< 耶利米書 9 >
1 恨不得我的頭髮變成水源,我的眼化為淚泉,好能日夜哭泣我被殺死的女兒──人民!
Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi, ndi maso anga ngati kasupe wa misozi! Ndikanalira usana ndi usiku kulirira anthu anga amene aphedwa.
2 誰能在o石我找一個旅棧,叫我好離開我的人民,離他們而遠去﹖因為都是些亂之徒,是一群反叛;
Ndani adzandipatsa malo ogona mʼchipululu kuti ndiwasiye anthu anga ndi kuwachokera kupita kutali; pakuti onse ndi achigololo, ndiponso gulu la anthu onyenga.
3 他們彎起像弓的舌頭,使 在地上得勢的,是虛偽而不是誠實,因為他們變本加厲作惡,全不理睬我──上主的斷語。
“Amapinda lilime lawo ngati uta. Mʼdzikomo mwadzaza ndi mabodza okhaokha osati zoonadi. Amapitirirabe kuchita zoyipa; ndipo sandidziwa Ine.” Akutero Yehova.
4 你們應各自提防自己的近人,不要信任弟兄,因為所有的弟兄都愛好欺詐,一般的近人都好說讒言;
“Aliyense achenjere ndi abwenzi ake; asadalire ngakhale abale ake. Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu. Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
5 人都欺騙自己的近人,不講實話,使自己的舌頭慣於說謊,謁力行惡,
Aliyense amamunamiza mʼbale wake ndipo palibe amene amayankhula choonadi. Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza; amalimbika kuchita machimo.
6 不願悔悟,卻強暴上又加強暴,欺詐上又加欺詐,全不理睬我──上主的斷語。
Iwe wakhalira mʼchinyengo ndipo ukukana kundidziwa Ine,” akutero Yehova.
7 為此萬軍的上主這樣說:「看,我要將他們淨化,提煉;否則,我將怎樣處理我的女兒──人民──的邪惡﹖
Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa. Kodi ndingachite nawonso bwanji chifukwa cha machimo awo?
8 他們的舌頭像毒箭,好出詐言;嘴上對鄰友說話溫和,心中卻設計陷害。
Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa; limayankhula zachinyengo. Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake, koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
9 為這些事我豈能不懲罰﹖──上主的斷語──像這樣的一個民族,我豈能不圖報復﹖
Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi? akutero Yehova. ‘Kodi ndisawulipsire mtundu wotere wa anthu?’”
10 我要為群山號咷痛哭,為原野高唱哀歌,因為全都被焚毀,沒有人往來,再聽不到牲畜的聲音;自天空的飛鳥到地上的走獸,都逃去無蹤。
Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu. Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako, ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe. Mbalame zamlengalenga zathawa ndipo nyama zakuthengo zachokako.
11 我要使耶路撒冷成為廢壚,成為豺狼的巢穴;使猶大的城市荒涼,無人居住。
Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja, malo okhalamo ankhandwe; ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”
12 誰夠聰明,明白這事﹖上主親口吩咐誰公佈這事﹖「為什麼像這地方遭受毀滅,荒蕪得有如無人經過的曠野﹖」
Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”
13 上主說:因為他們離棄了我給他們立的法律,沒有聽從我的聲音,沒有按照法律而行;
Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala.
14 反而去順從自己頑固的心,追隨祖先教給他們的巴耳神。
Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.”
15 為此萬軍的上主,以色列的天主這樣說:看,我必使這人民吃毒艾,飲毒水;
Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu.
16 使他們流離到他們和他們祖先素不相識的民族中;派刀劍追擊他們,直至將他們完全消滅。
Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”
17 萬軍的上主這樣說:你們應該明白,快召哀悼的婦女來,派人去叫擅長哭泣的女人來,
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere; itanani akazi odziwa kulira bwino.”
18 叫她們迅速前來,我們啼哭,使我們的眼睛流下眼淚,使我們的睫毛湧出睙水,
Anthu akuti, “Abwere mofulumira kuti adzatilire mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.
19 因為從熙雍那裏可以聽到哭聲:我們怎樣崩潰了,受了許多多大的恥辱! 竟要離開本國,拋棄我們的家園!
Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti, ‘Aa! Ife tawonongeka! Tachita manyazi kwambiri! Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’”
20 妳們婦女! 都應聽清上主的話,親耳聆聽衪口授的言詞;教妳們的女兒痛哭,彼此互相學唱哀歌:
Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova; tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova. Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni; aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
21 因為死亡已從我們的窗戶爬進來,進入了我們的宮殿,殲滅了街上的孩童,和廣場上的青年。
Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa; yapha ana athu mʼmisewu, ndi achinyamata athu mʼmabwalo.
22 你應這樣說──上主的斷語──人的屍體僵臥著,好像在田野裏的糞堆;又像遺留在收割者後面無人拾取的麥束。
Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti, “‘Mitembo ya anthu idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda, ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola, popanda munthu woyitola.’”
23 上主這樣說:「智者不應誇耀自己的智慧,力士不應誇耀自己的力量,富人不應誇耀自己的財富。
Yehova akuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake, kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,
24 凡要誇耀的,只應該在「知道和認識我」這件事誇耀,因為在地上是我,上主,施行仁慈、公道和正義,因為我喜愛這樣事──上主的斷語。
koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi: kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa, kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo, chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi. Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,” akutero Yehova.
25 看,時日將到──上主的斷語──我要懲罰所有受過割損而仍存有包皮的人,
“Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe.
26 即埃及、猶大、厄東、阿孟子民、摩阿布和所有住在曠野剃除鬚髮的人,因為這一切民族都未受過割損,至於以色列全家卻是未受過內心的割損」。
Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”