< Ezra 10 >

1 While Ezra prayed and made this confession, weeping and falling facedown before the house of God, a very large assembly of Israelites—men, women, and children—gathered around him, and the people wept bitterly as well.
Pamene Ezara ankapemphera ndi kuvomereza tchimo lawo, akulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, anthu ambiri anabwera kwa iye kudzasonkhana naye. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera mʼdziko lonse la Israeli ndipo ankalira kwambiri.
2 Then Shecaniah son of Jehiel, an Elamite, said to Ezra: “We have been unfaithful to our God by marrying foreign women from the people of the land, yet in spite of this, there is hope for Israel.
Ndipo Sekaniya, mwana wa Yehieli, wa fuko la Elamu, anawuza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mayiko akunowa. Koma ngakhale zili chomwechi, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraeli.
3 So now let us make a covenant before our God to send away all the foreign wives and their children, according to the counsel of my lord and of those who tremble at the command of our God. Let it be done according to the Law.
Tsopano tiyeni tichite naye pangano Mulungu wathu, kuti tichotse akazi onsewa ndi ana awo, potsata malangizo a inu mbuye wanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Lolani kuti zichitike motsatira malamulo.
4 Get up, for this matter is your responsibility, and we will support you. Be strong and take action!”
Tsono dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu. Ife tikuthandizani. Limbani mtima ndipo gwirani ntchitoyi.”
5 So Ezra got up and made the leading priests, Levites, and all Israel take an oath to do what had been said. And they took the oath.
Choncho Ezara anayimirira ndipo analumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraeli onse, kuti adzachitedi monga Sekaniya ananenera. Tsono onse analumbira.
6 Then Ezra withdrew from before the house of God and walked to the chamber of Jehohanan son of Eliashib. And while he stayed there, he ate no food and drank no water, because he was mourning over the unfaithfulness of the exiles.
Ezara anachoka ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu. Anatandala kumeneko usiku wonse ndipo sanadye chakudya kapena kumwa madzi popeza ankalira chifukwa cha kusankhulupirika kwa anthu obwera ku ukapolo.
7 And a proclamation was issued throughout Judah and Jerusalem that all the exiles should gather at Jerusalem.
Tsono anthu analengeza mʼdziko lonse la Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Yerusalemu kwa onse ochokera ku ukapolo aja kuti asonkhane ku Yerusalemu.
8 Whoever failed to appear within three days would forfeit all his property, according to the counsel of the leaders and elders, and would himself be expelled from the assembly of the exiles.
Ananena kuti wina aliyense amene saonekera pakutha pa masiku atatu, adzalandidwa katundu wake, potsata malangizo a nduna ndi akuluakulu, ndipo adzachotsedwa mʼgulu la anthu obwerako ku ukapolo.
9 So within the three days, all the men of Judah and Benjamin assembled in Jerusalem, and on the twentieth day of the ninth month, all the people sat in the square at the house of God, trembling regarding this matter and because of the heavy rain.
Choncho anthu onse a mʼdziko la Yuda ndi a mʼdziko la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onse anakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu akunjenjemera chifukwa cha mvula yambiri imene inagwa.
10 Then Ezra the priest stood up and said to them, “You have been unfaithful by marrying foreign women, adding to the guilt of Israel.
Ndipo wansembe Ezara anayimirira nawuza anthuwo kuti, “Inu mwachimwa pomakwatira akazi achikunja ndi kumawonjezera pa tchimo la Aisraeli.
11 Now, therefore, make a confession to the LORD, the God of your fathers, and do His will. Separate yourselves from the people of the land and from your foreign wives.”
Tsopano lapani kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu ndi kuchita zimene akufuna. Dzipatuleni kwa anthu a mayiko enawa ndi kwa akazi achikunjawa.”
12 And the whole assembly responded in a loud voice: “Truly we must do as you say!
Gulu lonse la anthu linayankha ndi mawu ofuwula kuti, “Nʼzoona! Tichita monga mwaneneramu.
13 But there are many people here, and it is the rainy season. We are not able to stay out in the open. Nor is this the work of one or two days, for we have transgressed greatly in this matter.
Koma pano pali anthu ambiri ndiponso mvula ikugwa kwambiri, choncho sitingakayime panja. Ndiponso ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena awiri, chifukwa tachimwa kwambiri pa zimene tachitazi.
14 Let our leaders represent the whole assembly. Then let everyone in our towns who has married a foreign woman come at an appointed time, together with the elders and judges of each town, until the fierce anger of our God in this matter is turned away from us.”
Tsono mulole kuti atsogoleri athu ayimirire mʼmalo mwa anthu onse. Aliyense wa mʼmizinda yathu amene anakwatira mkazi wachikunja abwere pa nthawi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akuluakulu ndi oweruza a mzindawo. Choncho mkwiyo wa Mulungu wathu udzatichoka.”
15 (Only Jonathan son of Asahel and Jahzeiah son of Tikvah, supported by Meshullam and Shabbethai the Levite, opposed this plan.)
Koma Yonatani yekha mwana wa Asaheli ndi Yahazieli mwana wa Tikiva ndiwo anatsutsapo pa zimenezi. Tsono Mesulamu ndi Mlevi Sebetai anawayikira kumbuyo.
