< Numeri 26 >

1 Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni,
瘟疫之後,耶和華曉諭摩西和祭司亞倫的兒子以利亞撒說:
2 “Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.”
「你們要將以色列全會眾,按他們的宗族,凡以色列中從二十歲以外、能出去打仗的,計算總數。」
3 Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti,
摩西和祭司以利亞撒在摩押平原與耶利哥相對的約旦河邊向以色列人說:
4 “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:
「將你們中間從二十歲以外的計算總數」;是照耶和華吩咐出埃及地的摩西和以色列人的話。
5 Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi: kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki; kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu;
以色列的長子是呂便。呂便的眾子:屬哈諾的,有哈諾族;屬法路的,有法路族;
6 kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi.
屬希斯倫的,有希斯倫族;屬迦米的,有迦米族;
7 Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.
這就是呂便的各族;其中被數的,共有四萬三千七百三十名。
8 Mwana wa Palu anali Eliabu,
法路的兒子是以利押。
9 ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova.
以利押的眾子是尼母利、大坍、亞比蘭。這大坍、亞比蘭,就是從會中選召的,與可拉一黨同向耶和華爭鬧的時候也向摩西、亞倫爭鬧;
10 Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo.
地便開口吞了他們,和可拉、可拉的黨類一同死亡。那時火燒滅了二百五十個人;他們就作了警戒。
11 Koma ana a Kora sanafe nawo.
然而可拉的眾子沒有死亡。
12 Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;
按着家族,西緬的眾子:屬尼母利的,有尼母利族;屬雅憫的,有雅憫族;屬雅斤的,有雅斤族;
13 kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera; kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli.
屬謝拉的,有謝拉族;屬掃羅的,有掃羅族。
14 Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.
這就是西緬的各族,共有二萬二千二百名。
15 Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi: kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni; kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi; kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni;
按着家族,迦得的眾子:屬洗分的,有洗分族;屬哈基的,有哈基族;屬書尼的,有書尼族;
16 kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini; kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri;
屬阿斯尼的,有阿斯尼族;屬以利的,有以利族;
17 kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi; kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli.
屬亞律的,有亞律族;屬亞列利的,有亞列利族。
18 Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.
這就是迦得子孫的各族,照他們中間被數的,共有四萬零五百名。
19 Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.
猶大的兒子是珥和俄南。這珥和俄南死在迦南地。
20 Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Sela, fuko la Asera; kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi; kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera.
按着家族,猶大其餘的眾子:屬示拉的,有示拉族;屬法勒斯的,有法勒斯族;屬謝拉的,有謝拉族。
21 Zidzukulu za Perezi zinali izi: kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli.
法勒斯的兒子:屬希斯崙的,有希斯崙族;屬哈母勒的,有哈母勒族。
22 Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.
這就是猶大的各族,照他們中間被數的,共有七萬六千五百名。
23 Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Tola, fuko la Atola; kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa;
按着家族,以薩迦的眾子:屬陀拉的,有陀拉族;屬普瓦的,有普瓦族;
24 kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu. Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi.
屬雅述的,有雅述族;屬伸崙的,有伸崙族。
25 Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.
這就是以薩迦的各族,照他們中間被數的,共有六萬四千三百名。
26 Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi; kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni; kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli.
按着家族,西布倫的眾子:屬西烈的,有西烈族;屬以倫的,有以倫族;屬雅利的,有雅利族。
27 Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500.
這就是西布倫的各族,照他們中間被數的,共有六萬零五百名。
28 Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:
按着家族,約瑟的兒子有瑪拿西、以法蓮。
29 Zidzukulu za Manase: kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi); kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi.
瑪拿西的眾子:屬瑪吉的,有瑪吉族;瑪吉生基列;屬基列的,有基列族。
30 Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi; kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri; kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki;
基列的眾子:屬伊以謝的,有伊以謝族;屬希勒的,有希勒族;
31 kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli; kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu;
屬亞斯烈的,有亞斯烈族;屬示劍的,有示劍族;
32 kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida; kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi.
屬示米大的,有示米大族;屬希弗的,有希弗族。
33 (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)
希弗的兒子:西羅非哈沒兒子,只有女兒。西羅非哈女兒的名字就是瑪拉、挪阿、曷拉、密迦、得撒。
34 Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.
