< Psalms 86 >
1 A prayer of David. Incline Your ear, O LORD, and answer me, for I am poor and needy.
Pemphero la Davide. Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosowa.
2 Preserve my soul, for I am godly. You are my God; save Your servant who trusts in You.
Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu. Inu ndinu Mulungu wanga; pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga.
3 Be merciful to me, O Lord, for I call to You all day long.
Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.
4 Bring joy to Your servant, for to You, O Lord, I lift up my soul.
Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye, pakuti ndimadalira Inu.
5 For You, O Lord, are kind and forgiving, rich in loving devotion to all who call on You.
Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino, wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.
6 Hear my prayer, O LORD, and attend to my plea for mercy.
Yehova imvani pemphero langa; mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.
7 In the day of my distress I call on You, because You answer me.
Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu, pakuti Inu mudzandiyankha.
8 O Lord, there is none like You among the gods, nor any works like Yours.
Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye; palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.
9 All the nations You have made will come and bow before You, O Lord, and they will glorify Your name.
Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye; iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.
10 For You are great and perform wonders; You alone are God.
Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndiye Mulungu.
11 Teach me Your way, O LORD, that I may walk in Your truth. Give me an undivided heart, that I may fear Your name.
Ndiphunzitseni njira yanu Yehova, ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu; patseni mtima wosagawikana kuti ndilemekeze dzina lanu.
12 I will praise You, O Lord my God, with all my heart; I will glorify Your name forever.
Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.
13 For great is Your loving devotion to me; You have delivered me from the depths of Sheol. (Sheol )
Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine; mwandipulumutsa ku malo ozama a manda. (Sheol )
14 The arrogant rise against me, O God; a band of ruthless men seeks my life, with no regard for You.
Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufuna kundipha, amene salabadira za Inu.
15 But You, O Lord, are a compassionate and gracious God, slow to anger, abounding in loving devotion and faithfulness.
Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
16 Turn to me and have mercy; grant Your strength to Your servant; save the son of Your maidservant.
Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo; perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17 Show me a sign of Your goodness, that my enemies may see and be ashamed; for You, O LORD, have helped me and comforted me.
Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi, pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.