< Masalimo 150 >

1 Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.
Lover Gud i hans Helligdom, lover ham i hans Vældes udstrakte Befæstning!
2 Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu; mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
Lover ham for hans vældige Gerninger, lover ham efter hans store Magt!
3 Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.
Lover ham med Basuns Klang, lover ham med Psalter og Harpe!
4 Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina, mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.
Lover ham med Tromme og Dans, lover ham med Strenge og Fløjte!
5 Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga, mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.
Lover ham med lydende Cymbler, lover ham med klingende Cymbler!
6 Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.
Alt det, som har Aande, love Herren! Halleluja!

< Masalimo 150 >