< Miyambo 3 >
1 Mwana wanga, usayiwale malangizo anga, mtima wako usunge malamulo anga.
υἱέ ἐμῶν νομίμων μὴ ἐπιλανθάνου τὰ δὲ ῥήματά μου τηρείτω σὴ καρδία
2 Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka ndipo udzakhala pa mtendere.
μῆκος γὰρ βίου καὶ ἔτη ζωῆς καὶ εἰρήνην προσθήσουσίν σοι
3 Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako.
ἐλεημοσύναι καὶ πίστεις μὴ ἐκλιπέτωσάν σε ἄφαψαι δὲ αὐτὰς ἐπὶ σῷ τραχήλῳ καὶ εὑρήσεις χάριν
4 Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu.
καὶ προνοοῦ καλὰ ἐνώπιον κυρίου καὶ ἀνθρώπων
5 Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
ἴσθι πεποιθὼς ἐν ὅλῃ καρδίᾳ ἐπὶ θεῷ ἐπὶ δὲ σῇ σοφίᾳ μὴ ἐπαίρου
6 Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
ἐν πάσαις ὁδοῖς σου γνώριζε αὐτήν ἵνα ὀρθοτομῇ τὰς ὁδούς σου ὁ δὲ πούς σου οὐ μὴ προσκόπτῃ
7 Usamadzione ngati wa nzeru. Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa.
μὴ ἴσθι φρόνιμος παρὰ σεαυτῷ φοβοῦ δὲ τὸν θεὸν καὶ ἔκκλινε ἀπὸ παντὸς κακοῦ
8 Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino ndi mafupa ako adzakhala olimba.
τότε ἴασις ἔσται τῷ σώματί σου καὶ ἐπιμέλεια τοῖς ὀστέοις σου
9 Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.
τίμα τὸν κύριον ἀπὸ σῶν δικαίων πόνων καὶ ἀπάρχου αὐτῷ ἀπὸ σῶν καρπῶν δικαιοσύνης
10 Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.
ἵνα πίμπληται τὰ ταμίειά σου πλησμονῆς σίτου οἴνῳ δὲ αἱ ληνοί σου ἐκβλύζωσιν
11 Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova, ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.
υἱέ μὴ ὀλιγώρει παιδείας κυρίου μηδὲ ἐκλύου ὑπ’ αὐτοῦ ἐλεγχόμενος
12 Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda, monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.
ὃν γὰρ ἀγαπᾷ κύριος παιδεύει μαστιγοῖ δὲ πάντα υἱὸν ὃν παραδέχεται
13 Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,
μακάριος ἄνθρωπος ὃς εὗρεν σοφίαν καὶ θνητὸς ὃς εἶδεν φρόνησιν
14 pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide.
κρεῖττον γὰρ αὐτὴν ἐμπορεύεσθαι ἢ χρυσίου καὶ ἀργυρίου θησαυρούς
15 Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.
τιμιωτέρα δέ ἐστιν λίθων πολυτελῶν οὐκ ἀντιτάξεται αὐτῇ οὐδὲν πονηρόν εὔγνωστός ἐστιν πᾶσιν τοῖς ἐγγίζουσιν αὐτῇ πᾶν δὲ τίμιον οὐκ ἄξιον αὐτῆς ἐστιν
16 Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.
μῆκος γὰρ βίου καὶ ἔτη ζωῆς ἐν τῇ δεξιᾷ αὐτῆς ἐν δὲ τῇ ἀριστερᾷ αὐτῆς πλοῦτος καὶ δόξα ἐκ τοῦ στόματος αὐτῆς ἐκπορεύεται δικαιοσύνη νόμον δὲ καὶ ἔλεον ἐπὶ γλώσσης φορεῖ
17 Njira zake ndi njira zosangalatsa, ndipo mu njira zake zonse muli mtendere.
αἱ ὁδοὶ αὐτῆς ὁδοὶ καλαί καὶ πάντες οἱ τρίβοι αὐτῆς ἐν εἰρήνῃ
18 Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa; wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri.
