< Oweruza 20 >

1 Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dziko la Dani mpaka ku Beeriseba ndiponso ku dziko la Giliyadi ananyamuka ngati munthu mmodzi nakasonkhana pamaso pa Yehova ku Mizipa.
Tous les Israélites se mirent en mouvement, depuis Dan jusqu’à Bersabée et le pays de Galaad, et se rendirent ensemble, comme un seul homme, devant l’Eternel, à Miçpa.
2 Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse Aisraeli anali nawo pa msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo asilikali oyenda pansi 400,000 atanyamula malupanga.
Toutes les sommités du peuple, de toutes les tribus d’Israël, assistèrent à cette assemblée du peuple de Dieu, composée de quatre cent mille hommes de pied, sachant tirer l’épée.
3 Anthu a fuko la Benjamini anali atamva kuti Aisraeli apita ku Mizipa. Tsono Aisraeli anati, “Tiwuzeni, zinthu zoyipa izi zinachitika bwanji.”
Les Benjamites furent informés que les enfants d’Israël étaient montés à Miçpa. Les enfants d’Israël dirent: "Expliquez-nous comment est arrivée cette chose odieuse!"
4 Choncho Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwa uja anayankha nati, “Ine ndinapita ku Gibeya mʼdziko la Benjamini pamodzi ndi mzikazi wanga kuti tikagone kumeneko.
Alors le lévite, celui dont la femme avait été assassinée, prit la parole et dit: "J’Étais venu à Ghibea-en-Benjamin, avec ma concubine, pour y passer la nuit.
5 Usiku anthu a ku Gibeya anandiwukira, nazinga nyumba munali ine. Ankafuna kundipha ndipo anagona ndi mzikazi wanga momukakamiza mpaka anafa.
Et les habitants de Ghibea se sont levés contre moi, et ont cerné de nuit la maison où j’étais; ils avaient le projet de me tuer, et ils ont abusé de ma concubine au point qu’elle en est morte.
6 Ine ndinatenga mzikazi wangayo ndi kumudula nthulinthuli ndikuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraeli. Anthu amenewa, zedi achita chinthu chonyansa kwambiri mʼdziko lino la Israeli.
Alors j’ai pris son corps, l’ai coupé en morceaux et l’ai envoyé dans toute la campagne du territoire d’Israël; car ils avaient commis un acte honteux et criminel en Israël.
7 Ndi zimenezotu inu Aisraeli nonse; yankhulaponi mawu ndi kupereka maganizo anu.”
Vous voici, tous, enfants d’Israël; avisez ici même et prenez un parti!"
8 Anthu onse anayimirira ngati munthu mmodzi nanena kuti, “Palibe mmodzi wa ife amene apite ku nyumba kwake. Palibe amene abwerere ku nyumba kwake.
Tout le peuple se leva comme un seul homme en disant: "Aucun d’entre nous ne rentrera dans sa tente, ni ne se retirera dans sa maison!
9 Koma tsopano chimene ife tichite ndi dziko la Gibeya ndi ichi: Tidzapita kukamenyana nawo potsatira zimene maere anene.
Et maintenant, voici comment nous agirons contre Ghibea: nous procéderons par un tirage au sort,
10 Mʼmafuko onse a Aisraeli tidzasankha anthu khumi pa anthu 100 aliwonse: ndiye kuti anthu 100 pa anthu 1,000 aliwonse kapena anthu 1,000 pa anthu 10,000 aliwonse. Anthu amenewa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Geba mʼdziko la Benjamini chifukwa chochita chinthu chonyansa chotere mʼdziko la Israeli.”
et prendrons ainsi, dans toutes les tribus d’Israël, dix hommes sur cent, cent sur mille, mille sur dix mille, qui seront chargés des subsistances du peuple, tandis que celui-ci marchera sur Ghibea-en-Benjamin, pour châtier l’infamie qu’il a commise en Israël."
11 Choncho anthu a ku Israeli anasonkhana pamodzi nagwirizana chimodzi, kukalimbana ndi mzindawo.
Et tous les hommes d’Israël marchèrent ensemble contre la ville, unis comme un seul homme.
12 Mafuko a Israeli anatumiza anthu kwa fuko lonse la Benjamini kukafunsa kuti, “Kodi zoyipa zachitika pakati panuzi ndi zotani?
Les tribus d’Israël envoyèrent d’abord des hommes dans toutes les familles de Benjamin, pour leur dire: "Qu’est-ce que ce méfait qui s’est commis chez vous?
