< Acts 5 >
1 But a certain man named Ananias, with Sapphira his wife, sold a possession,
Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo.
2 and kept back part of the price, his wife also having knowledge of it; and brought a certain part, and laid it at the feet of the apostles.
Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi.
3 But Peter said, Ananias, why did Satan fill thy heart that thou shouldst lie to the Holy Spirit, and keep back part of the price of the land?
Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama?
4 While it remained, was it not thine own? And after it was sold, was it not in thine own power? Why didst thou conceive this thing in thy heart? Thou didst not lie to men, but to God.
Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.”
5 And Ananias, hearing these words, fell down, and expired. And great fear came on all that heard of it.
Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi namwalira. Onse amene anamva zimene zinachitikazi anachita mantha kwambiri.
6 And the young men arose, and wrapt him up, and carried him out, and buried him.
Kenaka anyamata anafika, nakulunga thupi lake, ndipo anamunyamula ndi kukamuyika mʼmanda.
7 And it was about the space of three hours after, when his wife, not knowing what had happened, came in.
Patapita maora atatu mkazi wake analowa, wosadziwa zimene zinachitika.
8 Peter said to her, Tell me whether ye sold the land for so much. And she said, Yes, for so much.
Petro anamufunsa iye kuti, “Tandiwuza, kodi izi ndi ndalama zonse zimene iwe ndi Hananiya munalandira mutagulitsa munda?” Mkaziyo anati, “Inde ndi zimenezo.”
9 And Peter said to her, Why is it that ye agreed together to try the Spirit of the Lord? Lo! the feet of those who have buried thy husband are at the door, and they will carry thee out.
Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.”
10 And she fell down immediately at his feet, and expired; and the young men, when they came in, found her dead, and carried her out, and buried her by her husband.
Nthawi yomweyo anagwa pansi pa mapazi a Petro ndipo anamwalira. Ndipo anyamata aja analowa, napeza kuti wafa kale, anamunyamula ndi kukamuyika pafupi ndi mwamuna wake.
11 And great fear came upon all the church, and upon all that heard of these things.
Mpingo wonse ndi anthu onse amene anamva zimenezi anachita mantha kwambiri.
12 And many signs and wonders were wrought among the people by the hands of the apostles; and they were all with one accord in Solomon's porch.
Atumwi anachita zizindikiro zodabwitsa ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Ndipo onse okhulupirira ankasonkhana pamodzi mu Khonde la Solomoni.
13 But of the rest no one dared to join himself to them. But the people highly honored them;
Palibe ndi mmodzi yemwe analimba mtima kuphatikana nawo, ngakhale kuti anthu onse amawalemekeza kwambiri.
14 and more and more were believers added to the Lord, multitudes both of men and women;
Ngakhale zinali chotere, anthu ambiri anakhulupirira Ambuye ndipo amawonjezeredwa ku chiwerengero chawo.
15 so that in the streets they brought out the sick, and laid them on beds and couches, in order that at least the shadow of Peter, as he passed, might overshadow some of them.
Chifukwa cha zimenezi, anthu anabweretsa odwala mʼmisewu ya mu mzinda nawagoneka pa mabedi ndi pa mphasa kuti chithunzi chokha cha Petro chikhudze ena mwa iwo iye akamadutsa.
16 The multitude also belonging to the cities around came together to Jerusalem bringing the sick, and those plagued by unclean spirits; and they were all healed.
Anthu ochuluka ochokera ku mizinda yayingʼono ozungulira Yerusalemu amasonkhananso atatenga odwala awo ndi iwo amene amasautsidwa ndi mizimu yoyipa ndipo onsewo amachiritsidwa.
17 But the high-priest and all that were with him, which is the sect of the Sadducees, rose up and were filled with indignation,
Koma mkulu wa ansembe pamodzi ndi onse omuthandiza, amene anali a gulu la Asaduki, anachita nsanje.
18 and laid hands on the apostles, and put them in the public prison.
Iwo anagwira atumwi ndi kuwatsekera mʼndende ya anthu wamba.
19 But an angel of the Lord in the night opened the prison-doors, and brought them forth and said,
Koma usiku mngelo wa Ambuye anatsekula zitseko za ndende ndi kuwatulutsa
20 Go, stand and speak in the temple to the people all the words of this life.
Mngeloyo anati, “Pitani, ku mabwalo a Nyumba ya Mulungu ndipo mukawuze anthu uthenga onse wamoyo watsopanowu.”
21 And hearing this, they went into the temple at daybreak and taught. But the high-priest and they that were with him came and called together the council, and all the elders of the sons of Israel, and sent to the prison to have them brought.
Kutacha mmawa, atumwi analowa mʼbwalo la mʼNyumba ya Mulungu, monga anawuzidwa ndipo anayamba kuphunzitsa anthu. Mkulu wa ansembe pamodzi ndi omuthandiza ake amene anali naye anafika, anayitanitsa msonkhano wa Bwalo Lalikulu, ndilo bwalo la akulu onse a Israeli. Anatuma alonda kuti akatenge atumwi aja kundende.
22 But the officers that came did not find them in the prison; and they returned and brought word,
Koma alonda aja atafika kundende, sanawapezemo. Iwo anabwerera nakawafotokozera
23 saying, The prison we found shut in all security and the keepers standing at the doors: but when we opened them, we found no one within.
kuti, “Tinakapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndi alonda atayimirira pa khomo, koma pamene tinatsekula zitseko, sitinapezemo munthu aliyense mʼkatimo.”