這就是瑪拿西的各族;他們中間被數的,共有五萬二千七百名。
35 Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi; kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela; kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri; kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani.
按着家族,以法蓮的眾子:屬書提拉的,有書提拉族;屬比結的,有比結族;屬他罕的,有他罕族。
36 Zidzukulu za Sutela zinali izi: kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani.
書提拉的眾子:屬以蘭的,有以蘭族。
37 Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo.
這就是以法蓮子孫的各族,照他們中間被數的,共有三萬二千五百名。按着家族,這都是約瑟的子孫。
38 Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Bela, fuko la Abela; kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli; kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu;
按着家族,便雅憫的眾子:屬比拉的,有比拉族;屬亞實別的,有亞實別族;屬亞希蘭的,有亞希蘭族;
39 kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu; kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu;
屬書反的,有書反族;屬戶反的,有戶反族。
40 Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi: kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi; kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani;
比拉的眾子是亞勒、乃幔。屬 亞勒 的,有亞勒族;屬乃幔的,有乃幔族。
41 Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.
按着家族,這就是便雅憫的子孫,其中被數的,共有四萬五千六百名。
42 Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu. Izi zinali zidzukulu za Dani.
按着家族,但的眾子:屬書含的,有書含族。按着家族,這就是但的各族。
43 Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.
照其中被數的,書含所有的各族,共有六萬四千四百名。
44 Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna; kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi; kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya;
按着家族,亞設的眾子:屬音拿的,有音拿族;屬亦施韋的,有亦施韋族;屬比利亞的,有比利亞族。
45 ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya: kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi; kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli;
比利亞的眾子:屬希別的,有希別族;屬瑪結的,有瑪結族。
46 (Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera)
亞設的女兒名叫西拉。
47 Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.
這就是亞設子孫的各族,照他們中間被數的,共有五萬三千四百名。
48 Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli; kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni;
按着家族,拿弗他利的眾子:屬雅薛的,有雅薛族;屬沽尼的,有沽尼族;
49 kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri; kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu.
屬耶色的,有耶色族;屬示冷的,有示冷族。
50 Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.
按着家族,這就是拿弗他利的各族;他們中間被數的,共有四萬五千四百名。
51 Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.
以色列人中被數的,共有六十萬零一千七百三十名。
52 Yehova anawuza Mose kuti,
耶和華曉諭摩西說:
53 “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo.
「你要按着人名的數目將地分給這些人為業。
54 Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa.
人多的,你要把產業多分給他們;人少的,你要把產業少分給他們;要照被數的人數,把產業分給各人。
55 Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo.
雖是這樣,還要拈鬮分地。他們要按着祖宗各支派的名字承受為業。
56 Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”
要按着所拈的鬮,看人數多,人數少,把產業分給他們。」
57 Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa: kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni; kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati; kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari.
利未人,按着他們的各族被數的:屬革順的,有革順族;屬哥轄的,有哥轄族;屬米拉利的,有米拉利族。
58 Awanso anali mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, fuko la Kora banja la Akohati, (Kohati anali abambo a Amramu.
利未的各族有立尼族、希伯倫族、瑪利族、母示族、可拉族。哥轄生暗蘭。
59 Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo.
暗蘭的妻名叫約基別,是利未女子,生在埃及。她給暗蘭生了亞倫、摩西,並他們的姊姊米利暗。
60 Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
亞倫生拿答、亞比戶、以利亞撒、以他瑪。
61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).
拿答、亞比戶在耶和華面前獻凡火的時候就死了。
62 Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.
利未人中,凡一個月以外、被數的男丁,共有二萬三千。他們本來沒有數在以色列人中;因為在以色列人中,沒有分給他們產業。
63 Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko.
這些就是被摩西和祭司以利亞撒所數的;他們在摩押平原與耶利哥相對的約旦河邊數點以色列人。
64 Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai;
但被數的人中,沒有一個是摩西和祭司亞倫從前在西奈的曠野所數的以色列人,
65 Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.
因為耶和華論到他們說:「他們必要死在曠野。」所以,除了耶孚尼的兒子迦勒和嫩的兒子約書亞以外,連一個人也沒有存留。

< Numeri 26 >