13 Tsono tikuti mutipatse anthu achabechabe a ku Gibeya kuti tiwaphe kuti tichotse chinthu choyipachi mʼdziko la Israeli.” Koma fuko la Benjamini silinafune kumvera zimene ananena Aisraeli anzawo.
Maintenant livrez-nous ces hommes indignes qui sont à Ghibea, pour que nous les mettions à mort et fassions disparaître le mal du sein d’Israël." Mais les enfants de Benjamin ne voulurent pas céder à la voix des Israélites leurs frères,
14 Mʼmalo mwake, Abenjaminiwo anatuluka mʼmizinda yawo ku Gibeya kukamenyana ndi Aisraeli.
et ils se rendirent en masse des autres villes à Ghibea, pour engager la lutte avec les enfants d’Israël.
15 Tsiku limenelo Abenjamini anasonkhanitsa kuchokera ku mizinda yawo ankhondo 26,000 amalupanga awo, osawerengera anthu ena 700 a ku Gibeya amene anasankhidwa.
Les Benjamites de ces villes, s’étant comptés, formaient alors un total de vingt-six mille hommes tirant l’épée, outre les habitants de Ghibea, qui fournirent au dénombrement sept cents hommes d’élite:
16 Mwa onsewa panali ankhondo 70 amanzere amene aliyense anali wodziwa kulasa ngakhale tsitsi limodzi ndi mwala osaphonya.
élite de toute cette armée, ces sept cents hommes étaient gauchers, et, avec la pierre de leurs frondes, visaient un cheveu sans le manquer.
17 Aisraeli, kupatula fuko la Benjamini, anasonkhanitsa anthu 400,000 a malupanga, onse odziwa bwino nkhondo.
De leur côté, les Israélites, moins Benjamin, s’étant dénombrés, comptaient quatre cent mille hommes sachant manier l’épée, tous hommes de guerre.
18 Ndipo Aisraeli ananyamuka kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu. Iwo anati, “Ndani mwa ife amene angayambe kukamenyana ndi fuko la Benjamini?” Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe.”
Ceux-ci montèrent à Béthel pour consulter le Seigneur en ces termes: "Lequel de nous doit marcher le premier au combat contre les Benjamites?" L’Eternel répondit: "Juda sera le premier."
19 Mmawa mwake Israeli ananyamuka nakamanga msasa moyangʼanana ndi Gibeya.
Les Israélites se mirent en marche le lendemain matin, et dressèrent leur camp devant Ghibea.
20 Aisraeli anapita kukachita nkhondo ndi fuko la Benjamini ndipo anandandalika ankhondo awo moyangʼanana ndi Gibeya.
Puis ils s’avancèrent pour livrer bataille aux Benjamites, et engagèrent la lutte avec eux sous les murs de Ghibea.
21 A fuko la Benjamini anatuluka ku Gibeya ndipo tsiku limenelo anapha Aisraeli 22,000 ku nkhondoko.
Mais les Benjamites se jetèrent hors de Ghibea et firent ce jour-là mordre la poussière à vingt-deux mille hommes d’Israël.
22 Koma ankhondo a Israeli analimbikitsananso mtima ndipo anasonkhanitsanso kachiwiri ankhondo awo pa malo pamene anawandandalika poyamba paja.
L’Armée israélite, sans perdre courage, se rangea de nouveau en bataille au même lieu que le premier jour.
23 Aisraeli anapita kukalira pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana ndi a fuko la Benjamini abale athu?” Yehova anayankha kuti, “Pitani mukalimbane nawo.”
Et les Israélites montèrent pleurer devant le Seigneur jusqu’au soir et le consultèrent en disant: "Dois-je engager une seconde bataille avec Benjamin mon frère?" A quoi le Seigneur répondit: "Marchez contre lui."
24 Ndipo Aisraeli anayandikiranso pafupi ndi fuko la Benjamini tsiku lachiwiri lake kuti amenyane nawo.
Les enfants d’Israël s’avancèrent donc une seconde fois contre ceux de Benjamin.
25 Pa tsiku lachiwiri lomwelo Abenjamini anatulukanso mu mzinda wa Gibeya ndipo anaphanso ankhondo 18,000. Onse amene anawaphawo anali odziwa kugwiritsa ntchito bwino malupanga.
Et ceux-ci, ayant fait de Ghibea une nouvelle sortie contre eux, ce second jour, couchèrent encore dans la poussière dix-huit mille hommes d’Israël, tous habiles à manier l’épée.
