< Oweruza 5 >

1 “Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi:
καὶ ᾖσαν Δεββωρα καὶ Βαρακ υἱὸς Αβινεεμ ἐν τῇ ἡμέρᾳ ἐκείνῃ λέγοντες
2 “Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli; ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu, tamandani Yehova:
ἀπεκαλύφθη ἀποκάλυμμα ἐν Ισραηλ ἐν τῷ ἑκουσιασθῆναι λαὸν εὐλογεῖτε κύριον
3 “Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu! Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova, Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma.
ἀκούσατε βασιλεῖς καὶ ἐνωτίσασθε σατράπαι ἐγώ εἰμι τῷ κυρίῳ ἐγώ εἰμι ᾄσομαι ψαλῶ τῷ κυρίῳ τῷ θεῷ Ισραηλ
4 “Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri, pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu, dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka nigwetsa madzi.
κύριε ἐν τῇ ἐξόδῳ σου ἐν Σηιρ ἐν τῷ ἀπαίρειν σε ἐξ ἀγροῦ Εδωμ γῆ ἐσείσθη καὶ ὁ οὐρανὸς ἔσταξεν δρόσους καὶ αἱ νεφέλαι ἔσταξαν ὕδωρ
5 Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israeli.
ὄρη ἐσαλεύθησαν ἀπὸ προσώπου κυρίου Ελωι τοῦτο Σινα ἀπὸ προσώπου κυρίου θεοῦ Ισραηλ
6 “Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati, pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa; alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali.
ἐν ἡμέραις Σαμεγαρ υἱοῦ Αναθ ἐν ἡμέραις Ιαηλ ἐξέλιπον ὁδοὺς καὶ ἐπορεύθησαν ἀτραπούς ἐπορεύθησαν ὁδοὺς διεστραμμένας
7 Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi mpaka pamene iwe Debora unafika; unafika ngati mayi ku Israeli.
ἐξέλιπον δυνατοὶ ἐν Ισραηλ ἐξέλιπον ἕως οὗ ἀναστῇ Δεββωρα ἕως οὗ ἀναστῇ μήτηρ ἐν Ισραηλ
8 Pamene anasankha milungu ina, nkhondo inabwera ku zipata za mzinda, ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
ἐξελέξαντο θεοὺς καινούς τότε ἐπολέμησαν πόλεις ἀρχόντων θυρεὸς ἐὰν ὀφθῇ καὶ λόγχη ἐν τεσσαράκοντα χιλιάσιν ἐν Ισραηλ
9 Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli, uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu. Tamandani Yehova!
ἡ καρδία μου εἰς τὰ διατεταγμένα τῷ Ισραηλ οἱ ἑκουσιαζόμενοι ἐν λαῷ εὐλογεῖτε κύριον
10 “Inu okwera pa abulu oyera, okhala pa zishalo, ndi inu oyenda pa msewu, yankhulani.
ἐπιβεβηκότες ἐπὶ ὄνου θηλείας μεσημβρίας καθήμενοι ἐπὶ κριτηρίου καὶ πορευόμενοι ἐπὶ ὁδοὺς συνέδρων ἐφ’ ὁδῷ
11 Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta; kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana; akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli. “Choncho anthu a Yehova anasonkhana ku zipata za mzinda.
διηγεῖσθε ἀπὸ φωνῆς ἀνακρουομένων ἀνὰ μέσον ὑδρευομένων ἐκεῖ δώσουσιν δικαιοσύνας κυρίῳ δικαιοσύνας αὔξησον ἐν Ισραηλ τότε κατέβη εἰς τὰς πόλεις λαὸς κυρίου
12 Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera; tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo. Iwe Baraki! nyamuka Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’
ἐξεγείρου ἐξεγείρου Δεββωρα ἐξεγείρου ἐξεγείρου λάλησον ᾠδήν ἀνάστα Βαρακ καὶ αἰχμαλώτισον αἰχμαλωσίαν σου υἱὸς Αβινεεμ
13 “Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo; anthu a Yehova anapita kukamenyera Yehova nkhondo kulimbana ndi adani amphamvu.
τότε κατέβη κατάλειμμα τοῖς ἰσχυροῖς λαὸς κυρίου κατέβη αὐτῷ ἐν τοῖς κραταιοῖς
14 Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu; akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako. Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri, ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
ἐξ ἐμοῦ Εφραιμ ἐξερρίζωσεν αὐτοὺς ἐν τῷ Αμαληκ ὀπίσω σου Βενιαμιν ἐν τοῖς λαοῖς σου ἐν ἐμοὶ Μαχιρ κατέβησαν ἐξερευνῶντες καὶ ἀπὸ Ζαβουλων ἕλκοντες ἐν ῥάβδῳ διηγήσεως γραμματέως
15 Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora; inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki, ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira. Koma pakati pa mafuko a Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
καὶ ἀρχηγοὶ ἐν Ισσαχαρ μετὰ Δεββωρας καὶ Βαρακ οὕτως Βαρακ ἐν κοιλάσιν ἀπέστειλεν ἐν ποσὶν αὐτοῦ εἰς τὰς μερίδας Ρουβην μεγάλοι ἐξικνούμενοι καρδίαν
16 Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera zitoliro zoyitanira nkhosa? Pakati pa anthu a fuko la Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
εἰς τί ἐκάθισαν ἀνὰ μέσον τῆς διγομίας τοῦ ἀκοῦσαι συρισμοῦ ἀγγέλων εἰς διαιρέσεις Ρουβην μεγάλοι ἐξετασμοὶ καρδίας
17 Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani. Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi? Aseri anali pa gombe la Nyanja; anangokhala mʼmadooko mwawo.
