazindikira kuti ntchitoyo inachitika ndi thandizo la Mulungu wathu.
גם בימים ההם מרבים חרי יהודה אגרתיהם הולכות על טוביה ואשר לטוביה באות אליהם׃ | 17 |
Komanso masiku amenewo anthu olemekezeka a ku Yuda ankalemberana naye makalata ambiri ndi Tobiyayo,
כי רבים ביהודה בעלי שבועה לו כי חתן הוא לשכניה בן ארח ויהוחנן בנו לקח את בת משלם בן ברכיה׃ | 18 |
pakuti anthu ambiri a ku Yuda anali atalumbira kale kuti adzagwira naye ntchito popeza anali mkamwini wa Sekaniya mwana wa Ara, ndipo mwana wake Yehohanani anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.
גם טובתיו היו אמרים לפני ודברי היו מוציאים לו אגרות שלח טוביה ליראני׃ | 19 |
Kuwonjezera apo, anthu ankasimba za ntchito zake zabwino ine ndili pomwepo ndipo anakamuwululira mawu anga. Choncho Tobiyayo ankatumiza makalata ondiopseza.