26 Tsono Aisraeli onse, gulu lonse la ankhondo, anapita ku Beteli kukalira pamaso pa Yehova. Anakhala pansi nasala zakudya tsiku lonse mpaka madzulo. Anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova.
Alors tous les Israélites et toute la population montèrent à Béthel et restèrent là, devant l’Eternel, se lamentant et jeûnant toute la journée jusqu’au soir, et ils offrirent des holocaustes et des rémunératoires à l’Eternel;
27 Bokosi la Chipangano cha Yehova linali kumeneko.
et les Israélites consultèrent l’Eternel (car l’arche d’alliance du Seigneur était là à cette époque,
28 Finehasi mwana wa Eliezara mwana wa Aaroni ndiye ankatumikira nthawi imeneyo. Tsono Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukachita nkhondo ndi mʼbale athu Abenjamini, kapena ayi?” Yehova anayankha kuti, “Pitaninso chifukwa mawa ndidzawapereka mʼmanja mwanu.”
et Phinéas, fils d’Eléazar fils d’Aaron, fonctionnait devant lui en ce même temps), et ils dirent: "Dois-je encore aller en guerre contre mon frère Benjamin, ou cesser les hostilités?" Et l’Eternel répondit: "Marchez! car demain je le mettrai en votre puissance."
29 Choncho Aisraeli anayika anthu obisalira mozungulira Gibeya.
Alors les Israélites dressèrent des embuscades tout autour de Ghibea,
30 Tsiku lachitatu anapita kukamenyana ndi Benjamini ndipo anayika ankhondo mʼmalo mwawo kuti amenyane ndi Gibeya monga anachitira poyamba.
marchèrent une troisième fois contre les Benjamites, et s’avancèrent en bon ordre contre Ghibea, comme précédemment.
31 Abenjamini anatuluka kukamenyana nawo anthuwo ndipo anapita kutali ndi mzindawo. Iwo anayamba kupha Aisraeli monga poyamba paja, kotero kuti anapha anthu pafupifupi makumi atatu. Mitembo ya ena inali mu misewu yayikulu yopita ku Beteli ndi ku Gibeya, ndipo ina inali kwina poyera.
Les Benjamites firent une sortie contre eux, ce qui les éloigna de la ville, et ils commencèrent à leur infliger des pertes comme précédemment, faisant périr sur les routes de la campagne, dont l’une conduit è Béthel, l’autre à Ghibea, environ trente hommes d’Israël.
32 Abenjamini ankanena kuti, “Tikuwagonjetsa monga poyamba.” Koma Aisraeli ankanena kuti, “Tiyeni tithawe kuti apite ku msewu chapatali ndi mzinda wawo.”
Les enfants de Benjamin se dirent: "Les voilà battus par nous comme auparavant!" Mais les enfants d’Israël s’étaient dit: "Nous allons fuir, pour les attirer hors de la ville sur les routes."
33 Choncho Aisraeli onse anachoka mʼmalo mwawo ndi kukandanda ku Baala-Tamara, ndipo Aisraeli obisalira aja anatuluka mʼmalo awo kummawa kwa Geba.
Le gros de l’armée d’Israël quitta donc sa position et alla se ranger à Baal-Tamar, tandis que les Israélites embusqués débouchaient de leur poste, de la prairie de Ghibea.
34 Aisraeli osankhidwa 10,000 ndiwo anabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibeya. Nkhondoyo inafika poyipa kwambiri mwakuti Abenjamini samadziwa kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera.
Dix mille hommes, des meilleurs guerriers d’Israël, arrivèrent ainsi à l’opposite de Ghibea, et l’attaque fut terrible; mais les Benjamites ne se doutaient pas du désastre qui les atteignait.
35 Tsono Yehova anagonjetsa Abenjamini pamaso pa Israeli motero kuti Aisraeli anapha ankhondo a Abenjamini 25,100 tsiku limenelo.
Le Seigneur fit succomber Benjamin sous les armes d’Israël, et les Israélites, ce jour-là, tuèrent à Benjamin vingt-cinq mille cent hommes, tous experts à l’épée.
36 Choncho Abenjamini anaona kuti agonjetsedwa. Paja Aisraeli anathawa fuko la Benjamini chifukwa ankadalira anthu amene anawayika kuti abisalire mzinda wa Gibeya.
