< יחזקאל 9 >
וַיִּקְרָא בְאָזְנַי קוֹל גָּדוֹל לֵאמֹר קָרְבוּ פְּקֻדּוֹת הָעִיר וְאִישׁ כְּלִי מַשְׁחֵתוֹ בְּיָדֽוֹ׃ | 1 |
Pambuyo pake Yehova anandiyankhula mofuwula kuti, “Bwerani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense ali ndi chida chake mʼmanja.”
וְהִנֵּה שִׁשָּׁה אֲנָשִׁים בָּאִים ׀ מִדֶּרֶךְ־שַׁעַר הָעֶלְיוֹן אֲשֶׁר ׀ מָפְנֶה צָפוֹנָה וְאִישׁ כְּלִי מַפָּצוֹ בְּיָדוֹ וְאִישׁ־אֶחָד בְּתוֹכָם לָבֻשׁ בַּדִּים וְקֶסֶת הַסֹּפֵר בְּמָתְנָיו וַיָּבֹאוּ וַיַּעַמְדוּ אֵצֶל מִזְבַּח הַנְּחֹֽשֶׁת׃ | 2 |
Ndipo ndinaona anthu asanu ndi mmodzi akubwera kuchokera ku chipata chakumtunda chimene chimaloza kumpoto, aliyense ali ndi chida choopsa cha nkhondo mʼdzanja lake. Pagulu pawopa panali munthu wovala chovala chabafuta, atatenga zolembera pambali pake. Iwo analowa ndi kuyima pambali pa guwa lamkuwa.
וּכְבוֹד ׀ אֱלֹהֵי יִשְׂרָאֵל נַעֲלָה מֵעַל הַכְּרוּב אֲשֶׁר הָיָה עָלָיו אֶל מִפְתַּן הַבָּיִת וַיִּקְרָא אֶל־הָאִישׁ הַלָּבֻשׁ הַבַּדִּים אֲשֶׁר קֶסֶת הַסֹּפֵר בְּמָתְנָֽיו׃ | 3 |
Tsono ulemerero wa Mulungu wa Israeli unakwera kuchokera pamwamba pa akerubi, pamene unali, ndipo unafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Pamenepo Yehova anayitana munthu amene anavala chovala chabafuta uja amene anatenga zolembera pambali pake
וַיֹּאמֶר יְהוָה אלו אֵלָיו עֲבֹר בְּתוֹךְ הָעִיר בְּתוֹךְ יְרֽוּשָׁלָ͏ִם וְהִתְוִיתָ תָּו עַל־מִצְחוֹת הָאֲנָשִׁים הַנֶּֽאֱנָחִים וְהַנֶּאֱנָקִים עַל כָּל־הַתּוֹעֵבוֹת הַֽנַּעֲשׂוֹת בְּתוֹכָֽהּ׃ | 4 |
ndipo anamuwuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu ndi kuyika chizindikiro pamphumi pa anthu amene akumva chisoni ndi kulira chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene zikuchitika mu mzindamo.”
וּלְאֵלֶּה אָמַר בְּאָזְנַי עִבְרוּ בָעִיר אַחֲרָיו וְהַכּוּ על־אַל־תָּחֹס עיניכם עֵינְכֶם וְאַל־תַּחְמֹֽלוּ׃ | 5 |
Kenaka ndinamva Yehova akuwuza anthu ena aja kuti, “Mutsateni mu mzinda wonse ndipo mukakanthe aliyense mopanda kumvera chisoni kapena chifundo.
זָקֵן בָּחוּר וּבְתוּלָה וְטַף וְנָשִׁים תַּהַרְגוּ לְמַשְׁחִית וְעַל־כָּל־אִישׁ אֲשֶׁר־עָלָיו הַתָּו אַל־תִּגַּשׁוּ וּמִמִּקְדָּשִׁי תָּחֵלּוּ וַיָּחֵלּוּ בָּאֲנָשִׁים הַזְּקֵנִים אֲשֶׁר לִפְנֵי הַבָּֽיִת׃ | 6 |
Mukaphe kotheratu anthu okalamba, anyamata ndi atsikana, makanda ndi akazi koma musakakhudze wina aliyense amene ali ndi chizindikiro. Muyambire ku Nyumba yanga yopatulika.” Motero iwo anayamba ndi akuluakulu amene anali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
וַיֹּאמֶר אֲלֵיהֶם טַמְּאוּ אֶת־הַבַּיִת וּמַלְאוּ אֶת־הַחֲצֵרוֹת חֲלָלִים צֵאוּ וְיָצְאוּ וְהִכּוּ בָעִֽיר׃ | 7 |
Ndipo Yehova anawawuza kuti, “Ipitsani Nyumba ya Mulungu ndipo mudzaze mabwalo ake ndi anthu akufa. Pitani.” Choncho iwo anapita nayamba kupha anthu mu mzinda monse.
וַֽיְהִי כְּהַכּוֹתָם וְנֵֽאשֲׁאַר אָנִי וָאֶפְּלָה עַל־פָּנַי וָאֶזְעַק וָֽאֹמַר אֲהָהּ אֲדֹנָי יְהוִה הֲמַשְׁחִית אַתָּה אֵת כָּל־שְׁאֵרִית יִשְׂרָאֵל בְּשָׁפְכְּךָ אֶת־חֲמָתְךָ עַל־יְרוּשָׁלָֽ͏ִם׃ | 8 |
Pamene iwo ankapha anthu, ine ndinatsala ndekha. Tsono ndinadzigwetsa chafufumimba ndi kufuwula kuti, “Aa, Ambuye Yehova! Kodi mwawakwiyiratu anthu a ku Yerusalemu motero kuti mudzawononga kotheratu anthu onse otsala ku Israeli?”
וַיֹּאמֶר אֵלַי עֲוֺן בֵּֽית־יִשְׂרָאֵל וִֽיהוּדָה גָּדוֹל בִּמְאֹד מְאֹד וַתִּמָּלֵא הָאָרֶץ דָּמִים וְהָעִיר מָלְאָה מֻטֶּה כִּי אָמְרוּ עָזַב יְהוָה אֶת־הָאָרֶץ וְאֵין יְהוָה רֹאֶֽה׃ | 9 |
Iye anandiyankha kuti, “Tchimo la Aisraeli ndi Yuda ndi lalikulu kwambiri; dziko ladzaza ndi zophana ndipo mu mzinda mwadzaza ndi zosalungama. Iwo akunena kuti, ‘Yehova walisiya dziko lake; Yehova sakuona.’
וְגַם־אֲנִי לֹא־תָחוֹס עֵינִי וְלֹא אֶחְמֹל דַּרְכָּם בְּרֹאשָׁם נָתָֽתִּי׃ | 10 |
Choncho sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka, koma Ine ndidzawalanga potsata zochita zawo.”
וְהִנֵּה הָאִישׁ ׀ לְבֻשׁ הַבַּדִּים אֲשֶׁר הַקֶּסֶת בְּמָתְנָיו מֵשִׁיב דָּבָר לֵאמֹר עָשִׂיתִי כאשר כְּכֹל אֲשֶׁר צִוִּיתָֽנִי׃ | 11 |
Ndipo munthu wovala chovala chabafuta uja atatenga zolembera pambali pake anadzafotokozera Yehova kuti, “Ndachita monga munandilamulira.”