< 2 Corinthians 8 >

1 Moreover, brethren, we make known to you the charity of God, which is given by the congregations of Macedonia;
Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya.
2 that in a great trial of affliction, the abundance of their joy, and their extreme poverty, superabounded to the riches of their liberality:
Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri.
3 that to their power, (I bear witness, ) yes, beyond their power, they were willing of themselves; with much entreaty
Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa,
4 requesting us to accept the charity and the participation of the service, which is for the saints.
ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya.
5 Yes, beyond our expectations; for they first gave themselves to the Lord, and to us through the will of God.
Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu.
6 This moved us to entreat Titus, that as he had formerly begun, so he would also finish the same charity among you likewise.
Choncho tinamupempha Tito kuti atsirize poti nʼkuti atayamba kale ntchito yachisomoyi pakati panu.
7 Now as you abound in every gift, (in faith, and speech, and knowledge, and all diligence, and in your love to us, ) I wish that you may abound in this gift also.
Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka.
8 I speak not this as an injunction, but on account of the diligence of others, and to prove the sincerity of your love.
Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena.
9 (For you know the charity of our Lord Jesus Christ, that though he was rich, yet for your sake he became poor; that you, through his poverty, might be rich.)
Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.
10 And in this I give my opinion, not only to do, but also to be willing since the last year.
Ndipo nawa malangizo anga pa zoyenera inu kuchita pa nkhaniyi. Chaka chatha munali oyamba, osati ongofuna kupereka kokha komanso okhala ndi mtima ofuna kupereka.
11 At present, therefore, finish the doing of it; that as there was a readiness to will; so also let there be to finish, according to your ability.
Tsopano tsirizani ntchitoyi, ndipo changu chanu chofunitsitsa kugwira ntchitoyi ndi kuyitsiriza chichitike molingana ndi zimene muli nazo.
12 For if there be a willing mind, according to what a person has, he is accepted; and not according to what he has not.
Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.
13 However, I mean not that others should be eased and you distressed; but on account of equality,
Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana.
14 that now your abundance may be a supply for their want; that again, their abundance may be a supply for your want; that there may be an equality.
Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana,
15 As it is written, "He who gathered much, had nothing over; and he who gathered little, had no lack."
monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.”
16 Now thanks be to God, who has put the same earnest care concerning you, into the heart of Titus.
Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu.
17 For he, indeed, received an exhortation; but from his great earnestness, was going to you of his own accord.
Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha.
18 And with him we have sent the brother, whose praise in the gospel is throughout all the congregations.
Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino.
19 And not only so, but who was also chosen by the congregations our fellow-traveler, with this charity, which is ministered by us, to the glory of the Lord himself, and of your readiness:
Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza.
20 using this precaution, that none may blame us in the distribution of this abundance;
Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi.
21 premeditating things comely, not only in the sight of the Lord, but also in sight of men.
Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.
22 And we have sent with them our brother, whom we have oftentimes found diligent in many things; but now much more diligent, from the great confidence which he has in you.
Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu.
23 If any inquire concerning Titus, he is my partner and fellow-laborer for you; or if our brethren be inquired of, they are Apostles of congregations, and a glory of Christ.
Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu.
24 Wherefore, the proof of your love, and of our boasting concerning you, display before them, and before the face of the congregations.
Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.

< 2 Corinthians 8 >