16 So the exiles did as proposed. Ezra the priest selected men who were family heads, each of them identified by name, to represent their families. On the first day of the tenth month they launched the investigation,
Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja anachita zimene zimafunika. Ndipo wansembe Ezara anasankha amuna amene anali atsogoleri a mabanja potsata mafuko awo ndipo onsewo analembedwa mayina awo. Tsiku loyamba la mwezi wa khumi anayambapo kuyifufuza nkhani imeneyi.
17 and by the first day of the first month they had dealt with all the men who had married foreign women.
Ndipo pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba anali atathana nawo anthu amene anakwatira akazi achilendo aja.
18 Among the descendants of the priests who had married foreign women were found these descendants of Jeshua son of Jozadak and his brothers: Maaseiah, Eliezer, Jarib, and Gedaliah.
Nawu mʼndandanda wa ansembe amene anakwatira akazi achikunja: Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali awa: Maaseiya, Eliezara, Yaribu ndi Gedaliya.
19 They pledged to send their wives away, and for their guilt they presented a ram from the flock as a guilt offering.
Iwo anatsimikiza zochotsa akazi awo ndipo chifukwa cha kulakwa kwawo aliyense anapereka nkhosa yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo.
20 From the descendants of Immer: Hanani and Zebadiah.
Pa banja la Imeri panali awa: Hanani ndi Zebadiya.
21 From the descendants of Harim: Maaseiah, Elijah, Shemaiah, Jehiel, and Uzziah.
Pa banja la Harimu panali awa: Maseya, Eliya, Semaya, Yehieli ndi Uziya.
22 From the descendants of Pashhur: Elioenai, Maaseiah, Ishmael, Nethanel, Jozabad, and Elasah.
Pa banja la Pasuri panali awa: Eliyoenai, Maseya, Ismaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa.
23 Among the Levites: Jozabad, Shimei, Kelaiah (that is, Kelita), Pethahiah, Judah, and Eliezer.
Pakati pa Alevi panali: Yozabadi, Simei, Kelaya (ndiye kuti, Kelita). Petaya, Yuda ndi Eliezara.
24 From the singers: Eliashib. From the gatekeepers: Shallum, Telem, and Uri.
Pakati pa oyimba nyimbo panali Eliyasibu. Ochokera kwa alonda a zipata: Salumu, Telemu ndi Uri.
25 And among the other Israelites, from the descendants of Parosh: Ramiah, Izziah, Malchijah, Mijamin, Eleazar, Malchijah, and Benaiah.
Ochokera pakati pa Aisraeli ena: a fuko la Parosi anali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eliezara, ndi Benaya.
26 From the descendants of Elam: Mattaniah, Zechariah, Jehiel, Abdi, Jeremoth, and Elijah.
A fuko la Elamu anali Mataniya, Zekariya, Yehieli, Abidi, Yeremoti ndi Eliya.
27 From the descendants of Zattu: Elioenai, Eliashib, Mattaniah, Jeremoth, Zabad, and Aziza.
A fuko la Zatu anali Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza.
28 From the descendants of Bebai: Jehohanan, Hananiah, Zabbai, and Athlai.
A fuko la Bebai anali Yehohanani, Hananiya, Zabayi ndi Atilayi.
29 From the descendants of Bani: Meshullam, Malluch, Adaiah, Jashub, Sheal, and Jeremoth.
A fuko la Bani anali Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubu, Seali ndi Yeremoti.
30 From the descendants of Pahath-moab: Adna, Chelal, Benaiah, Maaseiah, Mattaniah, Bezalel, Binnui, and Manasseh.
A fuko la Pahati-Mowabu anali Adina, Kelali, Benaya, Maseya, Mataniya, Bezaleli, Binuyi ndi Manase.
31 From the descendants of Harim: Eliezer, Isshijah, Malchijah, Shemaiah, Shimeon,
A fuko la Harimu anali Eliezara, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni,
32 Benjamin, Malluch, and Shemariah.
Benjamini, Maluki ndi Semariya.
33 From the descendants of Hashum: Mattenai, Mattattah, Zabad, Eliphelet, Jeremai, Manasseh, and Shimei.
A fuko la Hasumu anali Mataneyi, Matata, Zabadi, Elifeleti, Yeremayi, Manase ndi Simei.
34 From the descendants of Bani: Maadai, Amram, Uel,
A fuko la Bani anali Madai, Amramu, Uweli,
35 Benaiah, Bedeiah, Cheluhi,
Benaya, Bediya, Keluhi,
36 Vaniah, Meremoth, Eliashib,
Vaniya, Meremoti, Eliyasibu,
37 Mattaniah, Mattenai, and Jaasu.
Mataniya, Matenayi ndi Yasu.
38 From the descendants of Binnui: Shimei,
A fuko la Binuyi anali Simei,
39 Shelemiah, Nathan, Adaiah,
Selemiya, Natani, Adaya,
40 Machnadebai, Shashai, Sharai,
Makinadebayi, Sasai, Sarai,
41 Azarel, Shelemiah, Shemariah,
Azaleli, Selemiya, Semariya,
42 Shallum, Amariah, and Joseph.
Salumu, Amariya ndi Yosefe.
43 And from the descendants of Nebo: Jeiel, Mattithiah, Zabad, Zebina, Jaddai, Joel, and Benaiah.
A fuko la Nebo anali Yeiyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya.
44 All these men had married foreign women, and some of them had children by these wives.
Onsewa anakwatira akazi achilendo. Tsono anawasudzula akaziwo ndi kuwatumiza kwawo pamodzi ndi ana awo.

< Ezra 10 >