< Chivumbulutso 15 >
1 Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu.
Καὶ εἶδον ἄλλο σημεῖον ἐν τῷ οὐρανῷ μέγα καὶ θαυμαστόν, ἀγγέλους ἑπτὰ ἔχοντας πληγὰς ἑπτὰ τὰς ἐσχάτας, ὅτι ἐν αὐταῖς ἐτελέσθη ὁ θυμὸς τοῦ θεοῦ.
2 Ndipo ndinaona chimene chinaoneka ngati nyanja yonyezimira yosakaniza ndi moto, ndipo pambali pa nyanjayo panayima amene anagonjetsa chirombo chija ndi fano lake, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo ananyamula azeze amene Mulungu anawapatsa.
Καὶ εἶδον ὡς θάλασσαν ὑαλίνην μεμιγμένην πυρὶ καὶ τοὺς νικῶντας ἐκ τοῦ θηρίου καὶ ἐκ τῆς εἰκόνος αὐτοῦ καὶ ἐκ τοῦ (χαράγματος τοῦ ἐκ τοῦ *K*) ἀριθμοῦ τοῦ ὀνόματος αὐτοῦ ἑστῶτας ἐπὶ τὴν θάλασσαν τὴν ὑαλίνην ἔχοντας κιθάρας τοῦ θεοῦ.
3 Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati, “Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona, Mfumu ya mitundu yonse.
καὶ ᾄδουσιν τὴν ᾠδὴν Μωϋσέως τοῦ δούλου τοῦ θεοῦ καὶ τὴν ᾠδὴν τοῦ ἀρνίου λέγοντες· μεγάλα καὶ θαυμαστὰ τὰ ἔργα σου, κύριε ὁ θεὸς ὁ παντοκράτωρ. δίκαιαι καὶ ἀληθιναὶ αἱ ὁδοί σου, ὁ βασιλεὺς τῶν (ἐθνῶν. *N(K)(O)*)
4 Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani, ndi kulemekeza dzina lanu? Pakuti Inu nokha ndiye woyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzapembedza pamaso panu, pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”
τίς οὐ μὴ φοβηθῇ (σε, *k*) κύριε, καὶ (δοξάσει *N(k)O*) τὸ ὄνομά σου; ὅτι μόνος (ὅσιος, *NK(o)*) ὅτι πάντα τὰ ἔθνη ἥξουσιν καὶ προσκυνήσουσιν ἐνώπιόν σου, ὅτι τὰ δικαιώματά σου ἐφανερώθησαν.
5 Zitatha izi, ndinaona kumwamba Nyumba ya Mulungu imene ndi Tenti ya Umboni, atatsekula.
Καὶ μετὰ ταῦτα εἶδον καὶ (ἰδού *K*) ἠνοίγη ὁ ναὸς τῆς σκηνῆς τοῦ μαρτυρίου ἐν τῷ οὐρανῷ.
6 Mʼnyumbamo munatuluka angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri. Angelowo anavala nsalu zoyera bwino zonyezimira ndi malamba agolide pa zifuwa zawo.
καὶ ἐξῆλθον οἱ ἑπτὰ ἄγγελοι οἱ ἔχοντες τὰς ἑπτὰ πληγὰς ἐκ τοῦ ναοῦ (οἳ ἦσαν *o*) ἐνδεδυμένοι (λίνον *NK(O)*) καθαρὸν (καὶ *k*) λαμπρὸν καὶ περιεζωσμένοι περὶ τὰ στήθη ζώνας χρυσᾶς.
7 Ndipo kenaka chimodzi cha zamoyo zinayi zija chinapereka kwa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya. (aiōn )
καὶ ἓν ἐκ τῶν τεσσάρων ζῴων ἔδωκεν τοῖς ἑπτὰ ἀγγέλοις ἑπτὰ φιάλας χρυσᾶς γεμούσας τοῦ θυμοῦ τοῦ θεοῦ τοῦ ζῶντος εἰς τοὺς αἰῶνας τῶν αἰώνων. (aiōn )
8 Ndipo Nyumba ya Mulungu inadzaza ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake, ndipo panalibe yemwe akanalowa mʼNyumbayo mpaka miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri aja itatha.
καὶ ἐγεμίσθη ὁ ναὸς καπνοῦ ἐκ τῆς δόξης τοῦ θεοῦ καὶ ἐκ τῆς δυνάμεως αὐτοῦ, καὶ οὐδεὶς ἐδύνατο εἰσελθεῖν εἰς τὸν ναὸν ἄχρι τελεσθῶσιν αἱ ἑπτὰ πληγαὶ τῶν ἑπτὰ ἀγγέλων.