< Proverbs 2 >
1 My son, if you accept my words and hide my commandments within you,
Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,
2 if you incline your ear to wisdom and direct your heart to understanding,
ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;
3 if you truly call out to insight and lift your voice to understanding,
ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,
4 if you seek it like silver and search it out like hidden treasure,
ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,
5 then you will discern the fear of the LORD and discover the knowledge of God.
ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
6 For the LORD gives wisdom; from His mouth come knowledge and understanding.
Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
7 He stores up sound wisdom for the upright; He is a shield to those who walk with integrity,
Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo. Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
8 to guard the paths of justice and protect the way of His saints.
pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama. Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.
9 Then you will discern righteousness and justice and equity—every good path.
Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo, kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
10 For wisdom will enter your heart, and knowledge will delight your soul.
Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako, kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.
11 Discretion will watch over you, and understanding will guard you,
Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga; kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.
12 to deliver you from the way of evil, from the man who speaks perversity,
Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa, kwa anthu amabodza,
13 from those who leave the straight paths to walk in the ways of darkness,
amene amasiya njira zolungama namayenda mʼnjira zamdima,
14 from those who enjoy doing evil and rejoice in the twistedness of evil,
amene amakondwera pochita zoyipa namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.
15 whose paths are crooked and whose ways are devious.
Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota, ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.
16 It will rescue you from the forbidden woman, from the stranger with seductive words
Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo; kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,
17 who abandons the partner of her youth and forgets the covenant of her God.
amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.
18 For her house sinks down to death, and her tracks to the departed spirits.
Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa; njira zake zimamufikitsa ku manda.
19 None who go to her return or negotiate the paths of life.
Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera kapena kupezanso njira zamoyo.
20 So you will follow in the ways of the good, and keep to the paths of the righteous.
Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino, uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.
21 For the upright will inhabit the land, and the blameless will remain in it;
Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;
22 but the wicked will be cut off from the land, and the unfaithful will be uprooted.
Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo, ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.