< Genesis 11 >

1 So it came to pass that, all the earth, was of one manner of speech, —and of one stock of words.
Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi.
2 And it came to pass as they brake away onwards, that they found a plain in the land of Shinar, and dwelt there.
Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.
3 Then said they, each man to his friend, Come on! let us make bricks, and burn them thoroughly, —So the bricks, served them for stone, and bitumen, served them for mortar,
Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.
4 And they said Come on! let us build for ourselves a city, and a tower with its head in the heavens, so let us make for ourselves a name, —lest we be scattered abroad over the face of all the earth.
Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
5 And Yahweh came down, to behold the city, and the tower, —which the sons of men had built.
Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga.
6 Then said Yahweh: Lo! one people and one manner of speech, have they all, this, then is what they have begun to do, —now, therefore, nothing will be withholden from them which they may plan to do.
Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita.
7 Come on! let us go down, and there confuse their speech, —that they may not understand, each man the speech of his friend.
Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”
8 So Yahweh scattered them from thence over the face of all the earth, —and so they left off building the city.
Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo.
9 For this cause, was the name thereof called Babel ["Confusion"]; because there, did Yahweh confuse the speech of all the earth, —and, from thence, did Yahweh scatter them abroad, over the face of all the earth.
Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
10 These, are the genealogies of Shem, Shem was a hundred years old when he begat Arpachshad, two years after the flood
Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi.
11 and Shem lived after he begat Arpachshad, five hundred years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
12 And, Arpachshad, lived thirty-five years, —and begat Shelah;
Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela.
13 and Arpachshad lived after he begat Shelah, four hundred and three years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
14 And, Shelah, lived thirty years, —and begat Eber;
Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi.
15 and Shelah lived, after he begat Eber, four hundred and three years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
16 And Eber lived thirty-four years, —and begat Peleg;
Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi.
17 and Eber lived after he begat Peleg, four hundred and thirty years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
18 And Peleg lived thirty years, and begat Reu:
Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu.
19 and Peleg lived after he begat Reu, two hundred and nine years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
20 And Reu lived thirty-two years—and begat Serug;
Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi.
21 and Reu lived after he begat Serug, two hundred and seven years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
22 And Serug lived thirty years, —and begat Nahor;
Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori.
23 and Serug lived after he begat Nahor, two hundred years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
24 And Nahor lived twenty-nine years, —and begat Terah;
Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera.
25 and Nahor lived, after he begat Terah, a hundred and nineteen years, —and begat sons and daughters.
Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
26 And Terah lived seventy years, —and begat Abram, Nahor, and Haran.
Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
27 These, then are the generations of Terah, Terah begat Abram, Nahor, and Haran, —and, Haran, begat Lot;
Nayi mibado yochokera mwa Tera. Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti.
28 and Haran died, in the presence of Terah his father, —in the land of his birth, in Ur of the Chaldees.
Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira.
29 And Abram and Nahor took to themselves wives; the name of Abram’s wife, was Sarai; and, the name of Nahor’s wife, Milcah, daughter of Haran father of Milcah, and father of Iscah.
Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani.
30 And, Sarai, remained barren, —she had no child,
Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.
31 And Terah took Abram his son and Lot son of Haran his son’s son, and Sarai his daughter-in-law, wife of Abram his son, —and came forth with them out of Ur of the Chaldees, that they might go their way towards the land of Canaan, and they came in as far as Haran and dwelt there.
Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
32 And the days of Terah were two hundred and five years, —and Terah died in Haran.
Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.

< Genesis 11 >