< Esdras 8 >
1 Voici les chefs de famille — avec leur généalogie, — de ceux qui montèrent avec moi de Babylone, sous le règne du roi Artaxerxès.
Nawa mayina a atsogoleri a mabanja amene anabwera nane kuchokera ku Babuloni nthawi ya ulamuliro wa mfumu Aritasasita:
2 Des fils de Phinées, Gersom; des fils d’Ithamar, Daniel; des fils de David, Hattus,
Geresomu wa fuko la Finehasi; Danieli wa fuko la Itamara; Hatusi
3 qui descendait de Séchénias; des fils de Pharos, Zacharie, et avec lui cent cinquante mâles inscrits dans le registre de famille.
mwana wa Sekaniya wa fuko la Davide; Zekariya wa fuko la Parosi. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwa anthu ena 150;
4 Des fils de Phahath-Moab, Elioénaï, fils de Zaréhias, et avec lui deux cents mâles;
Elihunai mwana wa Zerahiya, wa fuko la Pahati-Mowabu. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu ena 400.
5 des fils de Séchénias, fils d’Ezéchiel, et avec lui trois cents mâles;
Sekaniya, mwana wa Yahazieli wa fuko la Zatu. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwanso anthu 300.
6 des fils d’Adin, Abed, fils de Jonathan, et avec lui cinquante mâles;
Ebedi, mwana wa Yonatani wa fuko la Adini. Pamodzi naye analembedwanso anthu ena makumi asanu.
7 des fils d’Elam, Isaïe, fils d’Athalias, et avec lui soixante-dix mâles;
Yesaiya, mwana wa Ataliya wa fuko la Elamu. Pamodzi naye panali anthu ena 70.
8 des fils de Saphatias, Zébédias, fils de Michaël, et avec lui quatre-vingts mâles;
Zebadiya, mwana wa Mikayeli wa fuko la Sefatiya. Pamodzi naye panalinso anthu 80.
9 des fils de Joab, Obédias, fils de Jéhiel, et avec lui deux cent dix-huit mâles;
Obadiya, mwana wa Yehieli wa fuko la Yowabu. Pamodzi naye panalinso anthu 218.
10 des fils de Selomith, fils de Joséphias, et avec lui cent soixante mâles;
Selomiti mwana wa Yosifiya wa fuko la Bani. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu 160.
11 des fils de Bébaï, Zacharie, fils de Bébaï, et avec lui vingt-huit mâles;
Zekariya, mwana wa Bebai wa fuko la Babai. Pamodzi naye analembedwanso anthu 28.
12 des fils d’Azgad, Johanan, fils d’Eccétan, et avec lui cent dix mâles;
Yohanani, mwana wa Hakatani wa fuko la Azigadi. Pamodzi naye panalinso anthu 110.
13 des fils d’Adonicam, les derniers, dont voici les noms: Eliphélet, Jéhiel et Samaïas, et avec eux soixante mâles;
Atsogoleri a fuko la Adonikamu, anthu amene anabwera pambuyo pake mayina awo anali Elifeleti, Yeiyeli ndi Semaya. Pamodzi ndi iwowa panalinso anthu 60.
14 des fils de Béguaï, Uthaï et Zachur, et avec eux soixante-dix mâles.
Atsogoleri a fuko la Bigivai anali Utai ndi Zakuri. Pamodzi ndi iwowa panali anthu 70.
15 Je les rassemblai près de la rivière qui coule vers Ahava, et nous campâmes là trois jours. Ayant porté mon attention sur le peuple et sur les prêtres, je ne trouvai là aucun des fils de Lévi.
Anthu onse ndinawasonkhanitsa ku mtsinje umene umapita mpaka ku Ahava, ndipo kumeneko tinagona mʼmisasa masiku atatu. Nditayangʼana pakati pa anthu ndi ansembe, ndinapeza kuti panalibe Alevi.
