< Hebrews 10 >
1 For the Law hauing the shadowe of good things to come, and not the very image of the things, can neuer with those sacrifices, which they offer yeere by yeere continually, sanctifie the commers thereunto.
Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza.
2 For would they not then haue ceased to haue bene offered, because that the offerers once purged, should haue had no more conscience of sinnes?
Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo.
3 But in those sacrifices there is a remembrance againe of sinnes euery yeere.
Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka.
4 For it is vnpossible that the blood of bulles and goates should take away sinnes.
Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.
5 Wherefore when he commeth into the world, he saith, Sacrifice and offring thou wouldest not: but a body hast thou ordeined me.
Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati, “Simunafune nsembe kapena zopereka, koma thupi munandikonzera.
6 In burnt offerings, and sinne offrings thou hast had no pleasure.
Simunakondwere nazo nsembe zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.
7 Then I sayd, Lo, I come (In the beginning of the booke it is written of me) that I should doe thy will, O God.
Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’”
8 Aboue, when he sayd, Sacrifice and offring, and burnt offrings, and sinne offrings thou wouldest not haue, neither hadst pleasure therein (which are offered by the Lawe)
Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe.
9 Then sayd he, Lo, I come to doe thy wil, O God, he taketh away the first, that he may stablish the second.
Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri.
10 By the which wil we are sanctified, euen by the offring of the body of Iesus Christ once made.
Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.
11 And euery Priest standeth dayly ministring, and oft times offreth one maner of offring, which can neuer take away sinnes:
Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo.
12 But this man after he had offered one sacrifice for sinnes, sitteth for euer at the right hand of God,
Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu.
13 And from hencefoorth tarieth, till his enemies be made his footestoole.
Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake.
14 For with one offering hath he consecrated for euer them that are sanctified.
Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.
15 For the holy Ghost also beareth vs record: for after that he had sayd before,
Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,
16 This is the Testament that I will make vnto them after those dayes, sayth the Lord, I wil put my Lawes in their heart, and in their mindes I will write them.
“Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo,” akutero Yehova. “Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo, ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”
17 And their sinnes and iniquities will I remember no more.
Ndipo akutinso: “Sindidzakumbukiranso konse machimo awo ndi zolakwa zawo.”
18 Nowe where remission of these things is, there is no more offering for sinne.
Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.
19 Seeing therefore, brethren, that by the blood of Iesus we may be bolde to enter into the Holy place,
Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu.
20 By the newe and liuing way, which hee hath prepared for vs, through the vaile, that is, his flesh:
Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake.
21 And seeing we haue an hie Priest, which is ouer the house of God,
Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu.
22 Let vs drawe neere with a true heart in assurance of faith, our hearts being pure from an euill conscience,
Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera.
23 And washed in our bodies with pure water, let vs keepe the profession of our hope, without wauering, (for he is faithfull that promised)
Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.
24 And let vs consider one another, to prouoke vnto loue, and to good workes,
Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino.
25 Not forsaking the fellowship that we haue among our selues, as the maner of some is: but let vs exhort one another, and that so much the more, because ye see that the day draweth neere.
Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
26 For if we sinne willingly after that we haue receiued and acknowledged that trueth, there remaineth no more sacrifice for sinnes,
Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
27 But a fearefull looking for of iudgement, and violent fire, which shall deuoure the aduersaries.
Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu
28 He that despiseth Moses Law, dieth without mercy vnder two, or three witnesses:
Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu.
29 Of howe much sorer punishment suppose ye shall hee be worthy, which treadeth vnder foote the Sonne of God, and counteth the blood of the Testament as an vnholy thing, wherewith he was sanctified, and doeth despite the Spirit of grace?
Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?
30 For we know him that hath sayd, Vengeance belongeth vnto mee: I will recompense, saith the Lord. And againe, The Lord shall iudge his people.
Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”
31 It is a fearefull thing to fall into the hands of the liuing God.
Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.
32 Nowe call to remembrance the dayes that are passed, in the which, after ye had receiued light, ye endured a great fight in afflictions,
Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri.
33 Partly while yee were made a gazing stocke both by reproches and afflictions, and partly while ye became companions of them which were so tossed to and from.
Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere.
34 For both ye sorowed with mee for my bonds, and suffered with ioy the spoyling of your goods, knowing in your selues howe that ye haue in heauen a better, and an enduring substance.
Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.
35 Cast not away therefore your confidence which hath great recompense of reward.
Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.
36 For ye haue neede of patience, that after ye haue done the will of God, ye might receiue the promise.
Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza.
37 For yet a very litle while, and hee that shall come, will come, and will not tary.
Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe, Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
38 Nowe the iust shall liue by faith: but if any withdrawe himselfe, my soule shall haue no pleasure in him.
Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro. Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha, Ine sindidzakondwera naye.
39 But we are not they which withdrawe our selues vnto perdition, but follow faith vnto the conseruation of the soule.
Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.