< Colossians 2 >
1 For I woulde ye knewe what great fighting I haue for your sakes, and for them of Laodicea, and for as many as haue not seene my person in the flesh,
Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso.
2 That their heartes might be comforted, and they knit together in loue, and in all riches of the full assurance of vnderstanding, to know the mysterie of God, euen the Father, and of Christ:
Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu.
3 In whom are hid all the treasures of wisedome and knowledge.
Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso.
4 And this I say, lest any man shoulde beguile you with entising wordes:
Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake.
5 For though I be absent in the flesh, yet am I with you in the spirit, reioycing and beholding your order, and your stedfast faith in Christ.
Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.
6 As ye haue therefore receiued Christ Iesus the Lord, so walke in him,
Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo.
7 Rooted and built in him, and stablished in the faith, as ye haue bene taught, abouding therein with thankesgiuing.
Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.
8 Beware lest there be any man that spoile you through philosophie, and vaine deceit, through the traditions of men, according to the rudiments of the world, and not after Christ.
Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.
9 For in him dwelleth all the fulnesse of the Godhead bodily.
Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu.
10 And yee are complete in him, which is the head of all principalitie and power.
Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse.
11 In whome also yee are circumcised with circumcision made without handes, by putting off the sinfull body of the flesh, through the circumcision of Christ,
Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija.
12 In that yee are buried with him through baptisme, in whome ye are also raised vp together through the faith of the operation of God, which raised him from the dead.
Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.
13 And you which were dead in sinnes, and in the vncircumcision of your flesh, hath he quickened together with him, forgiuing you all your trespasses,
Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse.
14 And putting out the hand writing of ordinances that was against vs, which was contrarie to vs, hee euen tooke it out of the way, and fastened it vpon the crosse,
Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda.
15 And hath spoyled the Principalities, and Powers, and hath made a shew of them openly, and hath triumphed ouer them in the same crosse.
Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.
16 Let no man therefore condemne you in meate and drinke, or in respect of an holy day, or of the newe moone, or of the Sabbath dayes,
Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata.
17 Which are but a shadowe of thinges to come: but the body is in Christ.
Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu.
18 Let no man at his pleasure beare rule ouer you by humblenesse of minde, and worshipping of Angels, aduauncing himselfe in those thinges which hee neuer sawe, rashly puft vp with his fleshly minde,
Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu.
19 And holdeth not the head, whereof all the body furnished and knit together by ioyntes and bands, increaseth with the increasing of God.
Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.
20 Wherefore if ye be dead with Christ from the ordinances of the world, why, as though ye liued in ye world, are ye burdened with traditions?
Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa:
21 As, Touch not, Taste not, Handle not.
“Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?”
22 Which al perish with the vsing, and are after the commandements and doctrines of men.
Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe.
23 Which thinges haue in deede a shewe of wisdome, in voluntarie religion and humblenesse of minde, and in not sparing the body, which are thinges of no valewe, sith they perteine to the filling of the flesh.
Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.