ξύλον ζωῆς ἐστι πᾶσι τοῖς ἀντεχομένοις αὐτῆς καὶ τοῖς ἐπερειδομένοις ἐπ’ αὐτὴν ὡς ἐπὶ κύριον ἀσφαλής
19 Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru. Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba.
ὁ θεὸς τῇ σοφίᾳ ἐθεμελίωσεν τὴν γῆν ἡτοίμασεν δὲ οὐρανοὺς ἐν φρονήσει
20 Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka ndiponso mitambo inagwetsa mvula.
ἐν αἰσθήσει ἄβυσσοι ἐρράγησαν νέφη δὲ ἐρρύησαν δρόσους
21 Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino. Zimenezi zisakuchokere.
υἱέ μὴ παραρρυῇς τήρησον δὲ ἐμὴν βουλὴν καὶ ἔννοιαν
22 Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wosangalatsa ndi wabwino ngati mkanda wa mʼkhosi.
ἵνα ζήσῃ ἡ ψυχή σου καὶ χάρις ᾖ περὶ σῷ τραχήλῳ ἔσται δὲ ἴασις ταῖς σαρξί σου καὶ ἐπιμέλεια τοῖς σοῖς ὀστέοις
23 Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu, ndipo phazi lako silidzapunthwa;
ἵνα πορεύῃ πεποιθὼς ἐν εἰρήνῃ πάσας τὰς ὁδούς σου ὁ δὲ πούς σου οὐ μὴ προσκόψῃ
24 pamene ugona pansi, sudzachita mantha; ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma.
ἐὰν γὰρ κάθῃ ἄφοβος ἔσῃ ἐὰν δὲ καθεύδῃς ἡδέως ὑπνώσεις
25 Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi kapena chiwonongeko chimene chidzagwera anthu oyipa,
καὶ οὐ φοβηθήσῃ πτόησιν ἐπελθοῦσαν οὐδὲ ὁρμὰς ἀσεβῶν ἐπερχομένας
26 pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha.
ὁ γὰρ κύριος ἔσται ἐπὶ πασῶν ὁδῶν σου καὶ ἐρείσει σὸν πόδα ἵνα μὴ σαλευθῇς
27 Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino, pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi.
μὴ ἀπόσχῃ εὖ ποιεῖν ἐνδεῆ ἡνίκα ἂν ἔχῃ ἡ χείρ σου βοηθεῖν
28 Usanene kwa mnansi wako kuti, “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa” pamene uli nazo tsopano.
μὴ εἴπης ἐπανελθὼν ἐπάνηκε καὶ αὔριον δώσω δυνατοῦ σου ὄντος εὖ ποιεῖν οὐ γὰρ οἶδας τί τέξεται ἡ ἐπιοῦσα
29 Usamukonzere chiwembu mnansi wako, amene anakhala nawe pafupi mokudalira.
μὴ τεκτήνῃ ἐπὶ σὸν φίλον κακὰ παροικοῦντα καὶ πεποιθότα ἐπὶ σοί
30 Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa pamene iye sanakuchitire zoyipa.
μὴ φιλεχθρήσῃς πρὸς ἄνθρωπον μάτην μή τι εἰς σὲ ἐργάσηται κακόν
31 Usachite naye nsanje munthu wachiwawa kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.
μὴ κτήσῃ κακῶν ἀνδρῶν ὀνείδη μηδὲ ζηλώσῃς τὰς ὁδοὺς αὐτῶν
32 Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa koma amayanjana nawo anthu olungama.
ἀκάθαρτος γὰρ ἔναντι κυρίου πᾶς παράνομος ἐν δὲ δικαίοις οὐ συνεδριάζει
33 Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa, koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama.
κατάρα θεοῦ ἐν οἴκοις ἀσεβῶν ἐπαύλεις δὲ δικαίων εὐλογοῦνται
34 Anthu onyoza, Iye amawanyoza, koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.
κύριος ὑπερηφάνοις ἀντιτάσσεται ταπεινοῖς δὲ δίδωσιν χάριν
35 Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi.
δόξαν σοφοὶ κληρονομήσουσιν οἱ δὲ ἀσεβεῖς ὕψωσαν ἀτιμίαν