16 Alors je fis appeler les chefs Eliézer, Ariel, Séméïas, Elnathan, Jarib, un autre Elnathan, Nathan, Zacharie et Mosollam, ainsi que les docteurs Joïarib et Elnathan.
Choncho ndinayitana atsogoleri awa: Eliezara, Arieli, Semaiya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi awiri, Yoyaribu ndi Elinatani,
17 Je les envoyai vers le chef Eddo, à l’endroit appelé Chasphia, et je mis dans leur bouche les paroles qu’ils devaient dire à Eddo et à ses frères les Nathinéens qui étaient à l’endroit appelé Chasphia, afin qu’ils nous amenassent des ministres pour la maison de notre Dieu.
ndipo ndinawatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ine ndinawawuza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu.
18 Et comme la main bienfaisante de notre Dieu était sur nous, ils nous amenèrent un homme intelligent, d’entre les fils de Moholi, fils de Lévi, fils d’Israël, savoir Sarabias, et avec lui ses fils et ses frères au nombre de dix-huit;
Chifukwa cha kutikomera mtima kwa Mulungu wathu, Ido anatitumizira munthu wanzeru, Serabiya, wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israeli, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi abale ake, anthu 18.
19 Hasabias, et avec lui Isaïe, d’entre les fils de Mérari,
Anatitumiziranso Hasabiya ndi Yesaiya wa fuko la Merari pamodzi ndi abale ake ndi adzukulu ake, anthu makumi awiri.
20 ses frères et leurs fils au nombre de vingt; et d’entre les Nathinéens, que David et les chefs avaient donnés pour le service des lévites, deux cent vingt Nathinéens, tous nominativement désignés.
Panalinso anthu ena 220 mwa anthu ogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amene Davide ndi nduna zake anawasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onsewa analembedwa potsata mayina awo.
21 Je publiai là, près de la rivière d’Ahava, un jeûne pour nous affliger devant notre Dieu, afin d’implorer de lui un heureux voyage pour nous, pour nos enfants et pour tout ce qui nous appartenait.
Ku mtsinje wa Ahava, ndinalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kupempha kuti atiyendetse bwino ife ndi ana athu, ndi kuteteza katundu wathu yense.
22 Car j’aurais eu honte de demander au roi une escorte et des cavaliers pour nous secourir contre l’ennemi pendant la route, parce que nous avions dit au roi: « La main de notre Dieu est pour leur bien sur tous ceux qui le cherchent, mais sa force et sa colère sont sur tous ceux qui l’abandonnent. »
Ine ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti atipatse asilikali oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo kuti atiteteze kwa adani athu pa ulendo wathuwu popeza tinali titawuza kale mfumu kuti “Yehova amateteza aliyense amene amamudalira, koma amakwiyira onse amene amamukana.”
23 Et à cause de cela nous jeûnâmes et nous invoquâmes notre Dieu; et il nous exauça.
Choncho tinasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze ndipo Iye anamva pemphero lathu.
24 Je choisis douze chefs des prêtres, Sarabias et Hasabias, et dix de leurs frères.
Tsono ndinasankha atsogoleri a ansembe khumi ndi awiri awa, Serebiya, Hasabiya ndi abale awo khumi
25 Je pesai devant eux l’argent, l’or et les ustensiles, offrande qu’avaient prélevée pour la maison de notre Dieu le roi, ses conseillers et ses chefs, et tous ceux d’Israël qui se trouvaient là;
ndipo ndinawayezera siliva ndi golide, ndiponso ziwiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi alangizi ake, nduna zake ndi Aisraeli onse amene anali kumeneko anazipereka.
26 et je pesai, en les remettant entre leurs mains, six cent cinquante talents d’argent, des ustensiles d’argent de la valeur de cent talents, cent talents d’or,
Nditayeza zonse, ndinapereka mʼmanja mwawo, matani 22 asiliva, ziwiya zasiliva zolemera makilogalamu 70, ndiponso makilogalamu 3,400 a golide,
27 vingt coupes d’or de la valeur de mille dariques, et deux vases d’un bel airain brillant, aussi précieux que l’or.
mbale zagolide makumi awiri zolemera makilogalamu asanu ndi atatu ndi theka ndiponso ziwiya ziwiri zamkuwa wosalala, wonyezimira bwino ngati golide wamtengowapatali.