24 And when the priest, and the captain of the temple, and the chief priests heard these words, they were at a loss concerning them, to what this would come.
Mkulu wa alonda a Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe atamva zimenezi anathedwa nzeru, osadziwa kuti zimenezi zidzatha bwanji.
25 But one came and brought them word, Lo! the men whom ye put in prison are standing in the temple and teaching the people.
Ndipo wina anabwera ndi kuti, “Taonani! Anthu aja amene munawatsekera mʼndende ali ku Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.”
26 Then went the captain with the officers, and brought them without violence, that they might not be stoned; for they feared the people.
Pamenepo mkulu wa alonda pamodzi ndi alonda anakawatenga atumwi. Sanakawatenge mwaukali, chifukwa amaopa kuti anthu angawaponye miyala.
27 And having brought them, they set them before the council. And the high-priest questioned them,
Atafika nawo atumwi aja, anawayimika pamaso pa Bwalo Lalikulu kuti afunsidwe mafunso ndi mkulu wa ansembe.
28 saying, We strictly commanded you not to teach in this name, and lo! ye have filled Jerusalem with your teaching, and mean to bring this man's blood upon us.
Iye anati, “Ife tinakuletsani kuti musaphunzitsenso mʼdzina ili, koma inu mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mukufuna kutisenzetsa imfa ya munthu ameneyu.”
29 But Peter and the apostles answered and said, We ought to obey God rather than men.
Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu!
30 The God of our fathers raised up Jesus, whom ye slew by hanging him on a cross;
Mulungu wa makolo athu anamuukitsa Yesu, amene inu munamupha pomupachika pa mtengo.
31 him hath God exalted by his right hand, as a Leader and Saviour, to give repentance to Israel, and forgiveness of sins.
Mulungu anamukweza Iye ku dzanja lake lamanja kukhala Mfumu ndi Mpulumutsi kuti Iye apatse Aisraeli mtima wolapa ndi chikhululukiro cha machimo.
32 And we are his witnesses of these things, and so also is the Holy Spirit which God hath given to those who obey him.
Ife ndife mboni za zimenezi, ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu anapereka kwa iwo akumvera Iye.”
33 But when they heard this, they were filled with rage, and were resolving to kill them.
Akuluakuluwo atamva zimenezi anakwiya kwambiri nafuna kuwapha.
34 But there stood up one in the council, a Pharisee, named Gamaliel, a doctor of the law, in high esteem with all the people, and commanded to put the men forth a little while,
Koma Mfarisi wina dzina lake Gamalieli, mphunzitsi wa malamulo, amene anthu onse amamulemekeza, anayimirira ndi kulamula kuti atumwiwo ayambe apita panja.
35 and said to them [[of the council]], Men of Israel, take heed to yourselves as to what ye are about to do in respect to these men.
Ndipo iye anawuza bwalolo kuti, “Aisraeli, taganizani bwino, zimene mukufuna kuchita kwa anthu awa.
36 For before these days arose Theudas, boasting himself to be somebody; to whom a number of men, about four hundred, joined themselves: who was slain, and all, as many as obeyed him, were scattered, and came to nought.
Pakuti masiku a mʼmbuyomu kunali Teuda amene anadzitchukitsa, ndipo anthu pafupifupi 400 anamutsatira. Iye anaphedwa ndipo omutsatira akewo anabalalitsidwa, zonse zinatheratu.
37 After this man arose Judas the Galilaean, in the days of the registering, and drew people away after him; he also perished, and all, as many as obeyed him, were dispersed.
Pambuyo pake, nthawi ya kalembera kunalinso Yudasi wa ku Galileya, ndipo anatsogolera gulu la anthu amene anawukira, iyenso anaphedwa ndipo anthu ake onse anabalalitsidwa.
38 And now I say to you, Refrain from these men, and let them alone; for if this design or this work be of men, it will come to nought;
Chifukwa chake pa nkhani iyi ndikuwuzani kuti, alekeni anthuwa ndipo aloleni apite! Pakuti ngati zimene akuganiza kapena kuchita ndi zochokera kwa munthu zidzalephera.
39 but if it be of God, ye will not be able to overthrow them; lest haply ye be found also fighting against God.
Koma ngati ndi zochokera kwa Mulungu inu simudzatha kuwaletsa anthu awa: inu mwina muzapezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”
40 And they were persuaded by him; and having called the apostles, they beat them, and commanded them not to speak in the name of Jesus, and released them.
Akuluakulu enawo anavomerezana naye. Iwo anayitana atumwi aja ndipo anawakwapula kwambiri. Ndipo anawalamula kuti asayankhulenso mʼdzina la Yesu ndipo anawamasula.
41 They therefore went away from the presence of the council, rejoicing that they were counted worthy to suffer shame in behalf of that name;
Iwo anachoka ku Bwalo Lalikulu akukondwa chifukwa anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu.
42 and every day, in the temple, and in houses, they ceased not to teach, and to publish the glad tidings concerning Jesus the Christ.
Ndipo tsiku ndi tsiku, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira mʼNyumba ya Mulungu komanso nyumba ndi nyumba, Uthenga Wabwino wa kuti Yesu ndi Khristu.