< Numbers 34 >

1 Then the LORD said to Moses,
Yehova anawuza Mose kuti,
2 “Command the Israelites and say to them: When you enter the land of Canaan, it will be allotted to you as an inheritance with these boundaries:
“Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:
3 Your southern border will extend from the Wilderness of Zin along the border of Edom. On the east, your southern border will run from the end of the Salt Sea,
“‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere.
4 cross south of the Ascent of Akrabbim, continue to Zin, and go south of Kadesh-barnea. Then it will go on to Hazar-addar and proceed to Azmon,
Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni,
5 where it will turn from Azmon, join the Brook of Egypt, and end at the Sea.
kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.
6 Your western border will be the coastline of the Great Sea; this will be your boundary on the west.
“‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.
7 Your northern border will run from the Great Sea directly to Mount Hor,
“‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori
8 and from Mount Hor to Lebo-hamath, then extend to Zedad,
ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi,
9 continue to Ziphron, and end at Hazar-enan. This will be your boundary on the north.
ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
10 And your eastern border will run straight from Hazar-enan to Shepham,
“‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu.
11 then go down from Shepham to Riblah on the east side of Ain and continue along the slopes east of the Sea of Chinnereth.
Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti.
12 Then the border will go down along the Jordan and end at the Salt Sea. This will be your land, defined by its borders on all sides.”
Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere. “‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’”
13 So Moses commanded the Israelites, “Apportion this land by lot as an inheritance. The LORD has commanded that it be given to the nine and a half tribes.
Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka,
14 For the tribes of the Reubenites and Gadites, along with the half-tribe of Manasseh, have already received their inheritance.
chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo.
15 These two and a half tribes have received their inheritance across the Jordan from Jericho, toward the sunrise.”
Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
16 Then the LORD said to Moses,
Yehova anawuza Mose kuti,
17 “These are the names of the men who are to assign the land as an inheritance for you: Eleazar the priest and Joshua son of Nun.
“Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18 Appoint one leader from each tribe to distribute the land.
Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo.
19 These are their names: Caleb son of Jephunneh from the tribe of Judah;
Mayina awo ndi awa: Kalebe mwana wa Yefune, wochokera ku fuko la Yuda,
20 Shemuel son of Ammihud from the tribe of Simeon;
Semueli mwana wa Amihudi, wochokera ku fuko la Simeoni;
21 Elidad son of Chislon from the tribe of Benjamin;
Elidadi mwana wa Kisiloni, wochokera ku fuko la Benjamini;
22 Bukki son of Jogli, a leader from the tribe of Dan;
Buki mwana wa Yogili, mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;
23 Hanniel son of Ephod, a leader from the tribe of Manasseh son of Joseph;
Hanieli mwana wa Efodi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;
24 Kemuel son of Shiphtan, a leader from the tribe of Ephraim;
Kemueli mwana wa Sifitani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.
25 Eli-zaphan son of Parnach, a leader from the tribe of Zebulun;
Elizafani mwana wa Parinaki, mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;
26 Paltiel son of Azzan, a leader from the tribe of Issachar;
Palitieli mwana wa Azani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,
27 Ahihud son of Shelomi, a leader from the tribe of Asher;
Ahihudi mwana wa Selomi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;
28 and Pedahel son of Ammihud, a leader from the tribe of Naphtali.”
Pedaheli mwana wa Amihudi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”
29 These are the ones whom the LORD commanded to apportion the inheritance to the Israelites in the land of Canaan.
Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.

< Numbers 34 >