< 1 Korinterne 10 >
1 Thi jeg vil ikke, Brødre, at I skulle være uvidende om, at vore Fædre vare alle under Skyen og gik alle igennem Havet
Pakuti sindikufuna kuti inu mukhale osadziwa zenizeni, abale, kuti makolo athu anatsogozedwa ndi mtambo ndikuti onse anawoloka nyanja.
2 og bleve alle døbte til Moses i Skyen og i Havet
Ndipo onse anabatizidwa mwa Mose mu mtambo ndi mʼnyanja.
3 og spiste alle den samme aandelige Mad
Onse anadya chakudya chimodzi chauzimu
4 og drak alle den samme aandelige Drik; thi de drak af en aandelig Klippe, som fulgte med; men Klippen var Kristus.
ndipo anamwa chakumwa chimodzi chauzimu; popeza anamwa kuchokera mʼthanthwe lomwe anayenda nalo, ndipo thanthwe limeneli linali Khristu.
5 Alligevel fandt Gud ikke Behag i de fleste af dem; thi de bleve slagne ned i Ørkenen.
Ngakhale zinali choncho, Mulungu sanakondwere ndi ambiri a iwo, motero ambiri mwa iwo anafera mʼchipululu.
6 Men disse Ting skete som Forbilleder for os, for at vi ikke skulle begære, hvad ondt er, saaledes som hine begærede.
Tsono zinthu izi zinachitika kuti zikhale chitsanzo, kuti ife tisayike mitima yathu pa zinthu zoyipa monga anachitira makolo athuwo.
7 Bliver ej heller Afgudsdyrkere som nogle af dem, ligesom der er skrevet: „Folket satte sig ned at spise og drikke, og de stode op at lege.‟
Musakhale anthu opembedza mafano, monga analili ena mwa iwo. Pakuti zalembedwa kuti, “Anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.”
8 Lader os ej heller bedrive Utugt, som nogle af dem bedreve Utugt, og der faldt paa een Dag tre og tyve Tusinde.
Tisachite chigololo monga ena mwa iwo anachitira ndipo tsiku limodzi anafapo anthu 23,000.
9 Lader os ej heller friste Herren, som nogle af dem fristede ham og bleve ødelagte af Slanger.
Tisamuyese Khristu, monga ena mwa iwo anachitira ndipo anaphedwa ndi njoka.
10 Knurrer ej heller, som nogle af dem knurrede og bleve ødelagte af Ødelæggeren.
Ndipo osamawiringula, monga ena mwa iwo anachitira naphedwa ndi mngelo wowononga.
11 Men dette skete dem forbilledligt, men det blev skrevet til Advarsel for os, til hvem Tidernes Ende er kommen. (aiōn )
Zinthu izi zinawachitikira kuti zikhale chitsanzo ndipo zinalembedwa kuti zikhale chenjezo kwa ife, amene tiyandikira nthawi ya kutha kwa zonse. (aiōn )
12 Derfor den, som tykkes at staa, se til, at han ikke falder!
Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe!
13 Der er ikke kommet andre end menneskelige Fristelser over eder, og trofast er Gud, som ikke vil tillade, at I fristes over Evne, men som sammen med Fristelsen vil skabe ogsaa Udgangen af den, for at I maa kunne udholde den.
Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.
14 Derfor, mine elskede, flyr fra Afgudsdyrkelsen!
Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano.
15 Jeg taler som til forstandige; dømmer selv, hvad jeg siger.
Ndikuyankhula kwa a anthu anzeru zawo, nokha muweruze pa zimene ndikunenazi.
16 Velsignelsens Kalk, som vi velsigne, er den ikke Samfund med Kristi Blod? det Brød, som vi bryde, er det ikke Samfund med Kristi Legeme?
Pamene tidalitsa chikho cha Mgonero wa Ambuye, mothokoza Mulungu, kodi sitikugawana magazi a Khristu? Nanga buledi amene timanyemayo, kodi sitikugawana thupi la Khristu?
17 Fordi der er eet Brød, ere vi mange eet Legeme; thi vi faa alle Del i det ene Brød.
Pakuti buledi ndi mmodzi yekha, ifenso ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, popeza tonse timagawana buledi mmodzi yemweyo.
18 Ser til Israel efter Kødet; have de, som spise Ofrene, ikke Samfund med Alteret?
Taganizirani zimene amachita Aisraeli. Kodi onse amene amadya zoperekedwa nsembe, samachita nawo miyambo ya pa guwapo?
19 Hvad siger jeg da? At Afgudsofferkød er noget? eller at en Afgud er noget?
Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse?
20 Nej! men hvad Hedningerne ofre, ofre de til onde Aander og ikke til Gud; men jeg vil ikke, at I skulle faa Samfund med de onde Aander.
Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo.
21 I kunne ikke drikke Herrens Kalk og onde Aanders Kalk; I kunne ikke være delagtige i Herrens Bord og i onde Aanders Bord.
Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda.
22 Eller skulle vi vække Herrens Nidkærhed? Mon vi ere stærkere end han?
Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?
23 Alt er tilladt, men ikke alt er gavnligt; alt er tilladt, men ikke alt opbygger.
Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza.
24 Ingen søge sit eget, men Næstens!
Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.
25 Alt, hvad der sælges i Slagterbod, spiser det, uden at undersøge noget af Samvittigheds-Hensyn;
Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu.
26 thi Herrens er Jorden og dens Fylde.
Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”
27 Dersom nogen af de vantro indbyder eder, og I ville gaa derhen, da spiser alt det, som sættes for eder, uden at undersøge noget af Samvittigheds-Hensyn.
Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu.
28 Men dersom nogen siger til eder: „Dette er Offerkød, ‟ da lad være at spise for hans Skyld, som gav det til Kende, og for Samvittighedens Skyld.
Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima.
29 Samvittigheden siger jeg, ikke ens egen, men den andens; thi hvorfor skal min Frihed dømmes af en anden Samvittighed?
Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina?
30 Dersom jeg nyder det med Taksigelse, hvorfor hører jeg da ilde for det, som jeg takker for?
Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?
31 Hvad enten I derfor spise eller drikke, eller hvad I gøre, da gører alt til Guds Ære!
Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
32 Værer uden Anstød baade for Jøder og Grækere og for Guds Menighed,
Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu.
33 ligesom ogsaa jeg i alt stræber at tækkes alle, idet jeg ikke søger, hvad der gavner mig selv, men hvad der gavner de mange, for at de kunne frelses.
Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.