28 Et je leur dis: « Vous êtes saints devant Yahweh, et ces ustensiles sont saints, cet argent et cet or sont une offrande volontaire à Yahweh, Dieu de vos pères.
Kenaka ndinawawuza kuti, “Inu ndi opatulika a Yehova, ndiponso mphatso zonsezi ndi zopatulika. Siliva ndi golideyu ndi zopereka zaufulu kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu.
29 Soyez vigilants à les garder, jusqu’à ce que vous les pesiez devant les chefs des prêtres et des lévites, et devant les chefs de famille d’Israël, à Jérusalem, dans les chambres de la maison de Yahweh. »
Muzisamale bwino mpaka mutaziyeza pamaso pa atsogoleri a ansembe ndi Alevi ndi akulu a mabanja a Israeli mʼzipinda za mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu.”
30 Et les prêtres et les lévites reçurent au poids l’argent, l’or et les ustensiles, pour les porter à Jérusalem dans la maison de notre Dieu.
Choncho ansembe ndi Alevi analandira zonse zoyezedwa zija, siliva, golide pamodzi ndi ziwiya kuti apite nazo ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.
31 Nous partîmes de la rivière d’Ahava le douzième jour du premier mois, pour nous rendre à Jérusalem. La main de notre Dieu fut sur nous, et nous sauva des mains de l’ennemi et des embûches pendant la route.
Pa tsiku la khumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, tinachoka ku mtsinje wa Ahava kupita ku Yerusalemu. Ndipo Mulungu wathu anali nafe, ndipo anatiteteza kwa adani athu makamaka otibisalira pa njira.
32 Arrivés à Jérusalem, nous nous y reposâmes trois jours.
Tinafika ku Yerusalemu, komwe tinapumula masiku atatu.
33 Le quatrième jour, l’argent, l’or et les ustensiles furent pesés, dans la maison de notre Dieu, entre les mains de Mérimuth, fils d’Urie, le prêtre; il y avait avec lui Eléazar, fils de Phinées et avec eux les lévites Jozabad, fils de Josué, et Noadias, fils de Bennui.
Pa tsiku la chinayi lake, mʼNyumba ya Mulungu wathu, tinayeza siliva ndi golide ndi ziwiya zija nʼkuzipereka mʼmanja mwa Meremoti mwana wa wansembe Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eliezara mwana wa Finehasi ndiponso Alevi awa: Yozabadi mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binuyi.
34 Le tout fut livré selon le nombre et selon le poids; et le poids total fut mis par écrit en ce temps-là.
Zonsezi anaziwerenga ndi kuziyeza ndipo analemba kulemera kwa chinthu chilichonse.
35 Ceux qui revenaient de l’exil, les fils de la captivité, offrirent en holocauste au Dieu d’Israël douze taureaux pour tout Israël, quatre-vingt-seize béliers, soixante-dix-sept agneaux, douze boucs pour le péché, le tout en holocauste à Yahweh.
Pamenepo anthu amene anatengedwa ukapolo aja anabwerera, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israeli: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, kuperekera Aisraeli onse, nkhosa zazimuna 96, ana ankhosa 77, ndiponso mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri ngati nsembe yopepesera machimo. Zonsezi zinali nsembe yopsereza zopereka kwa Yehova.
36 Ils transmirent les ordres du roi aux satrapes du roi et aux gouverneurs d’au delà du fleuve, et ceux-ci soutinrent le peuple et la maison de Dieu.
Iwo anaperekanso chidziwitso cha mfumu chija kwa akuluakulu a mfumu ndi kwa akazembe a mʼdera la Patsidya pa Yufurate. Pamenepo iwo anathandiza Ayuda ndiponso ntchito za pa Nyumba ya Mulungu.