Γαλααδ ἐν τῷ πέραν τοῦ Ιορδάνου ἐσκήνωσεν καὶ Δαν εἰς τί παροικεῖ πλοίοις Ασηρ ἐκάθισεν παραλίαν θαλασσῶν καὶ ἐπὶ διεξόδοις αὐτοῦ σκηνώσει
18 Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa. Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.
Ζαβουλων λαὸς ὠνείδισεν ψυχὴν αὐτοῦ εἰς θάνατον καὶ Νεφθαλι ἐπὶ ὕψη ἀγροῦ
19 “Mafumu anabwera, anachita nkhondo; mafumu Akanaani anachita nkhondo ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido, koma sanatengeko zofunkha zasiliva.
ἦλθον αὐτῶν βασιλεῖς παρετάξαντο τότε ἐπολέμησαν βασιλεῖς Χανααν ἐν Θανααχ ἐπὶ ὕδατι Μεγεδδω δῶρον ἀργυρίου οὐκ ἔλαβον
20 Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo, zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
ἐξ οὐρανοῦ παρετάξαντο οἱ ἀστέρες ἐκ τρίβων αὐτῶν παρετάξαντο μετὰ Σισαρα
21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola. Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!
χειμάρρους Κισων ἐξέσυρεν αὐτούς χειμάρρους ἀρχαίων χειμάρρους Κισων καταπατήσει αὐτὸν ψυχή μου δυνατή
22 Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu, akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.
τότε ἐνεποδίσθησαν πτέρναι ἵππου σπουδῇ ἔσπευσαν ἰσχυροὶ αὐτοῦ
23 Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’ ‘Tembererani nzika zake mwaukali, chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova, kulimbana ndi adani ake amphamvu.’
καταρᾶσθε Μηρωζ εἶπεν ἄγγελος κυρίου καταρᾶσθε ἐπικατάρατος πᾶς ὁ κατοικῶν αὐτήν ὅτι οὐκ ἤλθοσαν εἰς βοήθειαν κυρίου εἰς βοήθειαν ἐν δυνατοῖς
24 “Akhale wodala kupambana akazi onse, Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu.
εὐλογηθείη ἐν γυναιξὶν Ιαηλ γυνὴ Χαβερ τοῦ Κιναίου ἀπὸ γυναικῶν ἐν σκηναῖς εὐλογηθείη
25 Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka; anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka.
ὕδωρ ᾔτησεν γάλα ἔδωκεν ἐν λεκάνῃ ὑπερεχόντων προσήνεγκεν βούτυρον
26 Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake, anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja. Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake, ndi kumubowola mu litsipa mwake.
χεῖρα αὐτῆς ἀριστερὰν εἰς πάσσαλον ἐξέτεινεν καὶ δεξιὰν αὐτῆς εἰς σφῦραν κοπιώντων καὶ ἐσφυροκόπησεν Σισαρα διήλωσεν κεφαλὴν αὐτοῦ καὶ ἐπάταξεν διήλωσεν κρόταφον αὐτοῦ
27 Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa, anagwa; iye anagona pamenepo. Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa; pamene anagwera, pamenepo anaferapo.
ἀνὰ μέσον τῶν ποδῶν αὐτῆς κατεκυλίσθη ἔπεσεν καὶ ἐκοιμήθη ἀνὰ μέσον τῶν ποδῶν αὐτῆς κατακλιθεὶς ἔπεσεν καθὼς κατεκλίθη ἐκεῖ ἔπεσεν ἐξοδευθείς
28 “Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera; nafuwula mokweza kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika? Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’
διὰ τῆς θυρίδος παρέκυψεν μήτηρ Σισαρα ἐκτὸς τοῦ τοξικοῦ διότι ᾐσχύνθη ἅρμα αὐτοῦ διότι ἐχρόνισαν πόδες ἁρμάτων αὐτοῦ
29 Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha, ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti,
αἱ σοφαὶ ἄρχουσαι αὐτῆς ἀπεκρίθησαν πρὸς αὐτήν καὶ αὐτὴ ἀπέστρεψεν λόγους αὐτῆς ἑαυτῇ
30 ‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane; akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri. Sisera akumupatsa zofunkha: zovala zonyikidwa mu utoto, zoti ndizivala mʼkhosi zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’
οὐχ εὑρήσουσιν αὐτὸν διαμερίζοντα σκῦλα οἰκτίρμων οἰκτιρήσει εἰς κεφαλὴν ἀνδρός σκῦλα βαμμάτων τῷ Σισαρα σκῦλα βαμμάτων ποικιλίας βάμματα ποικιλτῶν αὐτά τῷ τραχήλῳ αὐτοῦ σκῦλα
31 “Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke, koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa pamene lituluka ndi mphamvu zake.” Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.
οὕτως ἀπόλοιντο πάντες οἱ ἐχθροί σου κύριε καὶ οἱ ἀγαπῶντες αὐτὸν ὡς ἔξοδος ἡλίου ἐν δυνάμει αὐτοῦ καὶ ἡσύχασεν ἡ γῆ τεσσαράκοντα ἔτη

< Oweruza 5 >