< Masalimo 95 >
1 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe, tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu
2 Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.
3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu, mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.
4 Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi, ndipo msonga za mapiri ndi zake.
5 Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye, ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.
6 Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
7 pakuti Iye ndiye Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za mʼdzanja lake. Lero ngati inu mumva mawu ake,
8 musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba, monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.
9 Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa, ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.
10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo; ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera ndipo sanadziwe njira zanga.”
11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti, “Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”