Les Benjamites avaient donc jugé leurs ennemis battus; mais ceux-ci leur avaient cédé le terrain, parce qu’ils comptaient sur l’embuscade qu’ils avaient postée près de Ghibea.
37 Tsono anthu amene anabisala aja anachita changu kuwuthira nkhondo mzinda wa Gibeyawo. Ndipo anapha anthu onse a mu mzindawo ndi lupanga.
De fait, les hommes embusqués fondirent prestement sur Ghibea, se répandirent par la ville et passèrent tout au fil de l’épée.
38 Chizindikiro chimene Aisraeli anapangana ndi anthu obisalira aja chinali chakuti obisalira aja akangofukiza utsi wambiri ngati mtambo mu mzindamo,
Les hommes d’Israël étaient convenus d’un signal avec ceux de l’embuscade: celle-ci devait faire monter de la ville une masse épaisse de fumée.
39 ndiye kuti Aisraeli enawo abwerere ku nkhondo. Pa nthawiyo nʼkuti Abenjamini atayamba kale kumenya Aisraeliwo kwambiri ndi kupha pafupifupi anthu makumi atatu. Ndipo iwo ankanena kuti, “Ndithu tawapha monga poyamba paja.”
Donc, le combat engagé, les Israélites tournèrent le dos, et Benjamin commença à leur tuer du monde, environ trente hommes, persuadé qu’il les battrait comme au combat précédent.
40 Koma pamene utsi wa chizindikiro uja unayamba kukwera tolotolo mmwamba kuchoka mu mzindamo, Abenjamini anayangʼana mʼmbuyo ndipo anangoona utsi mu mzinda onse uli tolotolo kukwera mmwamba.
En ce moment, la fumée commença à s’élever de la ville en colonne épaisse; et Benjamin, en se retournant, vit toute la ville se dissiper en fumée dans les airs.
41 Kenaka Aisraeli anabwerera ndipo Abenjamini anachita mantha, chifukwa anaona kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera.
Et les hommes d’Israël firent volte-face, et ceux de Benjamin furent éperdus, voyant leur désastre imminent.
42 Choncho anathawa pamaso pa Aisraeli kudzera njira ya ku chipululu, koma nkhondo inawapeza. Ndipo anaphedwa kumeneko ndi Aisraeli amene anachokera mu mzindamo.
Et ils s’enfuirent devant ceux d’Israël dans la direction du désert, mais l’attaque les y suivit, tandis que ceux des villes les exterminaient à l’intérieur.
43 Anawazungulira Abenjaminiwo, nawathamangitsa ndi kuwagonjetseratu osawachitira chifundo mpaka ku dera la kummawa kwa Gibeya.
On cerna Benjamin, on le poursuivit à outrance, on l’écrasa à chaque halte, jusqu’à l’opposite de Ghibea à l’orient.
44 Abenjamini 18,000 olimba mtima anaphedwa.
Il périt ainsi de Benjamin dix-huit mille hommes, tous braves guerriers.
45 Koma ena anatembenuka nathawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowa Aisraeli anapha Abenjamini 5,000 mʼmisewu yayikulu. Anawapitikitsabe Abenjaminiwo mpaka kufika ku Gidomu ndi kuphanso ena 2,000.
Les autres s’enfuirent au désert, vers la Roche de Rimmon; on les écharpa sur les routes, au nombre de cinq mille hommes, et continuant la poursuite jusqu’a Ghideôm, on en tua encore deux mille.
46 Pa tsiku limenelo Abenjamini olimba mtima okhala ndi malupanga okwana 25,000 anafa.
Le total des pertes de Benjamin, en cette occurrence, fut donc de vingt-cinq mille hommes, tous braves guerriers.
47 Koma anthu 700 anabwerera ndi kuthawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni kumene anakhalako miyezi inayi.
Six cents hommes purent s’enfuir au désert, vers la Roche de Rimmon, où ils demeurèrent quatre mois.
48 Aisraeli anabwerera kukamenyana ndi Abenjamini otsala ndi kuwapha ndi lupanga kuphatikizapo ziweto ndi zonse anali nazo. Ndipo anayatsa moto mizinda yonse anayipeza.
De leur côté, les Israélites, se retournant contre la tribu de Benjamin, y passèrent au fil de l’épée la population entière des villes jusqu’au bétail, tout ce qu’ils rencontrèrent; et toutes les villes qui s’y trouvaient, ils les livrèrent aux flammes.

< Oweruza 20 >