< Nahumu 3 >
1 Tsoka kwa mzinda wopha anthu, mzinda wodzaza ndi mabodza, mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo, mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse!
Woe to the bloody city! Full of lies and plunder, without end is the spoil.
2 Kulira kwa zikwapu, mkokomo wa mikombero, kufuwula kwa akavalo ndiponso phokoso la magaleta!
Hear the crack of the whip, hear the rattle of wheels. Galloping horses, jolting chariots.
3 Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo, kungʼanima kwa malupanga ndi kunyezimira kwa mikondo! Anthu ambiri ophedwa, milumilu ya anthu akufa, mitembo yosawerengeka, anthu akupunthwa pa mitemboyo.
Horsemen charging, swords flashing, spears glittering, a multitude of slain, a heap of bodies, no end to the corpses over which people stumble!
4 Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere, wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga, amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake, ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.
“Because you acted like a whore, bewitching the nations, enticing the peoples,
5 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikutsutsana nawe. Ndidzakuvula chovala chako. Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wako ndipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse.
I am against you, Nineveh” the Lord of hosts declares. “I will strip your clothes and show the nations your nakedness, and the kingdoms your shame.
6 Ndidzakuthira zonyansa, ndidzakuchititsa manyazi ndiponso kukusandutsa chinthu choseketsa.
“I will fling loathsome filth at you, and make you an object of contempt, a spectacle,
7 Onse amene adzakuona adzakuthawa ndipo adzati, ‘Ninive wasanduka bwinja, adzamulira ndani?’ Kodi ndingamupeze kuti munthu woti nʼkukutonthoza?”
so that everyone who sees you will flee from you and say: ‘Nineveh is laid waste, who will mourn for her?’
8 Kodi ndiwe wopambana Tebesi, mzinda wokhala mʼmbali mwa Nailo, wozunguliridwa ndi madzi? Mtsinjewo unali chitetezo chake, madziwo anali linga lake.
“Are you any better than Thebes, which stood on the banks of the Nile, with waters around as a rampart, whose wall was the sea of waters?
9 Mphamvu zake zinali Kusi ndi Igupto, Puti ndi Libiya anali ena mwa abwenzi ake.
Her strength was Ethiopia and Egypt. The Libyans were her helpers, and Put with its countless people.
10 Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa ndipo anapita ku ukapolo. Ana ake anawaphwanyitsa pansi mʼmisewu yonse ya mu mzindamo. Anachita maere ogawana anthu ake otchuka, ndipo anthu ake onse amphamvu anamangidwa ndi maunyolo.
Yet she was exiled and made captive. On all corners of the streets her infants were dashed to pieces. Lots were cast for her nobles, all her great ones were bound in chains.
11 Iwenso Ninive udzaledzera; udzabisala ndipo udzafunafuna malo othawirako kuopa mdani.
“You too, Nineveh, will be drunk with fear; you too will seek a place of escape from the foe.
12 Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyu yokhala ndi zipatso zoyambirira kucha; pamene agwedeza mitengoyo, nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya.
All your fortresses are fig trees with the first ripe figs; if shaken, they fall into the mouth of the eater!
13 Tayangʼana ankhondo ako, onse ali ngati akazi! Zipata za dziko lako zatsekukira adani ako; moto wapsereza mipiringidzo yake.
Your troops are weak as women before your foes; the gates of your land are wide open; your defenses burned down.
14 Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu, limbitsani chitetezo chanu! Pondani dothi, ikani mʼchikombole, konzani khoma la njerwa!
“Draw water for the siege, strengthen your forts. Go to the clay pits and tread the clay; take up the brick moulds.
15 Kumeneko moto udzakupserezani; lupanga lidzakukanthani ndipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala. Chulukanani ngati ziwala, chulukanani ngati dzombe!
There the fire will consume you, the sword will cut you down. Multiply like the locust or a swarm of grasshoppers.
16 Mwachulukitsa chiwerengero cha anthu a malonda anu mpaka kupambana nyenyezi za mlengalenga, koma iwo ngati dzombe akuwononga dziko ndipo kenaka akuwuluka nʼkuchoka.
Increase the numbers of your merchants until they are more than the stars of heaven,
17 Akalonga ako ali ngati dzombe, akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombe limene lamatirira pa khoma nthawi yozizira, koma pamene dzuwa latuluka limawuluka, ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita.
until your watchmen are locusts, and your scribes like grasshoppers, which swarm in the hedges on a cold day; but when the sun rises they fly away, no one knows where.
18 Iwe mfumu ya ku Asiriya, abusa ako agona tulo; anthu ako olemekezeka amwalira. Anthu ako amwazikira ku mapiri popanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa.
“King of Assyria: your princes slumber, your nobles sleep! Your people are scattered on the mountains with no one to gather them!
19 Palibe chimene chingachize bala lako; chilonda chako sichingapole. Aliyense amene amamva za iwe amawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako, kodi alipo amene sanazilawepo nkhanza zako zosatha?
There is no healing for your hurt, your wound is incurable. All who hear of your fate clap their hands in joy, for who has escaped your limitless cruelty?”